Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 6/15 tsamba 23-28
  • Mboni Kufikira ku Malekezero Ake a Dziko Lapansi

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mboni Kufikira ku Malekezero Ake a Dziko Lapansi
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • ‘Ndi Liti Pamene Tingapite ku Thule?’
  • Kupita ku Thule
  • Vuto Lowopsa
  • Kulandiridwa Kwathu
  • Ulendo Umalizidwa
Nsanja ya Olonda—1996
w96 6/15 tsamba 23-28

Mboni Kufikira ku Malekezero Ake a Dziko Lapansi

ETAH

THULE

GODHAVN

GODTHÅB

JULIANEHÅB

ANGMAGSSALIK

THULE ndi mbali ya dzina limene lagwiritsiridwa ntchito kuyambira nthaŵi zakale kutanthauza chonulirapo chachikulu, cha malo enieni kapena cha zinthu zina. Lerolino Thule lili dzina la mudzi wina kumpoto kwenikweni kwa Greenland, chisumbu chachikulu koposa padziko lapansi. Mudziwo unatchedwa dzinalo mu 1910, pamene wofufuza malo wa ku Denmark Knud Rasmussen anaugwiritsira ntchito monga posonkhanitsira katundu kaamba ka maulendo akumadera amenewo. Ngakhale tsopano, ulendo wopita ku Thule sumangokhala ulendo wamba.

Ngakhale zili choncho, maulendo otero opita ku Thule akufunika mwamsanga. Polabadira lamulo la Yesu lakuti: ‘Khalani mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko,’ Mboni za Yehova nzofunitsitsa kubweretsa uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu kumalo ano, umodzi wa midzi yachikhalire ya anthu yakumpoto kwenikweni padziko lapansi.​—Machitidwe 1:8; Mateyu 24:14.

‘Ndi Liti Pamene Tingapite ku Thule?’

Mu 1955 Mboni ziŵiri za ku Denmark zimene zinafuna kutengamo mbali m’kulalikira ku “malekezero ake a dziko” zinafika ku Greenland. Ena anabwera pambuyo pake, ndipo m’kupita kwa nthaŵi ntchito yawo ya kulalikira inaloŵetsamo gombe la kummwera ndi kumadzulo kufika ku Melville Bay ndi pafupifupi kufika kugombe lakummawa. Koma madera akutali kwambiri monga Thule ankafikidwa kokha mwa makalata kapena telefoni.

Tsiku lina mu 1991, Bo ndi mkazi wake, Helen, atumiki aŵiri anthaŵi zonse, anaimirira pathanthwe loyang’anizana ndi Melville Bay. Akumapenya kumpoto iwo analingalira kuti, ‘Kodi ndi liti pamene tidzakhoza kuyenda mpaka ku Thule kupereka uthenga wabwino wa Ufumu kwa anthu kumeneko?’

Mu 1993, Werner mtumiki wina wanthaŵi zonse, analimbika mtima kuti adutse Melville Bay mu boti lake lokhala ndi injini lotchedwa Qaamaneq (Kuunika) la mamita asanu ndi theka. Anali atayenda kale makilomita 1,200 panyanja kuchokera ku Godthåb kufika ku dera la Upernavik. Komabe, kudutsa Melville Bay​—makilomita 400 a madzi ambiri a mu Arctic​—ndi nkhani inanso. Chigwegwecho chimatsekedwa ndi madzi oundana kwa nthaŵi yaitali pachaka. Werner anakwanitsa kudutsa chigwegwecho, ngakhale kuti injini imodzi inazima chifukwa cha madzi oundana. Ndipo anakwanitsa kuchita ntchito ya kulalikira asanabwerere.

Kupita ku Thule

Pambuyo pa ulendo umenewo, Werner anayamba kupanga makonzedwe atsopano. Anakambitsirana ndi Arne ndi Karin​—amenenso anali ndi boti la mamita asanu ndi aŵiri lokhala ndi malo anayi okhalamo kapena kugona ndipo, chofunika kwambiri, lokhala ndi ziŵiya zamakono zopimira ulendo wapanyanja​—ponena za kupanga ulendo umodzi wopita ku Thule. Mabotiwo adzakhala mogona, ndipo kukhala ndi maboti aŵiri oyendera pamodzi, sikungakhale kwangozi kwambiri kudutsa Melville Bay. Kuti afole tauni yaikulu ndi okhalamo ake 600 ndi midzi isanu ndi umodzi yokhala mu deralo, iwo anafunikira thandizo lowonjezereka. Motero anaitana Bo ndi Helen ndi Jørgen ndi Inge​—onse atumiki achidziŵitso odziŵa mayendedwe a m’dzikoli​—kuti apite nawo. Asanu a gululi amalankhulanso Chigrinilande.

Anayamba atumiza mitokoma ya mabuku ofotokoza Baibulo. Mabotiwo anadzazidwanso ndi mabuku, pamodzinso ndi zofunika zoyenera monga chakudya ndi madzi, mafuta oyendera, injini yapadera ndi boti lapulasitiki lopulumukiramo. Ndiyeno, pa August 5, 1994, pambuyo pa miyezi yambiri ya kukonzekera, gululo linakumana ndipo maboti onse aŵiri anali okonzeka ndipo odzaza katundu padoko la Ilulissat. Ulendo wopita kumpoto unayamba. Werner, Bo, ndi Helen anali m’boti laling’onolo. “Chinthu chokha chimene ukanachita ndicho kungokhala kapena kugona pamalo ako basi ndi kugwiririra chinachake,” akulemba motero Bo. Tiyeni tilondole zochitika paulendowo.

“Panali mitunda yaitali ya nyanja yabata. Tinayamba kuona zinthu zambiri zokongola kwambiri​—nyanja yong’anima pang’ono, malo okhala ndi nkhungu yochindikala, dzuŵa lowala ndi mlengalenga wa bluu, miyala yaikulu ya madzi oundana ya mapangidwe ndi maonekedwe osiyanasiyana okongola kwambiri, walrus yakuda ikuwothera dzuŵa pa mwala woyandama wa madzi oundana, gombe lokhala ndi mapiri akuda ndi madambo aang’ono​—kaonekedwe ka malowo kanali kungosinthabe.

“Inde, mbali yokondweretsa kwambiri inali kuchezera midzi ya m’mbali mwake. Nthaŵi zonse potsikira panali anthu, makamaka ana, ofuna kuona amene alendowo ali ndi kuwalandira. Tinagaŵira mabuku ofotokoza Baibulo ndi kubwereka anthu vidiyo yosonyeza gulu lathu. Ambiri anatha kuiona tisananyamuke. Ku South Upernavik, anthu angapo anabwera ndi maboti awo ku maboti athu ngakhale pamene tisanafike. Choncho madzulo onse, tinali ndi odzatichezera m’mabotiwo ndipo tinayankha mafunso ambiri a Baibulo.”

Tsopano, pambuyo pa makilomita a ulendowo 700 oyamba, maboti aŵiriwo anali okonzekera kudutsa Melville Bay.

Vuto Lowopsa

“Aliyense anakhulupirira kuti imeneyi ndiyo inali mbali yovuta kwambiri ya ulendowo. Ndipo tinafunikira kudutsa mosaima chifukwa mudzi wa Savissivik (pamene gawo liyambira ndi pamene mwinamwake tikanapeza malo okhala) unali wotsekeredwabe ndi madzi oundana.

“Chotero tinanyamuka. Popeza kunali madzi oundana ochuluka, tinapita kutali m’nyanja. Mwamwaŵi, madzi anali abata. Pamaola angapo oyamba panalibe zochitika zokondweretsa​—tikumayenda makilomita ambirimbiri panyanja. Podzafika madzulo tinaona Cape York ndipo pang’onopang’ono tinatembenukira kumpoto, kufupi ndi mtunda. Ndiyeno tinapezanso madzi oundana​—akale, ochindikala, ndipo miyala yake yomasungunuka yoyandama kufika kutali kumene maso sangafike. Tinatsatira m’mbali mwa madzi oundanawo kwa mtunda wautali, nthaŵi zina kuyenda m’tinjira tating’ono. Ndiyeno tinapeza nkhungu, mtambo wochindikala ndipo wombuŵirira, wokongola pawokha m’kuunika kwa dzuŵa lomaloŵa. Ndi mafunde! Nkhungu, mafunde, ndi madzi oundana zonse panthaŵi imodzi​—kaŵirikaŵiri chimodzi cha zimenezi nchokwanira kuyambitsa mavuto.”

Kulandiridwa Kwathu

“Pamene tinali kuyandikira Pituffik tinaloŵa m’madzi abata. Chilengedwe chinatilandira mogwira mtima: dzuŵa lili pamwamba m’thambo loti ngwee; patsogolo pathu, chigwegwe chotakata, cha madzi oŵalima, chokhala ndi mapiri ambiri opangidwa ndi madzi oundana; ndipo kutsogolo kwambiri kunaoneka chizimezime cha thanthwe la ku Dundas​—Thule wakale!” Pafupifupi makilomita 100 kutsogolonso chakumpoto, apaulendowo anafika kumene anali kupita.

Tsopano anali ofunitsitsa kuyamba kulalikira kunyumba ndi nyumba. Aŵiri a iwo anakanidwa mosapita m’mbali pakhomo lawo loyamba. “Tinakanidwa monga ngati tinali ku Denmark,” iwo anatero. “Koma ambiri anatilandira ndi mtima wonse. Anthu ake anali olingalira kwambiri ndi odziŵa zinthu. Ena ananena kuti anali atamva za ife ndipo anali okondwera kuti tafika pomalizira pake. Tinakumana ndi anthu ochititsa chidwi, monga osaka ma seal amene anapitapo ku North Pole, ndiponso anthu akumaloko, okhutira ndipo osinira okhala ndi malingaliro okayikira kutsungula kwamakono.”

Masiku angapo otsatira, onse anakhala ndi zokumana nazo zabwino. Mabuku ofotokoza Baibulo analandiridwa ndi chiyamikiro kulikonse. M’nyumba zingapo Mbonizo zinayambitsa maphunziro a Baibulo nthaŵi yomweyo. Inge akusimba za nyumba ina pamene anapeza wokondweretsedwa kuti: “Inali nyumba yoyera ndi yabwino yopanda zipinda. Masiku atatu otsatizana, tinachezera mwamuna wofatsayo amene anali kukhala mmenemo ndipo tinamkonda kwambiri. Analidi wosaka ma seal, ndi bwato lake panja pa nyumba. Anapha zimbalangondo zambiri zakumadera ozizira, ma walrus, ndiponso ma seal. Paulendo wathu womaliza, tinapemphera naye, ndipo maso ake anadzaza ndi misozi. Tsopano zonse tikuzisiya m’manja mwa Yehova ndi kuyembekezera nthaŵi ndi mpata wa kubwererako.”

Aeskimo a ku Canada amabwera ku Thule kaŵirikaŵiri. Inge akunena kuti: “Ineyo ndi Helen tinakumana ndi Aeskimo angapo ochokera ku Canada. Nkodabwitsa kuti amakambitsirana ndi anthu a ku Greenland; anthu a ku dera la Arctic akuoneka kuti amalankhula zinenero zofanana. Ngakhale kuti Aeskimo a ku Canada ali ndi chinenero chawochawo chokhoza kulembedwa, anakhoza kuŵerenga mabuku athu a m’Chigrinilande. Zimenezi zingawatsegulire mpata wabwino kwambiri.”

Midzi imene inali pamtunda wa makilomita 50 mpaka 60 paulendo wapaboti inachezeredwa. “Pamene tinali kupita ku mudzi wa Qeqertat, tinatsatira kwambiri gombe, tikumayembekezera kupeza anthu amene akusaka ma narwhal. Zoonadi, tinapeza msasa pathanthwe wokhala ndi mabanja atatu kapena anayi, ovala zovala zaubweya, ndi mahema awo ndi mabwato awo. Atagwira uta m’manja, amunawo anasinthana kukhala pa mwala kuyembekezera kuona ma narwhal ofunika kwambiriwo. Pokhala atayembekezera kale kwa masiku angapo mosaphula kanthu, sanakondwere kutiona chifukwa tikanathamangitsa anamgumiwo! Anaoneka kukhala otanganitsidwa kwambiri ndi ntchito yawo. Akazi analandira mabuku ena, koma siinali nthaŵi yabwino ya kukambitsirana zowonjezereka. Pomalizira pake tinafika ku Qeqertat ndi nthaŵi ya 11 koloko usiku ndi kumaliza ulendo wathu m’mudzimo ndi nthaŵi ya 2 koloko mmamaŵa!”

“Pomalizira pake, tinafika pamudzi wa Siorapaluk, mudzi wa kumpoto zedi kwa Greenland. Uwo uli pagombe lamchenga munsi mwa matanthwe obiriŵira, ophimbidwa ndi udzu pamalo opanda zomera m’mbali zina.” Mbonizo zafika kumalekezero a dziko lapansi m’lingaliro lenileni m’ntchito yawo ya kulalikira, makamaka chakumpoto.

Ulendo Umalizidwa

Mbonizo zamaliza ntchito yawo. Zalalikira kunyumba ndi nyumba ndi kuhema ndi hema, zagaŵira mabuku, masabusikripishoni, zasonyeza mavidiyo, zalankhula ndi anthu ambiri a ku Greenland, ndipo zachititsa maphunziro a Baibulo. Tsopano ndi nthaŵi yopita kwawo. “Pamene tinakwera boti lathu lapulasitiki lopulumukiramo madzulowo kuti tipalase kuchoka pamudzi wa Moriusaq, kunali anthu angapo kugombe odzationa popita, akumakupiza mabuku kapena mabrosha amene tinawasiyira.”

Pambuyo pake, pamalo ena opanda mudzi a gombelo, Mbonizo zinadabwa kuona mwamuna wina akukupiza manja ake ataimirira pathanthwe​—pamenepo pamalo akutali kwenikweni! “Inde, tinapita kumtunda kukaonana naye. Anali mnyamata wa ku Berlin, Germany, amene anali kuyenda m’mbali mwa gombe m’bwato lake ndipo anali paulendowo kwa mwezi umodzi. Ku Germany Mboni za Yehova zinkamchezera kaŵirikaŵiri ndipo anali ndi mabuku awo osiyanasiyana. Tinakhala naye maola angapo, ndipo anakondweradi kukumana ndi Mboni kumalo otero.”

M’mudzi wa Savissivik, umene unapitiriridwa paulendo wobwerera, atumiki oyendayendawo analandiridwa ndi mtima wonse. Ena kumeneko anali atalandira ndi kuŵerenga mabuku chaka chapapitapo, ndipo anali ndi njala ya chakudya chowonjezereka chauzimu.

Kudutsa Melville Bay paulendo wobwerera kunatenga maola 14. “Tinaona kuloŵa kwa dzuŵa, kumene kunoko kumatenga maola ambiri, ndi kusinthasintha kosalekeza kwa maonekedwe okongola kwambiri. Kutuluka kwa dzuŵa, kumene kumatsatira nthaŵi yomweyo, kunatenganso nthaŵi yaitali. Pamene kuli kwakuti thambo la kumpoto koma chakummaŵa linali ndi maonekedwe a kuloŵa kwadzuŵa ofiira, dzuŵa linatuluka pamwamba pang’ono kummwera. Ndi maonekedwe ovuta kuwafotokoza​—kapena ngakhale kuwajambula​—mokwanira.” Apaulendo onsewo sanagone usiku wonse.

“Pamene tinafika ku Kullorsuaq, tinali otopa kwambiri. Koma tinali achimwemwe ndi okhutira. Tinali titamaliza bwino ulendowo! Pambali yonse yotsala ya ulendowo, tinapeza anthu ambiri okondwerera m’matauni ndi m’midzi ya kugombe. Funso limene linali kubwerezedwabwerezedwa linali lakuti, ‘Nchifukwa ninji ena a inu sangakhale nafe? Tili achisoni kukuonani mukupita mofulumira!’”

Ku Qaarsut banja laubwenzi linaitanira asanu a alendowo kudzadya nawo. “Banjalo linafuna kuti tigone. Koma popeza panali malo abwinopo oimikapo maboti makilomita 40 kuchoka pamenepo, tinakana kugona ndipo tinapitirizabe ulendowo. Pambuyo pake tinamva kuti chimwala chachikulu cha madzi oundana chinagamuka mmaŵa mwake, ndipo funde linapenula maboti aang’ono 14 pamalo pamene tinali titaima!”

Pomalizira pake, gululo linafikanso ku Ilulissat, atamaliza ulendo wawo wa ku Thule. Pafupifupi panthaŵi imodzimodziyo, ofalitsa ena aŵiri anali atapita kumalo okhala kwaokha kugombe lakummaŵa la Greenland. Pamaulendo aŵiriwo, ofalitsa anagaŵira chiŵerengero chonse cha mabuku 1,200, mabrosha 2,199, ndi magazini 4,224, ndipo analembetsa masabusikripishoni 152. Kulankhulana ndi okondwerera ambiriwo tsopano kumachitidwa mwa matelefoni ndi makalata.

Mosasamala kanthu za nthaŵi, nyonga, ndi ndalama zofunika, Mboni za Yehova zimapeza chimwemwe chachikulu pa kutsatira lamulo la Ambuye wawo la ‘kukhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.’​—Machitidwe 1:8.

[Bokosi patsamba 28]

Kugombe Lakummaŵa la Greenland

PAFUPIFUPI panthaŵi imodzimodziyo pamene gulu la ofalitsa linafika ku Thule, Mboni ziŵiri zokwatirana, Viggo ndi Sonja, zinapita kugawo lina losagwiridwako ntchito​—Ittoqqortoormiit (Scoresbysund) kugombe lakummaŵa la Greenland. Kuti afike kumeneko anapita ku Iceland, kukwera ndege kubwerera ku Constable Point kugombe la Greenland, ndiyeno kupita ndi helikoputala.

“Imeneyi inali nthaŵi yoyamba kuti Mboni za Yehova zifike kuno,” akusimba motero apainiya aŵiriwa, amene chinenero chawo ndi Chigrinilande. “Mosasamala kanthu za kukhala kwawo kwaokha, zinali zodabwitsa kuti anthuwo anali odziŵa zinthu. Ngakhale zili choncho, anasangalalanso kuphunzira zinthu zatsopano. Monga akatswiri osimba nthano, anatiuza mwachidwi za kusaka kwawo ma seal ndi zochitika zina m’chilengedwe.” Kodi iwo analabadira motani ku ntchito ya ulalikiwo?

“Pamene tinali kulalikira kunyumba ndi nyumba, tinakumana ndi J——, amene ali mphunzitsi wa katekizimu. ‘Zikomo kaamba ka kundiphatikiza pa omwe mukuchezera,’ anatero. Tinamsonyeza mabuku athu ndi mmene angawagwiritsire ntchito. Tsiku lotsatira anadza kwa ife nafuna kuphunzira za dzina lakuti Yehova. Tinamsonyeza mafotokozedwe m’mawu amtsinde m’Baibulo lake la Chigrinilande. Pamene tinachoka, anaimbira foni anzathu ku Nuuk kuti ayamikire kucheza kwathu. Tiyenera kupitirizabe kuyesa kuthandiza mwamunayu.

“Tinakumananso ndi O——, mphunzitsi amene amadziŵa Mboni za Yehova. Anatipatsa maola aŵiri kuti tilankhule ndi kalasi lake la azaka 14 mpaka 16. Motero tinawasonyeza vidiyo yathu ndi kuyankha mafunso awo. Mafunso Achichepere Akufunsa​—Mayankho Amene Amathandizaa ndi mabuku ena anatha mwamsanga. Pambuyo pake tinakumana ndi atatu a atsikanawo. Anali ndi mafunso ambiri, mmodzi wa iwo anali wokondwera kwambiri. Iye anafunsa kuti, ‘Kodi munthu amakhala motani Mboni? Ziyenera kukhala zabwinodi kukhala ngati inu. Atate anga alinso kumbali yanu.’ Tinalonjeza kumlembera kalata.

“Mu umodzi wa midziyo, tinakumana ndi mphunzitsi winanso wa katekizimu, M——, ndipo tinali ndi makambitsirano okondweretsa. Iye anati adzatsimikizira kuti amuna ena amene anapita kukasaka adzalandira mabuku athu atangobwerako. Chotero tsopano ndi ‘wofalitsa’ wathu kumalo akutali amenewo.”

Ngakhale kuti unali ulendo wozungulira kwambiri ndi wotopetsa, apainiya aŵiriwo anaona kuti zoyesayesa zawo zinafupidwa kwambiri.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena