Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 7/1 tsamba 19-24
  • Chilakiko cha Kulambira Koona Chayandikira

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Chilakiko cha Kulambira Koona Chayandikira
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Alendo m’Kachisi Wauzimu wa Mulungu
  • Malo Opatulika ndi Ziŵiya Zake
  • Chilakiko Chokwana cha Kulambira Koona
  • Chiukiriro cha Padziko Lapansi
  • Madyerero a Misasa Ophiphiritsira
  • Madyerero Osaiŵalika a m’Mbiri ya Israyeli
    Nsanja ya Olonda—1998
  • “Iwe Uzikhala Wosangalala Basi”
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Khamu Lalikulu Kwambiri
    Mapeto Osangalatsa a Masomphenya a M’buku la Chivumbulutso
  • Kachisi Wauzimu Wamkulu wa Yehova
    Nsanja ya Olonda—1996
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1996
w96 7/1 tsamba 19-24

Chilakiko cha Kulambira Koona Chayandikira

“Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse.”​—ZEKARIYA 14:9.

1. Kodi Akristu odzozedwa anakumana ndi chiyani mkati mwa Nkhondo Yadziko I, ndipo kodi zimenezi zinanenedweratu motani?

MKATI mwa nkhondo yadziko yoyamba, Akristu odzozedwa anasauka ndi mavuto ambiri ndi kumangidwa ndi maiko omenyana. Nsembe zawo za chitamando kwa Yehova zinaletsedwa kwambiri, ndipo analoŵa mu mkhalidwe wa ukapolo wauzimu. Zonsezi zinanenedweratu pa Zekariya 14:2, amene amafotokoza za kulimbana kwa amitundu onse ndi Yerusalemu. Mzinda wa ulosi umenewu ndiwo “Yerusalemu wakumwamba,” Ufumu wakumwamba wa Mulungu ndi malo a “mpando wachifumu wa Mulungu ndi wa Mwanawankhosa.” (Ahebri 12:22, 28; 13:14; Chivumbulutso 22:3) Odzozedwa a Mulungu amene ali padziko lapansi anaimira mzinda umenewo. Okhulupirika pakati pawo anapulumuka pa chiukirocho, akumakana kutengedwa undende kuchoka “m’mudzimo.”a

2, 3. (a) Kodi kulambira Yehova kwalakika motani chiyambire 1919? (b) Kodi nchiyani chimene chachitika kuyambira 1935?

2 Mu 1919 odzozedwa okhulupirika anamasulidwa kuchoka mu mkhalidwe wawo wa ukapolo, ndipo nthaŵi yomweyo anagwiritsira ntchito mwaŵi wa nyengo ya mtendere imene inadza pambuyo pa nkhondoyo. Monga akazembe a Yerusalemu wakumwamba, anagwiritsira ntchito mwaŵi waukulu wa kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu ndi kuthangatira kusonkhanitsa omalizira a 144,000. (Mateyu 24:14; 2 Akorinto 5:20) Mu 1931 anatenga dzina loyenerera la m’Malemba lakuti Mboni za Yehova.​—Yesaya 43:10, 12.

3 Kuyambira pamenepo, Mboni zodzozedwa za Mulungu sizinayang’ane kumbuyo. Ngakhale Hitler mwiniyo ndi gulu lake la Nazi sanathe kuwatontholetsa. Mosasamala kanthu za chizunzo cha padziko lonse, ntchito yawo yabala zipatso padziko lonse lapansi. Makamaka kuyambira chaka cha 1935, iwo agwirizana ndi “khamu lalikulu” la m’mitundu yonse, lonenedweratu m’buku la Chivumbulutso. Ameneŵanso ndiwo Akristu odzipatulira ndi obatizidwa ndipo “anatsuka zovala zawo, naziyeretsa m’mwazi wa Mwanawankhosa,” Yesu Kristu. (Chivumbulutso 7:9, 14) Komabe, sali odzozedwa, okhala ndi chiyembekezo cha moyo wakumwamba. Chiyembekezo chawo ndicho cha kulandira chimene Adamu ndi Hava anataya, ndiko kuti, moyo wangwiro waumunthu padziko lapansi la paradaiso. (Salmo 37:29; Mateyu 25:34) Lerolino, khamu lalikulu laposa pa anthu mamiliyoni asanu. Kulambira Yehova koona kukulakika, koma chilakiko chake chomaliza sichinadzebe.

Alendo m’Kachisi Wauzimu wa Mulungu

4, 5. (a) Kodi khamu lalikulu likulambira Yehova lili kuti? (b) Kodi ndi mwaŵi wotani umene lili nawo, ndipo mokwaniritsa ulosi uti?

4 Monga kunanenedweratu, khamu lalikulu “[likulambira, NW, mawu amtsinde] [Mulungu] usana ndi usiku m’kachisi mwake.” (Chivumbulutso 7:15) Popeza kuti sali Aisrayeli auzimu ansembe, mwinamwake Yohane anawaona ataima m’bwalo la Akunja la kachisi. (1 Petro 2:5) Ha, mmene kachisi wauzimu wa Yehova wakhalira ndi ulemerero nanga, bwalo lake likumadzaza namtindi wa anthu amene, limodzi ndi otsalira a Israyeli wauzimu, akumtamanda!

5 Khamu lalikulu silimatumikira Mulungu mumkhalidwe wochitiridwa chithunzi ndi bwalo lamkati la ansembe. Silimayesedwa lolungama ndi chifuno cha kuti akhale ana auzimu a Mulungu. (Aroma 8:1, 15) Komabe, mwa kusonyeza chikhulupiriro m’dipo la Yesu, amakhala ndi kaimidwe koyera pamaso pa Yehova. Amayesedwa olungama ndi chifuno chakuti akhale mabwenzi ake. (Yerekezerani ndi Yakobo 2:21, 23.) Nawonso ali ndi mwaŵi wa kupereka nsembe zovomerezeka pa guwa la nsembe lauzimu la Mulungu. Motero, ponena za khamu lalikulu limeneli, ulosi wa Yesaya 56:6, 7 ukukwaniritsidwa mwaulemerero: “Alendonso amene adziphatika okha kwa Yehova, kuti amtumikire iye, ndi kukonda dzina la Yehova, . . . nawonso ndidzamka nawo ku phiri langa lopatulika, ndi kuwasangalatsa m’nyumba yanga yopemphereramo; zopereka zawo zopsereza ndi nsembe zawo zidzalandiridwa pa guwa la nsembe langa; pakuti nyumba yanga idzatchedwa nyumba yopemphereramo anthu onse.”

6. (a) Kodi ndi nsembe zotani zimene alendo amapereka? (b) Kodi chotengera madzi chokhala m’bwalo la ansembe chimawakumbutsanji?

6 Pakati pa nsembe zimene alendo ameneŵa amapereka pali “chipatso cha milomo [monga nsembe ya ufa woperedwa bwino] yovomereza dzina [la Mulungu]” ndi “kuchitira chokoma ndi kugaŵira ena.” (Ahebri 13:15, 16) Chotengera madzi chachikulu chimene ansembe anali kugwiritsira ntchito kusambiramo chilinso chikumbutso chofunika kwa alendo ameneŵa. Iwonso ayenera kuvomereza kusamba kwauzimu ndi kwa makhalidwe pamene Mawu a Mulungu apitiriza kufotokozedwa bwino kwa iwo.

Malo Opatulika ndi Ziŵiya Zake

7. (a) Kodi a khamu lalikulu amaona motani mathayo a ansembe oyera mtima? (b) Kodi ndi mathayo owonjezereka otani amene ena a alendowo alandira?

7 Kodi Malo Opatulika ndi ziŵiya zake zili ndi tanthauzo lililonse kwa khamu lalikulu la alendo limeneli? Aha, iwo sadzakhala mu mkhalidwe wochitiridwa chithunzi ndi Malo Opatulika. Samabadwanso monga ana auzimu a Mulungu okhala ndi unzika wakumwamba. Kodi zimenezi zimawapangitsa kukhala ndi kaduka kapena nsanje? Ayi. M’malo mwake, amakondwera ndi mwaŵi wawo wa kuchirikiza otsalira a 144,000, ndipo amasonyeza chiyamikiro chachikulu pa chifuno cha Mulungu popanga ameneŵa kukhala ana auzimu, amene adzathandizana ndi Kristu kutukulira anthu ku ungwiro. Ndiponso, khamu lalikulu la alendo limaŵerengera kwambiri chisomo chachikulu cha Mulungu powapatsa chiyembekezo cha padziko lapansi cha moyo wosatha m’Paradaiso. Ena a alendo ameneŵa, mofanana ndi Anetini akale, apatsidwa mathayo a kuyang’anira zinthu pothandiza ansembe oyera mtima.b (Yesaya 61:5) Pakati pa ameneŵa Yesu amaika “[akalonga, NW] m’dziko lonse lapansi.”​—Salmo 45:16.

8, 9. Kodi ndi phindu lotani limene a khamu lalikulu amapeza posinkhasinkha za ziŵiya za m’Malo Opatulika?

8 Pamene kuli kwakuti sadzaloŵa m’Malo Opatulika ophiphiritsira, a khamu lalikulu la alendo amapeza maphunziro ofunika pa ziŵiya zake. Monga momwe choikapo nyali chinafunikira kukhala ndi mafuta nthaŵi zonse, moteronso alendowo amafunikira kukhala ndi mzimu woyera kuwathandiza kumvetsa mopitiriza choonadi cha m’Mawu a Mulungu, kudzera m’ngalande ya “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45-47) Ndiponso, mzimu wa Mulungu umawathandiza kulabadira chiitano ichi chakuti: “Mzimu ndi mkwatibwi [otsalira a odzozedwa] anena, Idzani. Ndipo wakumva anene, Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 22:17) Motero, choikapo nyali ndicho chikumbutso kwa khamu lalikulu cha thayo lawo la kuŵala monga Akristu ndi kupeŵa mkhalidwe, maganizo, mawu, kapena mchitidwe umene umamvetsa chisoni mzimu wa Mulungu.​—Aefeso 4:30.

9 Gome la mkate woonekera limakumbutsa a khamu lalikulu kuti, kuti akhalebe athanzi mwauzimu, ayenera kudya chakudya chauzimu nthaŵi zonse kuchokera m’Baibulo ndi m’zofalitsa za “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 4:4) Guwa la nsembe lofukizapo limawakumbutsa za kufunika kwa kupemphera mwaphamphu kwa Yehova kaamba ka thandizo kuti asunge umphumphu wawo. (Luka 21:36) Mapemphero awo ayenera kuphatikizapo mawu apansi pa mtima a chitamando ndi chiyamiko. (Salmo 106:1) Guwa la nsembe lofukizapo limawakumbutsanso za kufunikira kwawo kutamanda Mulungu m’njira zina, monga ngati mwa kuimba nyimbo za Ufumu ndi mtima wonse pamisonkhano yachikristu ndi mwa kukonzekera kwawo bwino kuti azipanga “chilengezo chapoyera cha chipulumutso.”​—Aroma 10:10, NW.

Chilakiko Chokwana cha Kulambira Koona

10. (a) Kodi ndi chinthu chachikulu chiti chimene tikuyembekezera? (b) Kodi nzochitika zotani zimene ziyenera kuchitika choyamba?

10 Lerolino “anthu ambiri” ochokera m’mitundu yonse akusonkhana kunyumba ya Yehova ya kulambira. (Yesaya 2:2, 3) Pochitira umboni zimenezi, Chivumbulutso 15:4 chimati: “Ndani adzakhala wosawopa ndi wosalemekeza dzina lanu [Yehova, NW]? Chifukwa inu nokha muli woyera; chifukwa mitundu yonse idzadza nidzalambira pamaso panu, popeza zolungama zanu zidaonetsedwa.” Zekariya chaputala 14 amafotokoza zimene zikutsatira. Posachedwapa, mzimu woipa wa anthu aunyinji padziko lapansi udzafika pachimake pamene asonkhana kotsirizira kuti amenyane ndi Yerusalemu​—oimira a Yerusalemu wakumwamba amene ali padziko lapansi. Pamenepo Yehova adzachitapo kanthu. Monga Mulungu Wankhondo, iye “adzatuluka, nadzachita nkhondo ndi amitundu aja” amene adzayesa kuyamba kuukira kumeneku.​—Zekariya 14:2, 3.

11, 12. (a) Kodi Yehova adzachita motani ndi kuukira kumene kudzadza pa olambira m’kachisi wake? (b) Kodi nchiyani chimene chidzachitika pa nkhondo ya Mulungu?

11 “Mliri umene Yehova adzakantha nawo mitundu yonse ya anthu imene idathira nkhondo pa Yerusalemu ndi uwu: nyama yawo idzawonda akali chiriri pa mapazi awo, ndi maso awo adzapuwala m’funkha mwawo, ndi lilime lawo lidzanyala m’kamwa mwawo. Ndipo kudzali tsiku lomwelo, kuti chisokonezo chachikulu chochokera kwa Yehova chidzakhala pakati pawo; ndipo adzagwira yense dzanja la mnzake; ndi dzanja lake lidzaukira dzanja la mnzake.”​—Zekariya 14:12, 13.

12 Kaya mliri umenewu udzakhala weniweni kapena wophiphiritsira, tifunikira kuyembekezera kuti tidzaone. Komabe, pali chinthu chimodzi chotsimikizirika. Pamene kuli kwakuti adani a Mulungu ayamba kuti aukire gulu lonse la atumiki a Yehova, adzaimitsidwa ndi zisonyezero zowopsa za mphamvu ya Mulungu wamphamvuyonse. Adzatontholetsa pakamwa pawo. Zidzachita monga ngati kuti lilime lawo lonyoza lanyala. Cholinga chawo chimodzi chidzakhala chachimbuuzi m’malingaliro mwawo, monga ngati kuti maso awo apuwala. Nyonga yawo yakuthupi, imene inawalimbitsa mtima kuukira, idzatha. Posokonezeka, adzaukirana ndi kuphana kwakukulu. Motero adani onse apadziko lapansi a kulambira Mulungu adzasesedwa. Potsirizira pake, mitundu yonse idzaumirizika kuzindikira uchifumu wachilengedwe chonse wa Yehova. Ulosi wakuti, “Yehova adzakhala mfumu ya dziko lonse,” udzakwaniritsidwa. (Zekariya 14:9) Pambuyo pake, Satana ndi ziŵanda zake adzamangidwa pamene Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi uyamba limodzi ndi madalitso aakulu amene asungidwa kaamba ka anthu.​—Chivumbulutso 20:1, 2; 21:3, 4.

Chiukiriro cha Padziko Lapansi

13. Kodi ndani amene ali “otsala onse a amitundu”?

13 Ulosi wa Zekariya ukupitiriza pa chaputala 14, vesi 16: “Kudzachitika kuti otsala onse a amitundu onse anadzawo kulimbana ndi Yerusalemu, adzakwera chaka ndi chaka kulambira mfumu Yehova wa makamu, ndi kusunga madyerero amisasa.” Malinga ndi kunena kwa Baibulo, anthu onse amene ali moyo lero amene adzapitiriza kukhala ndi moyo kufikira mapeto a dongosolo lino ndi amene adzaweruzidwa kukhala adani a kulambira koona adzalandira “chilango, ndicho chiwonongeko chosatha.” (2 Atesalonika 1:7-9; onaninso Mateyu 25:31-33, 46.) Sadzauka. Pamenepa, mwachionekere, “otsala” amenewo akuphatikizapo anthu amitundu amene anafa nkhondo yomaliza ya Mulungu isanachitike ndi amenenso ali ndi chiyembekezo chozikidwa pa Baibulo cha chiukiriro. “Ikudza nthaŵi,” Yesu analonjeza motero, “imene onse ali m’manda adzamva mawu ake, nadzatulukira, amene adachita zabwino, kukuuka kwa moyo; koma amene adachita zoipa kukuuka kwa kuweruza.”​—Yohane 5:28, 29.

14. (a) Kodi nchiyani chimene oukitsidwa adzayenera kuchita kuti adzapeze moyo wosatha? (b) Kodi nchiyani chimene chidzachitika kwa aliyense amene adzakana kudzipatulira kwa Yehova ndi kutsatira kulambira koona?

14 Oukitsidwa onsewa adzayenera kuchita kanthu kena kuti kuuka kwawo kukhale kwa moyo ndipo osati kwa chiweruzo choipa. Adzayenera kufika m’mabwalo apadziko lapansi a kachisi wa Yehova ndi kugwada modzipatulira kwa Mulungu kupyolera mwa Yesu Kristu. Woukitsidwa aliyense amene akana kuchita zimenezi adzakumana ndi mliri umodzimodziwo umene udzagwera amitundu amakono. (Zekariya 14:18) Adziŵa ndani chiŵerengero cha anthu oukitsidwa amene modzifunira adzagwirizana ndi khamu lalikulu kudzasangalala m’Madyerero a Misasa ophiphiritsira? Mosakayikira, padzakhala ambiri, ndipo kachisi wauzimu wamkulu wa Yehova adzakhaladi waulemerero kwambiri chifukwa cha zimenezo!

Madyerero a Misasa Ophiphiritsira

15. (a) Kodi nziti zinali mbali zina zapadera za Madyerero a Misasa a Israyeli wakale? (b) Kodi nchifukwa ninji ng’ombe 70 zinaperekedwa nsembe pamadyererowo?

15 Chaka chilichonse, Israyeli wakale anafunikira kusunga Madyerero a Misasa. Anali kutenga mlungu umodzi ndipo anali kuyamba atatuta zolima zawo. Inali nthaŵi ya chikondwerero cha mayamiko. M’nthaŵi yonse ya mlunguwu, anali kukhala m’misasa yofoleredwa ndi masamba a mitengo, makamaka makhwatha a kanjedza. Madyerero ameneŵa anakumbutsa Israyeli za mmene Mulungu anapulumutsira makolo awo kutuluka mu Igupto ndi mmene iyeyo anawasamalilira pamene anakhala m’misasa popupulikapupulika m’chipululu kwa zaka 40 kufikira ataloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. (Levitiko 23:39-43) Mkati mwa madyererowo, anapereka nsembe ng’ombe 70 pa guwa la nsembe. Malinga ndi umboni, mbali imeneyi ya madyerero inali kulosera ntchito yangwiro ndi yokwana yopulumutsa moyo yochitidwa ndi Yesu Kristu. Potsiriza pake mapindu a nsembe yake ya dipo adzafika kwa mbadwa zosaŵerengeka za mafuko 70 a anthu onse amene achokera kwa Nowa.​—Genesis 10:1-29; Numeri 29:12-34; Mateyu 20:28.

16, 17. (a) Kodi ndi liti pamene Madyerero a Misasa ophiphiritsira anayamba, ndipo anayenda motani? (b) Kodi khamu lalikulu limasunga nawo motani zimenezi?

16 Motero Madyerero a Misasa akale analoza kukusonkhanitsidwa kwachimwemwe kwa anthu ochimwa owomboledwa kuwaloŵetsa m’kachisi wauzimu wamkulu wa Yehova. Kukwaniritsidwa kwa Madyerero ameneŵa kunayamba pa Pentekoste mu 33 C.E. pamene kusonkhanitsidwa kwachimwemwe kwa Aisrayeli auzimu kuwaloŵetsa mu mpingo wachikristu kunayamba. (Machitidwe 2:41, 46, 47) Odzozedwa ameneŵa anazindikira kuti anali “alendo ndi ogonera” m’dziko la Satana chifukwa chakuti ‘[unzika, NW] wawo weniweni uli kumwamba.’ (1 Petro 2:11; Afilipi 3:20) Madyerero achimwemwewo anaphimbidwa kwakanthaŵi ndi mpatuko umene unachitika pa kuyambika kwa Dziko Lachikristu. (2 Atesalonika 2:1-3) Komabe, madyererowo anayambanso mu 1919 ndi kusonkhanitsidwa kwachimwemwe kwa omalizira a Aisrayeli auzimu a 144,000, motsatiridwa ndi kuja kwa khamu lalikulu lapadziko lonse la Chivumbulutso 7:9.

17 Khamu lalikulu likusonyezedwa kukhala lili ndi makhwatha a kanjedza m’manja mwawo, zimene zikusonyeza kuti nawonso ali osunga achimwemwe a Madyerero a Misasa ophiphiritsira. Monga Akristu odzipatulira, mwachimwemwe amagwirizana nawo m’ntchito ya kusonkhanitsira olambira ena m’kachisi wa Yehova. Ndiponso, monga ochimwa, amazindikira kuti alibe kuyenera kwachikhalire kwa kukhala padziko lapansi. Iwowo, limodzi ndi amene adzaukitsidwa mtsogolo, ayenera kusonyezabe chikhulupiriro mu nsembe ya dipo ya Kristu kufikira atapeza ungwiro waumunthu pamapeto pa Ulamuliro wa Kristu wa Zaka Chikwi.​—Chivumbulutso 20:5.

18. (a) Kodi nchiyani chimene chidzachitika pamapeto a Ulamuliro wa Yesu Kristu wa Zaka Chikwi? (b) Kodi kulambira koona kwa Yehova kudzalakika motani potsirizira pake?

18 Ndiyeno, olambira Yehova padziko lapansi adzaima pamaso pake mu ungwiro waumunthu osafunikira ansembe akumwamba. Nthaŵi idzakhala itafika pamene Yesu Kristu “adzapereka ufumu kwa Mulungu, ndiye Atate.” (1 Akorinto 15:24) Satana adzamasulidwa “kanthaŵi” kuti ayese anthu angwiro. Munthu aliyense wosakhulupirika adzawonongedwa kosatha, limodzi ndi Satana ndi ziŵanda zake. Awo amene adzakhalabe okhulupirika adzapatsidwa moyo wosatha. Adzakhala nzika zachikhalire m’Paradaiso wapadziko lapansi. Motero Madyerero a Misasa ophiphiritsirawo adzafika pamapeto ake aulemerero ndi achipambano. Kulambira koona kudzakhala kutalakika ku ulemerero wosatha wa Yehova ndi chimwemwe chamuyaya cha anthu.​—Chivumbulutso 20:3, 7-10, 14, 15.

[Mawu a M’munsi]

a Kaamba ka kufotokozedwa kwa vesi ndi vesi kwa Zekariya chaputala 14, onani buku la Paradise Restored to Mankind​—By Theocracy!, lofalitsidwa mu 1972 ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc., mitu 21 ndi 22.

b Kaamba ka zowonjezereka pa Anetini amakono, onani Nsanja ya Olonda, ya April 15, 1992, tsamba 16.

Mafunso a Kupenda

◻ Kodi “Yerusalemu” anaukiridwa motani m’nkhondo yadziko yoyamba?​—Zekariya 14:2.

◻ Kodi nchiyani chimene chachitika kwa anthu a Mulungu chiyambire 1919?

◻ Kodi ndani lerolino amene amasunga nawo Madyerero a Misasa ophiphiritsira?

◻ Kodi kulambira koona kudzalakika motani kotheratu?

[Chithunzi patsamba 23]

Makhwatha a kanjedza anali kugwiritsiridwa ntchito pokondwerera Madyerero a Misasa

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena