Kuyendera Dziko Lolonjezedwa
TINENE kuti bwenzi lanu lakuuzani kuti lakugulirani—monga mphatso—nyumba yatsopano pamalo okongola ndi abata. ‘Ikuoneka motani?’ mungadzifunse. Mosakayikira mungakhale wofunitsitsa kudzionera nokha nyumba imeneyi, kuloŵamo ndi kuona chipinda chilichonse. Ndi iko komwe, imeneyi ndi nyumba yanu yatsopano!
Mu 1473 B.C.E., Yehova anapatsa mtundu wakale wa Israyeli nyumba yatsopano—Dziko Lolonjezedwa, dera lokwanira pafupifupi makilomita 500 kuchokera kumpoto mpaka kummwera ndipo makilomita 55 m’bwambi, pa avareji.a Lokhala mu imene yatchedwa kuti Fertile Crescent, Dziko Lolonjezedwalo linali malo abwino kukhalamo, lodalitsidwa ndi mikhalidwe yakeyake yapadera.
Koma kodi nchifukwa ninji inu lerolino muyenera kuchita chidwi ndi “nyumba” imene inapatsidwa kwa wina wake, makamaka munthu amene anakhalako kalelo? Chifukwa chakuti kudziŵa dziko la m’mbiri limeneli kungakuthandizeni kumvetsa nkhani za m’Baibulo. “M’dziko la Baibulo,” analemba motero malemu Profesa Yohanan Aharoni, “malo ake ndi mbiri nzoloŵana kwambiri kwakuti palibe chimene chingamvetsetsedwe bwino popanda thandizo la chinzake.” Ndiponso, pamene linafika pachimake Dziko Lolonjezedwa linapereka chitsanzo pamlingo waung’ono cha zimene Paradaiso mu Ufumu wa Mulungu adzatanthauza kwa anthu posachedwapa padziko lonse lapansi!—Yesaya 11:9.
Mu utumiki wake wa padziko lapansi, Yesu Kristu anagwiritsira ntchito zinthu zimene aliyense anaona za mu Dziko Lolonjezedwa kupereka maphunziro othandiza. (Mateyu 13:24-32; 25:31-46; Luka 13:6-9) Ifenso tingaphunzire zambiri zothandiza mwa kulingalira za mbali zina za Palestina wakale. Tiyeni tiyende mkati mwa zina za zipinda zake, titero kunena kwake, kufufuza mikhalidwe ina yapadera ya dzikoli limene linali kwawo kwa anthu a Mulungu kwa zaka mazana ambiri. Monga momwe tidzaonera, Dziko Lolonjezedwa lingatiphunzitse zambiri.
[Mawu a M’munsi]
a Mawuwo “Dziko Lolonjezedwa” m’nkhani zino agwiritsiridwa ntchito malinga ndi mmene analili m’nthaŵi zakale, monga momwe Baibulo limafotokozera, ndipo sizikuloŵetsamo zonena zamakono za ndale/chipembedzo pamalowo.
[Mawu a Chithunzi patsamba 2]
Cover: Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 3]
Garo Nalbandian