Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w92 5/1 tsamba 24-25
  • Iye Anagaŵira Aisrayeli Zosoŵa Zawo m’Chipululu cha Sinai

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Iye Anagaŵira Aisrayeli Zosoŵa Zawo m’Chipululu cha Sinai
  • Nsanja ya Olonda—1992
  • Nkhani Yofanana
  • Mafunso Ochokera kwa Owerenga
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yophunzira)—2023
  • Sinai Phiri la Mose ndi Chifundo
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Chipululu cha Yuda—Chosabala Koma Chosangalatsa
    Nsanja ya Olonda—1989
  • Musaiwale Yehova
    Nsanja ya Olonda—2009
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1992
w92 5/1 tsamba 24-25

Malo a ku Dziko Lolonjezedwa

Iye Anagaŵira Aisrayeli Zosoŵa Zawo m’Chipululu cha Sinai

TAYEREKEZERANI mamiliyoni a anthu​—amuna, akazi, ndi ana​—akupita kukaloŵa ‘m’chipululu chachikulu ndi chowopsacho, munali njoka zamoto, ndi zinkhanira, mouma mopanda madzi’!

Mawu a Mulungu amenewo opezeka pa Deuteronomo 8:15 amatipatsa chithunzi cha ulendo umene uyenera kuti unawoneka wowopsa kwa Aisrayeli pamene anatuluka mu Igupto ndi kuloŵa m’chipululu cha Sinai. Panali vuto limodzi lodetsa nkhaŵa kwenikweni: Kodi ndani amene akawagaŵira chakudya chokwanira ndi madzi?

Aisrayeli adali muukapolo kumene anachokerako m’dera la kumatsiriro a mtsinje wa Nile, koma sanasoŵe kanthu kalikonse. Zithunzithunzi zolembedwa pazipupa m’manda akale zimasonyeza dzinthu dzosiyanasiyana monga mpesa, mavwendi, ndi dzinthu dzina, pamodzi ndi nsomba ndi zifuyo zimene zikapereka zakudya zosiyanasiyana. Pamenepa, nkowona chotani nanga kudandaula kwawo m’chipululu kwakuti: ‘Adzatipatsa nyama ndani? Tikumbukira nsomba tinazidya m’Igupto chabe, mankhaka, ndi mavwendi, ndi anyesi a mitundu itatu!’​—Numeri 11:4, 5; 20:5.

Pamene Aisrayeli anawoloka Nyanja Yofiira, anauwona mkhalidwe weniweni wa chipululu cha Sinai. Iwo sanatenge njira yomwe amalonda anayendamo kaŵirikaŵiri yodzera kumpoto koma anakhota pamene anafika kubondo la Nyanja Yofiira. Atayenda kwa makilomita 80 m’chipululu, vuto lawo lakusoŵa madzi linakula. Sanakhoza kumwa madzi amene anapeza, chifukwa chakuti anali oŵaŵa ndipo mwinamwake opatsa matenda. ‘Tidzamwa chiyani?’ iwo anadandaula motero. Mulungu analoŵapo, nasandutsa madziwo kukhala okoma.​—Eksodo 15:22-25.

Tawonani mmene ukuwonekera mlongo wa ngamira pamwambapo. Mukhoza kumvetsetsa funso lakuti ndimotani mmene Israyeli akakhozera kuyendabe m’chipululu kumka ku phiri la Sinai. Kodi ndimotani mmene akapitirizira kudzipezera iwo eni pamodzi ndi nkhosa ndi ng’ombe​—madzi okwanira ndi chakudya​—zomwe anafunikira kuti akhale ndimoyo?​—Eksodo 12:38.

Iwo anapitabe patsogolo pang’ono kulinga kum’mwera ndipo anapeza madzi otonthoza ndi chakudya pa Elimu. (Eksodo 15:27) Komabe, kumeneko sikumene ankapita. Iwo analinga ku “phiri la Mulungu,” phiri la Sinai. (Eksodo 3:1; 18:5; 19:2; 24:12-18) Panali mtunda wa makilomita 120 kukafika kumeneko​—kupyola m’dziko lamajidumajidu ndi louma.

Pamene gulu lalikululo linayenda kulinga ku phiri la Sinai, anafika pafupi​—ndipo mwachiwonekere anaima​—pamalo amadzi aakulu a Feiran. Kachigawo kake kakuwoneka pachithunzithunzi patsamba lapandunjili.a Malo amadziwo amalamba ndi njira m’chipululu, kulinga ku Nyanja Yofiira (Thamanda la Suez). Ha, anapeza chitonthozo chotani nanga kumeneko!

Pamene kuli kwakuti chipululu cha Sinai chingayenere malongosoledwe akuti ‘chipululu chachikulu ndi chowopsa,’ Aisrayeli anakhala mumthunzi wabwino wa mngwalangwa ndi mitengo ina pamalo amadzi a Feiran. Iwo anatha kupeza kanjedza wabwino wokwanira, monga chakudya chokonzeka kale ndi chimene anakhoza kunyamula popita.

Zonsezi zinali zotheka chifukwa chakuti madzi apansi anatumphukira pamwamba panthaka ya Feiran. Tangoyerekezerani mmene mukamverera ngati munali m’chipululu ndipo mwadzidzidzi mutulukira madzi akumwa ozizira! Izi zimasonyeza kuti ngakhale m’chipululu cha Sinai alipo malo ena opezekako madzi. Nthaŵi zina payenera kukumbidwa chitsime chakuya ndithu. Ndiyeno pakakhala ntchito yakutunga madzi ofunikawo ndi kudzaza mitsuko yambiri, makamaka ngati nkhosa ndi ng’ombe zifuna kumwa madzi. Kufikira lerolino anthu a fuko la Bedouin a ku Sinai amakakhala ku zitsime kumene angatunge madzi awo ndi a ngamira zawo.​—Yerekezerani ndi Genesis 24:11-20; 26:18-22.

Inde, mosasamala kanthu kuti nthaŵi zina anadandaula ndi kusoŵa kumene kunawoneka kukhala kosatha, Aisrayeli anali ndi madzi ndi chakudya. Nthaŵi zina Mulungu anagaŵira zoterozo mozizwitsa. (Eksodo 16:11-18, 31; 17:2-6) Panthaŵi zina mwachiwonekere, anawatsogoza kumalo ‘kopumulira’ kumene zosoŵa zawo zikakhutiritsidwa ndi zogaŵira zachilengedwe. (Numeri 10:33-36) Nthaŵi yonseyo, iye anawaikira patsogolo kuchuluka kwa zinthu kumene kunayembekezera okhulupirika m’Dziko Lolonjezedwa.​—Deuteronomo 11:10-15.

[Mawu a M’munsi]

a Chithunzithunzi chachikulu chirimo mu Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1992.

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

[Mawu a Chithunzi patsamba 24]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

[Mawu a Chithunzi pamasamba 24, 25]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

[Mawu a Chithunzi patsamba 25]

Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena