Malo a ku Dziko Lolonjezedwa
Sinai Phiri la Mose ndi Chifundo
PAMENE muganiza za phiri la Sinai, mwinamwake mumakumbukira Mose. Chifukwa ninji? Chifukwa Mose analandira Chilamulo cha Mulungu paphiri m’dera la ndomo ya Sinai. Phiri liti? Mothekera limene lasonyezedwa pamwambapa.a
Kum’mwera kwa ndomoyo, chapakati pa mbali ziŵiri za Nyanja Yofiira, pali mtandadza wa mapiri aŵiri. Malo wamba ameneŵa amayenerana ndi zochitika za m’Baibulo zonena za Mose. Phiri limodzi limatchedwa Jebel Musa, kutanthauza “Phiri la Mose.”
Zochitika zosiyanasiyana za m’Baibulo zimachititsa dzinalo kukhala loyenera kwambiri. Kodi mukumbukira kuti Mose analikuŵeta nkhosa za Yetero pamene mngelo anawonekera m’chitsamba choyaka moto? Kodi kumeneko kunali kuti? Baibulo limati kunali ku ‘phiri la Mulungu, ku Horebe,’ limene limatchedwanso phiri la Sinai. (Eksodo 3:1-10; 1 Mafumu 19:8) Mose atatulutsa anthu a Mulungu mu Igupto, anawabweretsa kunoko. Eksodo 19:2, 3 amati “Israyeli anamanga tsasa pamenepo pandunji pa phirilo. Ndipo Mose anakwera kwa Mulungu; ndipo Yehova ali m’phirimo anamuitana.”
Kumeneko kunali kuyamba kwa Mose kukwera phiri la Sinai, ndipo sanangoyenda mtunda waufupi kukwera matereziwo. Timaŵerenga kuti: “Yehova anatsikira pa phiri la Sinai, pamutu pake pa phiri; ndipo Yehova anaitana Mose akwere pamutu pa phiri.”—Eksodo 19:20.
Oyendera malo amakono zikwi zambiri alikwera movutikira usiku m’tinjira toikidwa zizindikiro kufika pansonga yake, kukhala pompo kuti awone dzuŵa likutuluka, ndiyeno kutsika kufika munsi mwake masana. Sizinali choncho ndi Mose. Mulungu anamuuza kuti: “Ukwere kudza kwa ine m’phiri muno, nukhale pompano; ndipo ndidzakupatsa magome amiyala, ndi chilamulo.” Panthaŵi yomweyo “Mose anakhala m’phiri masiku makumi anayi usana ndi usiku.”—Eksodo 24:12-18.
Chotero zili zomveka kuti dzina la Mose lili logwirizana ndi phirili, koma nchifukwa ninji “chifundo” chili mbali ya dzinalo? Eya, pamene Mose anali m’phirimo kulandira Chilamulo, anthu m’chigwa munsi mwake (mwinamwake Chigwa cha er-Raha pachithunzithunzipo) anatenga njira yopusa. Iwo anakakamiza mbale wa Mose kupanga mulungu. Aroni anati: “Thyolani mphete zagolidi . . . ndi kubwera nazo kwa ine.” Motero anapanga mwana wa ng’ombe wagolidi womlambira. Zimenezi zinakwiitsa Mulungu wowona ndi kuphetsa zikwi zambiri. (Eksodo 32:1-35) Koma Aroni anachitiridwa chifundo ndipo sanaphedwe. Chifukwa?
Ndemanga ya Mulungu pa Eksodo 32:10 imasonyeza kuti iye sanawone Aroni monga wochititsa wamkulu wa tchimo la Israyeli. Ndipo pamene nthaŵi yakuthetsa mlanduwo inafika, “ana amuna onse a Levi” anasankha mbali ya Mulungu, mosakaikira anaphatikizapo Aroni. (Eksodo 32:26) Choncho mosasamala kanthu za kukhala ndi liŵongo lina lake kwa Aroni, iye anachitiridwa chifundo ndi Mulungu munsi mwa phiri la Sinai.
Pambuyo pake, Mose anasonyeza chikhumbo cha kudziŵa Yehova bwino koposa ndi kuwona ulemerero Wake. (Eksodo 33:13, 18) Pamene kunali kosatheka kwa Mose kuwona nkhope ya Mulungu, Yehova anamsonyezadi wina wa ulemerero Wake, akumagogomezera kuti Iye ‘adzachitira chifundo amene [Iye] adzamchitira chifundo.’ (Eksodo 33:17–34:7) Kunali koyenera kwambiri kwa Mulungu kugogomezera chifundo chake, pakuti Baibulo limagwiritsira ntchito “chifundo” nthaŵi zambiri ponena za zochita za Mulungu ndi Israyeli, amene anamloŵetsa m’pangano pa Sinai.—Salmo 103:7-13, 18.
Alendo ochezera phiri la Sinai lerolino amapeza nyumba ya agulupa munsi mwake, imene singakumbutse konse wina za kulambira kowona kumene Mose anaphunzira paphiri lili pamwambalo. Mmalomwake, chipembedzo cha m’nyumba ya agulupa imeneyo chimasumikidwa pa zifaniziro zachipembedzo. Chosonyezedwa panopa ndicho “Makwerero a ku Paradaiso.” Chinatengedwa m’buku la mgulupa wa ku Byzantium, John Climacus. Atatha pafupifupi zaka 40 m’kachipinda ka m’nyumba ya agulupa, anakhala mkulu wa nyumba ya agulupa nalemba za makwerero ophiphiritsira opita kumwamba. Koma tawonani kuti atsogoleri ena achipembedzo akukokedwera ku chizunzo chosatha m’moto wahelo ndi ziŵanda. Ndichithunzithunzi chosonyeza bwino lomwe zimene zikuchitika, koma nchotsutsa malemba!—Mlaliki 9:5, 10; Yeremiya 7:31.
Mosiyana ndi chiphunzitso chonyenga chimenecho, chowonadi nchakuti Wamphamvuyonseyo ali “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi.” (Eksodo 34:6) Mose anayandikira pafupi ndi Mulungu wachifundo ameneyu pa phiri la Sinai.
[Mawu a M’munsi]
a Kuti muwone chithunzithunzi chachikulu, onani Kalenda ya Mboni za Yehova ya 1993.
[Mawu a Chithunzi patsamba 8]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.
[Mawu a Chithunzi patsamba 9]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.