Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • lfb phunziro 23 tsamba 60-tsamba 61 ndime 4
  • Analonjeza Kuti Azimvera Yehova

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Analonjeza Kuti Azimvera Yehova
  • Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
  • Nkhani Yofanana
  • Yehova Apereka Malamulo Ake
    Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo
  • Sinai Phiri la Mose ndi Chifundo
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Phunzirani Njira za Yehova
    Nsanja ya Olonda—2005
  • Aisiraeli Sanachite Zimene Analonjeza
    Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
Onani Zambiri
Zimene Tingaphunzire Munkhani za M’Baibulo
lfb phunziro 23 tsamba 60-tsamba 61 ndime 4
Aisiraeli aima m’munsi mwa phiri la Sinai

MUTU 23

Analonjeza Kuti Azimvera Yehova

Patadutsa miyezi iwiri chichokereni ku Iguputo, Aisiraeli anafika paphiri la Sinai ndipo anamanga misasa. Yehova anauza Mose kuti akwere m’phirimo. Kumeneko anamuuza kuti: ‘Ndapulumutsa Aisiraeli. Ngati angandimvere komanso kusunga malamulo anga, adzakhala anthu anga apadera.’ Mose anatsika m’phirimo n’kukauza Aisiraeli zimene Yehova ananenazi. Kodi iwo anatani atamva zimenezi? Anayankha kuti: ‘Tidzachita chilichonse chimene Yehova wanena.’

Mose anapitanso kuphiri kuja. Ndiyeno Yehova anamuuza kuti: ‘Ndilankhula nanu pakadutsa masiku atatu. Uchenjeze anthu kuti asakwere phirili.’ Mose anatsika n’kukauza Aisiraeli kuti akonzekere kumva zimene Yehova adzawauze.

Aisiraeli akuona mphenzi ndi mtambo wakuda paphiri la Sinai

Patadutsa masiku atatu, kunayamba kuchita mphezi ndi mabingu ndipo paphiri lonselo panali mtambo wakuda. Kunamvekanso kulira kwa mphamvu kwa lipenga. Ndiyeno paphiripo panali moto kusonyeza kuti Yehova wabwera paphiripo. Aisiraeli anachita mantha kwambiri moti anayamba kunjenjemera. Phiri lonselo linkafuka utsi komanso linkagwedezeka kwambiri. Nalonso phokoso la lipenga lija linkawonjezereka. Ndiyeno Mulungu anati: ‘Ine ndine Yehova. Musamalambire milungu ina.’

Mose anakweranso m’phiri muja ndipo Yehova anamupatsa malamulo oti anthuwo azitsatira pomulambira komanso pochita zinthu zatsiku ndi tsiku. Mose analemba malamulowo n’kukawawerengera Aisiraeli. Iwo analonjeza kuti: ‘Tidzachita zonse zimene Yehova wanena.’ Aisiraeliwo analonjeza kuti azimvera Mulungu. Koma kodi anachitadi zimenezi?

“Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, moyo wanu wonse ndi maganizo anu onse.”​—Mateyu 22:37

Mafunso: Kodi paphiri la Sinai panachitika zotani? Kodi Aisiraeli analonjeza kuti adzachita chiyani?

Ekisodo 19:1-25; 20:1-21; 24:1-8; Deuteronomo 7:6-9; Nehemiya 9:13, 14

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena