Kodi Mukukumbukira?
Kodi mwasangalala kuŵerenga makope a Nsanja ya Olonda aposachedwapa? Chabwino, tiyeni tione ngati mungayankhe mafunso otsatirawa:
◻ Kodi mawu a Yesu akuti, “Zochimwa za anthu alionse muwakhululukira, zikhululukidwa kwa iwo,” amatanthauza kuti Akristu angathe kukhululukira machimo? (Yohane 20:23)
Palibe umboni wa m’Malemba umene umatisonyeza kuti Akristu alionse, kapena ngakhale akulu oikidwa mumpingo, ali ndi ulamuliro wochokera kwa Mulungu wa kukhululukira machimo. Nkhani yonse ya Yesu imasonyeza kuti kudzera mwa mzimu atumwi anapatsidwa ulamuliro wapadera wa kukhululukira kapena kusakhululukira machimo. (Onani Machitidwe 5:1-11; 2 Akorinto 12:12.)—4/15, tsamba 28.
◻ Kodi nchiyani chimene chili chapadera m’matembenuzidwe a buku la Masalmo a J. J. Stewart Perowne lofalitsidwa koyamba mu 1864?
M’kutembenuza kwake Perowne anayesetsa kumamatira “mosamalitsa ku mpangidwe wachihebri, ponse paŵiri m’kalembedwe ka chinenerocho ndi m’maumbidwe a mawu.” Pochita motero anakonda kubwezeretsa dzina la Mulungu mu mpangidwe wa “Yehova.”—4/15, tsamba 31.
◻ Kodi Yesu anapereka chitsogozo chotani kwa otsatira ake ponena za kuchita ndi maboma a dzikoli?
Yesu anati: “Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.” (Mateyu 22:21) Ananenanso kuti: “Amene akakukakamiza kumperekeza njira imodzi, upite naye ziŵiri.” (Mateyu 5:41) Pano Yesu anali kusonyeza njira ya kugonjera kofunitsitsa pa zofunsira zoyenera, kaya ndi m’maunansi a anthu kapena m’zofunika za boma zimene zili zogwirizana ndi lamulo la Mulungu. (Luka 6:27-31; Yohane 17:14, 15)—5/1, tsamba 12.
◻ Kodi ‘kuyenda m’choonadi’ kumatanthauzanji? (Salmo 86:11)
Zimenezi zikuphatikizapo kuchita mogwirizana ndi zofunika za Mulungu ndi kumtumikira mokhulupirika ndi moona mtima. (Salmo 25:4, 5; Yohane 4:23, 24)—5/15, tsamba 18.
◻ Kodi Yehova anakwaniritsanji mwa kutumiza Yona ku Nineve?
Monga momwe zinthu zinachitikira, ntchito ya Yona ya kulalikira ku Nineve inasonyeza kusiyana pakati pa Anineve olapa ndi Aisrayeli ouma khosi, amene analibiretu chikhulupiriro ndi kudzichepetsa. (Yerekezerani ndi Deuteronomo 9:6, 13; Yona 3:4-10.)—5/15, tsamba 28.
◻ Kodi ndani amene ali Njoka ndipo ndani amene ali “mkazi” wotchulidwa pa Genesis 3:15?
Njokayo sili yawamba koma amene anaigwiritsira ntchito, Satana Mdyerekezi. (Chivumbulutso 12:9) “Mkaziyo” si Hava ayi koma ndi gulu lakumwamba la Yehova, mayi wa atumiki ake odzozedwa ndi mzimu padziko lapansi. (Agalatiya 4:26)—6/1, tsamba 9.
◻ Kodi munthu angatuluke motani m’Babulo Wamkulu ndi kupeza malo opulumukira? (Chivumbulutso 18:4)
Ayenera kudzilekanitsa kotheratu ndi magulu a zipembedzo zonyenga ndiponso miyambo yake ndi mzimu umene zimachirikiza, ndiyeno ayenera kuthaŵira kumalo opulumukira m’gulu lateokrase la Yehova. (Aefeso 5:7-11)—6/1, tsamba 18.
◻ Kodi nchifukwa ninji chiombankhanga chimatchulidwa nthaŵi zambiri m’Malemba?
Olemba Baibulo amatchula za mikhalidwe ya chiombankhanga kukhala ikuimira zinthu zonga nzeru, chitetezo chaumulungu, ndi liŵiro.—6/15, tsamba 8.
◻ Kodi atumiki a Mulungu lerolino amene ali ndi chiyembekezo cha padziko lapansi ali ndi mzimu wa Mulungu wofanana ndi umene Akristu odzozedwa ali nawo?
Kwenikweni, yankho nlakuti, inde. Mzimu wa Mulungu umene magulu onsewo amalandira ngofanana, ndipo chidziŵitso ndi kuzindikira zinthu zimapezedwa ndi magulu aŵiri onsewo mofanana.—6/15, tsamba 31.
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kwa ife lerolino kupenda utumiki wopatulika umene ansembe a Israyeli anachita pa kachisi mu Yerusalemu?
Mwa kuchita zimenezo timazindikira mokwanira bwino za makonzedwe achifundo mwa amene anthu ochimwa lerolino amayanjanitsidwira ndi Mulungu. (Ahebri 10:1-7)—7/1, tsamba 8.
◻ Kodi kachisi wachiŵiri womangidwa pa Yerusalemu anapeza ulemerero wokulirapo motani kuposa amene anamangidwa ndi Solomo?
Kachisi wachiŵiriyo anakhala zaka 164 kuposa kachisi wa Solomo. Olambira ambiri ochokera m’maiko ambiri anafika m’mabwalo ake. Chofunika kwambiri nchakuti, kachisi wachiŵiri ameneyu anali wapadera kwambiri chifukwa cha kukhala ndi Mwana wa Mulungu, Yesu Kristu, akumaphunzitsa m’mabwalo ake.—7/1, masamba 12, 13.
◻ Kodi Mulungu anamanga liti kachisi wake wauzimu?
Mmenemu munali mu 29 C.E. pamene Mulungu anavomereza pemphero la ubatizo wa Yesu. (Mateyu 3:16, 17) Kuvomereza kwa Mulungu thupi la Yesu kunatanthauza kuti, m’lingaliro lauzimu, guwa la nsembe lalikulu kuposa limene linali m’kachisi wa Yerusalemu linali litayamba kugwira ntchito.—7/1, masamba 14, 15.
◻ Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhala okhululukira?
Kukhululukira wotilakwira amene wapepesa nkofunika ngati titi tisunge umodzi wachikristu. Udani ndi kusunga zinthu kukhosi kumatibera mtendere wamaganizo. Ngati tili osakhululukira, tili pangozi yakuti tsiku lina Yehova sadzatikhululukiranso machimo athu. (Mateyu 6:14, 15)—7/15, tsamba 18.
◻ Kodi Aisrayeli akanakhala motani oyera?
Chiyero chinali chotheka kokha mwa kukhala ndi unansi wapafupi ndi Yehova, Mulungu woyera, ndi kumlambira kwawo koyera. Anafunikira chidziŵitso cholongosoka cha “Woyerayo” kuti amlambire m’chiyero, chakuthupi ndi chauzimu. (Miyambo 2:1-6; 9:10)—8/1, tsamba 11.