Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w96 8/15 tsamba 22-26
  • “Mulu wa Mboni” m’Dziko la “Phiri la Mulungu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Mulu wa Mboni” m’Dziko la “Phiri la Mulungu”
  • Nsanja ya Olonda—1996
  • Timitu
  • Mwa Kuyenda pa Bwato, ndi Matola a Kumidzi, Kapena pa Njinga?
  • Kuloŵa Mkatikati
  • Kumka cha Kumtunda Kumpoto
  • Kuchitira Umboni m’Mizinda
  • Kulinganiza Ulendo?
Nsanja ya Olonda—1996
w96 8/15 tsamba 22-26

“Mulu wa Mboni” m’Dziko la “Phiri la Mulungu”

PA mapu ya kontinentiyo, ngati mutsatira gombe la nyanja la West Africa ndi kumka kummaŵa m’mbali mwa Gulf of Guinea, kufika pamalo pamene gombelo limakhotera kummwera, mudzapeza Cameroon. Ngati mupitirizabe kumka kummwera kumunsi kwa gombelo, mudzafika kumagombe aakulu a mchenga wakuda. Mchenga wakudawo unakhalako chifukwa cha volokano ya Mount Cameroon.

Phiri losongoka limeneli la mamitala 4,070 nlotchuka kwambiri m’deralo. Pamene dzuŵa limene likuloŵa liunikira zigwa za Mount Cameroon, limapereka maonekedwe amphamvu okondweretsa​—ofiirira, achikasu, agolidi, ndi a crimson. Maonekedwe onsewa ndi madambo ake apafupi amaonekera m’nyanja, zimenezi zikumapangitsa kusiyanitsa thambo ndi nthaka kukhala kovuta. Nkosavuta kumvetsa chifukwa chake mafuko opembedza zinthu zolengedwa a ku chigawocho anatcha phirilo kuti Mongo Ma Loba, limene tanthauzo lake ndilo “Galeta la milungu,” kapena monga momwe ambiri amalidziŵira, “Phiri la Mulungu.”

Kutsika cha kummwera, kuli mtunda wautali wa magombe amchenga woyera, wokhala ndi mitengo ya mngole. Kuwonjezera pa gombe lokongolalo, dera lokulira la dzikolo nlokutidwa ndi nkhalango ya m’dera lotentha yothinana, yokafika kumalire a Congo ndi Central African Republic ndi kumpoto ku Nigeria ndi dera la Chad la kumunsi kwa Sahara. Mbali yakumadzulo ya dzikolo njamapiri, ikumakumbutsa woyenda za mbali zina za Ulaya. Komabe, mkhalidwe wotentha wa malowo udzakuchititsani kusaiŵala kuti muli pafupi kwambiri ndi equator. Kusiyanasiyana kwa malo ake kumachititsa oonetsa malo alendo ambiri kufotokoza Cameroon kukhala chosonyezera Afirika chaching’ono. Lingaliro limeneli limachirikizidwa ndi mafuko osiyanasiyana ndi olankhula zinenero 220 zodziŵika bwino.

Mukanapita ku Cameroon, mwina mukanakakhala mu imodzi ya mahotela aakulu ku doko la Douala, kapena likulu lake, Yaoundé. Koma mukanaphonya mwaŵi wa kudziŵa kanthu kena ponena za moyo wa anthu, makamaka wa Mboni za Yehova zoposa 24,000, zimene zakhala zikupanga “mulu wa mboni” m’dziko lonseli la “Phiri la Mulungu.”a Bwanji osapanga ulendo wodutsa dzikolo kukaonana ndi zina za izo? Kutulukira kwanu dziko limeneli la West Africa kudzakufupani kwambiridi.

Mwa Kuyenda pa Bwato, ndi Matola a Kumidzi, Kapena pa Njinga?

Pamene Sanaga, mtsinje wautali koposa mu Cameroon, amathirira m’nyanja, mpotakasukira kwambiri cham’mbali. Kaŵirikaŵiri Mboni za Yehova zimafunikira kuyenda ndi mabwato kuti zifikire nzika zonse za chigawo chachikulu chimenechi. Zimenezi nzimene ofalitsa Ufumu asanu ndi anayi a kagulu kena ku Mbiako amachita. Aŵiri a iwo amakhala pa mtunda wa makilomita 25, m’mudzi wa Yoyo. Kuti iwo akafike ku Mbiako amafunikira kupalasa bwato mwamphamvu, komabe nthaŵi zonse amafika pa misonkhano yachikristu. Woyang’anira woyendayenda wina anasonyeza vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses​—The Organization Behind the Name, pamene anali kuchezera kaguluka. Komatu zimenezo nzosavuta kunena koposa kuchita. Kodi nkuti kumene akanapeza lekodala ya vidiyokaseti, wailesi yakanema, ndi magetsi ake oyendetsera kumudzi wakutali ngati umenewo?

Mkati mwa mlungu wa kuchezetsawo, ofalitsa ena anafikira pasitala wina wa tchalitchi chakomweko. Anadabwa pamene pasitalayo anawalandira ndi manja aŵiri, ndipo anakambitsirana naye Baibulo mosangalatsa kwambiri. Atadziŵa kuti pasitalayo sanali ndi VCR yokha komanso jeneletala ya magetsi, abalewo analimbika mtima kumpempha ngati akhoza kuwabwereka ziŵiyazo. Pokhala atasangalala ndi makambitsirano a Baibulo, pasitalayo anavomera kuwathandiza. Pa Loŵeruka madzulo anthu 102 anafika kudzaona, kuphatikizapo pasitalayo ndi mamembala ochuluka a tchalitchi chake. Mboni ziŵiri zimenezo za ku Yoyo zinafika ndi okondwerera ambiri m’mabwato aŵiri. Kupalasa bwato molimbana ndi madzi omawonjezereka sanakuone kukhala kovuta kwambiri. Ataonerera vidiyo imeneyo, anakhudzidwa mtima kwambiri ndi kulimbikitsidwa, ndipo anali onyadira kukhala a m’gulu lalikulu limenelo limene cholinga chake ndicho kulemekeza Yehova.

Kuti munthu afike kumene mabwato sangathe kufika, afunikira kukwera matola akumidzi. Malo amene matola ameneŵa amaimikidwako poyembekezera okwera amakhala apiringupiringu ndi anthu nthaŵi zonse. Nkosavuta kusokonezeka kwambiri pamene muli pakati pa ogulitsa madzi akumwa ozizira, ogulitsa nthochi, ndi anyamata okweza akatundu pa basi. Ntchito ya anyamata okweza akatundu pa basiwo ndiyo kuloŵetsa anthu m’matola oyembekezera, amene, malinga ndi kunena kwawo, amati onsewo ‘atsala pang’ono kunyamuka.’ Komabe, ‘kutsala pang’ono’ kumeneko simuyenera kukukhulupirira kwenikweni. Apaulendo amathera maola ambiri, nthaŵi zina masiku amene, akumayembekezera. Pamene okwera onse akhala mopanikizana mkati ndipo woyendetsa atatha kupachira katundu, matumba a dzinthu, ndipo nthaŵi zina ngakhale nkhuku ndi mbuzi zamoyo, pakaliyala yapamwamba, matolawo amayenda m’tinjira tamabampu ndi tafumbi.

Mtumiki wina woyendayenda, atatopa ndi mtundu umenewu wa zoyendera, anasankha kukhala woyenda yekha momasuka. Tsopano iyeyo amayenda maulendo ake onse pa njinga. Akunena kuti: “Chiyambire pamene ndinasankha kugwiritsira ntchito njinga kuyenda ulendo wa ku mipingo yosiyanasiyana, nthaŵi zonse ndimafika panthaŵi yake kudzachezetsa. Zoonadi, ulendowo ungatenge maola angapo, komano sindimatofunikira kuthera tsiku lonse kapena masiku aŵiri ndikumayembekezera matola akumidzi. M’nyengo ya mvula, misewu ina imatsala pang’ono kuzimiririka chifukwa cha kusefukira kwa madzi. Mufunikira kuvula nsapato kuti mudutse matope ndi madzi ameneŵa. Tsiku lina nsapato yanga imodzi inagwera mu mfuleni ndipo sindinaipeze kufikira patapita milungu ingapo, pamene mwamwaŵi mwana wamkazi wa Mboni ina anaigwira mwangozi pamene anali kuŵedza nsomba! Ndili ndi chimwemwe kuvalanso nsapato zimenezi, pambuyo pakuti imodzi yathera nthaŵi ina ndi nsomba m’madzi. Nthaŵi zina ndimadutsa m’madera amene Mboni za Yehova sizinayambe zalalikiramo. Nthaŵi zonse nzika za m’midzi imeneyo zimandifunsa zimene ndawatengera. Chotero ndimakhala ndi magazini ndi mabrosha pafupi. Nthaŵi iliyonse pamene ndiima, ndimagaŵira zofalitsa zimenezi zozikidwa pa Baibulo ndi kupereka umboni wachidule. Ndikhulupirira kuti Yehova adzakulitsa mbewu zimenezi za choonadi.”

Kuloŵa Mkatikati

Mboni za Yehova zimayesayesa kuuza ena uthenga wabwino wa Ufumu ngakhale mkati mwenimweni mwa Cameroon, m’midzi yobisika mkati mwa nkhalango. Zimenezi zimafuna kuyesayesa kwakukulu, koma zipatso zake nzosangalatsa mtima.

Marie, mtumiki wa nthaŵi zonse, anayamba kuphunzira Baibulo ndi msungwana wina wotchedwa Arlette. Pamapeto a phunziro loyamba, Marie anapempha Arlette ngati angakonde kumperekeza, popeza kuti ku mbali imeneyi ya Afirika umenewu ndiwo mwambo wake. Komabe, msungwanayo analongosola kuti sankatha kuyenda chifukwa cha kupweteka kwa mapazi ake. Mapazi a Arlette anayambukiridwa ndi mtundu wina wa nthata zimene zazikazi zake zimabisala mu mnofu, zikumachititsa zithupsa. Marie anapsinya nthatazo imodziimodzi molimba mtima. Pambuyo pake, anafikiranso pa kuzindikira kuti msungwanayu anali kuzunzidwa ndi ziŵanda usiku. Marie anafotokoza mofatsa za mmene munthu angaikire chidaliro chake mwa Yehova, ndiko kuti mwa kuitana dzina lake momveka m’pemphero.​—Miyambo 18:10.

Arlette anapita patsogolo mofulumira. Poyamba a m’banja lake sanaone choipa chilichonse ndi phunzirolo chifukwa cha kupita patsogolo kumene anali kupanga ponse paŵiri mwakuthupi ndi mwamaganizo. Koma pamene anazindikira kuti anafuna kukhala mmodzi wa Mboni za Yehova, anamkaniza kupitiriza phunzirolo. Patapita masabata atatu amayi ake a Arlette, pozindikira mmene mwana wawo anavutikira maganizo, anaonana ndi Marie nampempha kupitiriza kuphunzira naye.

Pamene nthaŵi yopita ku msonkhano wadera inafika, Marie analipirira Arlette ndalama kwa woyendetsa takisii kumnyamula pa masiku onse aŵiri. Komabe, woyendetsayo anakana kupita kunyumba kwa Arlette, ataona kuti njira yake yomka ku msewu inali yovuta kudzeramo. Chotero Marie anabweretsa msungwanayo kumsewu. Yehova anadalitsadi zoyesayesa zimenezi. Lerolino Arlette amafika pamisonkhano yonse ya mpingo. Kuti amthandize kuchita zimenezi, Marie amafika kudzamtenga mosatopa. Amayendera limodzi ulendo wa mphindi 75 kupita kokha. Popeza kuti msonkhano wa pa Lamlungu umayamba pa 8:30 a.m., Marie amafunikira kunyamuka kwawo pa 6:30; komabe amatha kufika pa nthaŵi yake. Arlette akuyembekezera kusonyeza kudzipatulira kwake ndi ubatizo wa m’madzi posachedwa. Marie akunena kuti: “Munthu amene sanamuone pamene anayamba kuphunzira sangakhulupirire mmene wasinthira. Ndikuthokoza kwambiri Yehova chifukwa cha mmene wamdalitsira.” Marie alidi chitsanzo chabwino kwambiri cha munthu wosonyeza chikondi chodzimana.

Kumka cha Kumtunda Kumpoto

Kumpoto kwa Cameroon kuli zinthu zambiri zosiyanasiyana zokondweretsa. M’nyengo ya mvula, kumasintha kukhala malo a udzu wambiri wobiriŵira. Koma pamene dzuŵa loŵaula lifika, udzuwo umafota. Pamene dzuŵa lili pakati, ndipo pamene kuli kovuta kupeza mthunzi, nkhosa zimadzipanikiza m’mbali mwa nyumba za dothi la katondo. Pakati pa mchenga ndi udzu wouma, zinthu zobiriŵira zokha zimene zimatsalira ndizo masamba ochepa a mitengo ya mulambe. Ngakhale kuti imeneyi sili yaikulu mofanana ndi inzake ya mu nkhalango ya equator, iyo njofanana nayo kulimba. Kukhoza kwawo kukhalabe m’malo ovuta kukusonyeza bwino lomwe changu ndi kulimba mtima kwa Mboni zimene zapita kukakhala m’chigawo chimenechi kuti ziŵalitse kuunika kwa choonadi.

Mipingo ina m’derali yalekanitsidwa ndi makilomita 500 mpaka 800, ndipo amamvadi kukhala ali okhaokha. Koma kuli anthu ambiri okhala ndi chidwi. Mboni za m’madera ena zimasamukira kuno kudzathandiza. Kuti akhale ogwira mtima mu utumiki, amafunikira kuphunzira Chifoufouldé, chinenero cha kuno.

Mboni ina ya ku Garoua inasankha zokathera masiku angapo ikulalikira m’mudzi wakwawo, wa pamtunda wa pafupifupi makilomita 160. Anapeza okondwerera, komano kukwera mtengo kwa zoyendera kunamletsa kubwererako mokhazikika. Pambuyo pa masabata angapo, Mboniyo inalandira kalata kuchokera kwa mmodzi wa okondwerera yompempha kuti apite kukacheza nawonso. Koma chifukwa cha kusoŵabe ndalama zokwerera, sanathe kupita. Tangoganizani mmene Mboniyo inadabwira pamene munthu wina anafika panyumba pake ku Garoua kuzamdziŵitsa kuti anthu khumi m’mudziwo anali kumuyembekezera kufika!

M’mudzi wina, pafupi ndi malire a Chad, gulu lina la anthu 50 okondwerera linalinganiza phunziro lawo la Baibulo. Analinganiza kuti atatu m’gulu lawolo azifika pa misonkhano ya mpingo umene ali nawo pafupi mu Chad. Motero, pamene ameneŵa abwerera azichita phunziro la Baibulo ndi gulu lonselo. Ndithudi, mawu a Yesu atha kugwira ntchito pamenepa: “Zotuta zichulukadi koma antchito ali oŵerengeka. Chifukwa chake pempherani Mwini zotuta kuti akokose antchito kukututa kwake.”​—Mateyu 9:37, 38.

Kuchitira Umboni m’Mizinda

Pambuyo pa zaka zambiri za kusoŵa, pafupifupi zaka ziŵiri zapitazo, magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! anayamba kupezeka mosavuta mu Cameroon. Anthu ambiri akukondwera kwambiri ndi magazini ameneŵa pamene akuwaŵerenga kwa nthaŵi yoyamba. Apainiya apadera aŵiri ena achichepere okwatirana amene atumizidwa ku umodzi wa mizindayi anagaŵira magazini 86 mmaŵa wawo woyamba wa kulalikira m’gawo lawo latsopano. Ofalitsa ena amagaŵira magazini ofikira pa 250 m’mwezi umodzi! Kodi chinsinsi cha chipambano chawo nchiyani? Sonyezani magazini kwa aliyense.

Mboni ina imene imagwira ntchito mu ofesi imene mumafika anthu ambiri nthaŵi zonse imasiya magaziniwo poyera. Mkazi wina anayang’ana magaziniwo komano sanatenge alionse. Mboniyo inazindikira za chidwi cha mkaziyo nimpatsa kope, limene mkaziyo analandira. Mboniyo inadabwa kuona mkaziyo akufikanso tsiku lotsatira. Mkaziyo sanangofuna kupereka chopereka cha magazini amene anatenga komanso anapempha owonjezereka. Chifukwa? Pokhala atagwiriridwa chigololo, anasankha magazini a nkhani imeneyo. Anali atathera usiku wonse akumaŵerenga mobwerezabwereza uphungu wake umene unaperekedwamo. Pokhala atatonthozedwa kwambiri, anafuna kudziŵa zambiri ponena za Mboni za Yehova.

Ngakhale ana aang’ono angakhale ndi phande m’kuwanditsa uthenga wa Baibulo wa chiyembekezo. Pamene msungwana wina wa Mboni wa zaka zisanu ndi chimodzi anapemphedwa ndi mphunzitsi wake kuimba nyimbo yachikatolika, anakana, akumafotokoza kuti anali mmodzi wa Mboni za Yehova. Ndiyeno mphunzitsiyo anampempha kuimba nyimbo ina ya chipembedzo chake kuti adziŵe giredi imene angampatse. Anasankha nyimbo yakuti “Lonjezo la Mulungu la Paradaiso” ndi kuiimba pamtima. Mphunzitsiyo anamfunsa kuti: “M’nyimbo yakoyi watchulamo za paradaiso. Kodi paradaiso ameneyu alikuti?” Msungwanayo anafotokoza za chifuno cha Mulungu cha kukhazikitsa Paradaiso padziko lapansi posachedwa. Atadabwa ndi yankho lake, mphunzitsiyo anapempha makolo ake buku limene msungwanayo anali kuphunzira. Anafunitsitsa kuona giredi imene angampatse pa zimenezi m’malo mwa zimene anali kuphunzitsidwa m’maphunziro a chipembedzo. Makolowo anapereka lingaliro kwa mphunzitsiyo lakuti ngati anafuna kupatsa msungwanayo giredi molondola, choyamba mphunzitsi mwiniyo aliphunzire. Anayamba kuchita naye phunziro la Baibulo.

Kulinganiza Ulendo?

Ku mbali zambiri za dziko lerolino, anthu ngamphwayi ndi uthenga wabwino wa Ufumu. Alibe chidwi ndi Mulungu kapenanso ndi Baibulo. Ena amagwidwa ndi mantha aakulu ndipo amangokana kumvetsera kwa mlendo aliyense pa khomo. Zonsezi ndi vuto lenileni kwa Mboni za Yehova mu utumiki wawo. Komatu zimenezi nzosiyana chotani nanga ku Cameroon!

Kunoko kulalikira kukhomo ndi khomo nkosangalatsa. M’malo mwa kugogoda, ndi mwambo wake kunena kuti, “Kong, kong, kong.” Ndiyeno a m’nyumba amavomera kuti, “Ndani?” ndipo timadzidziŵikitsa kuti ndife Mboni za Yehova. Kaŵirikaŵiri, makolo amatuma ana awo kukatenga mabenchi ndi kuwaika pamthunzi wa mtengo, mwinamwake mtengo wamango. Ndiyeno mumathera nthaŵi yosangalatsa mukumafotokoza chimene Ufumu wa Mulungu uli ndi zimene udzachita kuchotsera anthu mkhalidwe wachisoni.

Pomvetsera makambitsirano oterowo, mkazi wina anaulula zakukhosi, akumati: “Ndikuvutika mtima poona kuti choonadi chimene ndakhala ndikufunafuna sichipezeka m’chipembedzo chimene ndinabadwiramo ndi mmene ndakalambiramo. Ndikuthokoza Mulungu kuti wandionetsa choonadi. Ndinali dikoni m’tchalitchi mwanga. Fano la Namwali Mariya limathera mlungu umodzi m’nyumba ya dikoni aliyense kuti aliyense wa iwo apereke pempho lake kwa iye. Ponena za ine, nthaŵi zonse ndinkapempha Mariya kundithandiza kudziŵa choonadi. Tsopano Mulungu wandisonyeza kuti choonadi chimenecho sichili kwa iye. Ndikuthokoza Yehova.”

Chotero ngati tsiku lina mudzafuna kupeza chimwemwe chachikulu chimene chingapezedwe m’kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu, bwanji osadzapita kukaona mbali imeneyi ya West Africa? Kuwonjezera pa kutulukira “chosonyezera Afirika chaching’ono,” kaya ndi bwato, matola akumidzi, kapena njinga, mudzakhalanso mukuchirikiza “mulu wa mboni” umene ukuwonjezereka m’dziko la “Phiri la Mulungu.”

[Mawu a M’munsi]

a “Mulu wa Mboni” mwina ndiwo mawu otanthauza liwu lachihebri lakuti “Gileadi.” Chiyambire 1943, Sukulu ya Watchtower ya Baibulo ya Gileadi yakhala ikutumiza amishonale kukayambitsa ntchito yolalikira padziko lonse, kuphatikizapo ku Cameroon.

[Mawu a Chithunzi patsamba 22]

Mapu: Mountain High Maps® Copyright © 1995 Digital Wisdom, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena