“Mphatso Yodabwitsa Yochokera kwa Yehova”
KOPE la Nsanja ya Olonda ya May 1, 1996, linali ndi nkhani yofotokoza momvekera bwino uchete wachikristu ndi mmene tingalinganizire mathayo athu kwa Yehova ndi kwa “Kaisara.” (Mateyu 22:21) Tamva mawu ambiri oyamikira chidziŵitso chatsopanocho chimene chinaperekedwa. Pakati pa iwo pali kalata yotsatirayi, yolembedwa ndi Mboni mu Greece ndipo inalembera Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova:
“Ndikufuna kukuthokozani kwambiri nonsenu abale okondedwa kaamba ka kutisamalira bwino motere mwauzimu. Pokhala nditathera zaka zisanu ndi zinayi m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro changa chachikristu, ndithudi ndikuyamikira malingaliro odabwitsa amenewo a m’kope la Nsanja ya Olonda ya May 1, 1996. (Yesaya 2:4) Iyi inali mphatso yodabwitsa yochokera kwa Yehova.—Yakobo 1:17.
“Mmene ndimasangalala ndi nkhani zimenezi, ndinakumbukira ndemanga inayake mu Nsanja ya Olonda yapapitapo (August 1, 1994, tsamba 14): ‘Mwachionekere, kulolera kuli mkhalidwe wamtengo wapatali, umene umatisonkhezera kukonda Yehova koposerapo.’ Inde, abale, ndikuthokoza Yehova kuti ndili mbali ya gulu lake lachikondi ndi lachifundo, limene limasonyeza nzeru yake moonekera bwino.—Yakobo 3:17.
“Kuwala kowonjezereka mu Nsanja ya Olonda ya May 1 kwalandiridwa ndi manja aŵiri muno mu Greece, makamaka ndi aja amene anathera zaka zingapo m’ndende kapena amene adakali m’ndende chifukwa cha chikhulupiriro chawo. Ndikukuthokozani kachiŵirinso. Yehova akulimbikitsenitu ndi mzimu wake kuti mupitirize kutipatsa chakudya chauzimu chofunika m’nthaŵi zovuta zino.”