Mamiliyoni Akupita Nanga Inuyo Simupita?
Kupita kuti? Kuchikumbutso cha pachaka cha imfa ya Yesu Kristu. Mu 1996 anthu 12,921,933 padziko lonse anapezekapo.
Nchifukwa ninji anthu amapitako? Chifukwa cha tanthauzo la imfa ya Yesu kwa mtundu wa anthu. Imatanthauza kumasuka ku matenda, kuvutika, ndi imfa. Ngakhale okondedwa akufa adzaukitsidwa kukhala ndi moyo padziko lapansi lobwezeretsedwa kukhala Paradaiso.
Kodi imfa ya Yesu Kristu idzadzetsa motani madalitso ameneŵa? Tikukupemphani kuti mufufuze. Mboni za Yehova zikukuitanani kuti mukasonkhane nazo pachochitika chofunika chimenechi.
Pitani pa Nyumba ya Ufumu yapafupi kwambiri ndi nyumba yanu. Chaka chino deti lake ndi March 23, pa Sande dzuŵa litaloŵa. Funsani Mboni za Yehova zakwanuko kuti zikuuzeni nthaŵi yake yeniyeni.