Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 4/1 tsamba 3-4
  • Kodi Nchifukwa Ninji Nthaŵi Zino Zili Zoipa Kwambiri?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Nchifukwa Ninji Nthaŵi Zino Zili Zoipa Kwambiri?
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Nkhani Yofanana
  • Funso Lachitatu: N’chifukwa Chiyani Mulungu Amalola Kuti Ndizivutika?
    Nsanja ya Olonda—2012
  • Kodi Nchifukwa Ninji Anthu Abwino Amavutika?
    Nsanja ya Olonda—1992
  • Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
    Kodi Mulungu Amatisamaliradi?
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2017
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 4/1 tsamba 3-4

Kodi Nchifukwa Ninji Nthaŵi Zino Zili Zoipa Kwambiri?

PAMENE mukhala pansi kuti muŵerenge nyuzipepala kapena kuonerera TV kaya kumvetsera nkhani za pawailesi, mumayembekezera kumvapo nkhani zachisoni, sichoncho? Mwinamwake simudabwa kumva kuti nkhondo yomwe ikuchitika ikupitirizabe, kuti chiwawa choopsa chilipobe, kapena kuti njala idakali kuwonongabe mphamvu za dziko lomatukuka kumene.

Ngati mumakhala kutali ndi komwe izi zikuchitikira, mwinamwake simuchita kunyanya kuipidwa ndi malipoti otereŵa. Ndi iko komwe, ndani angamve chisoni ndi mmene anthu ambirimbiriwo akuvutikira? Komabe, nkovuta kuti tikhale osatekeseka ngati tiona kapena kumva mmene mavuto amakhudzira anthu mmodzi ndi mmodzi. M’mawu ena, kuŵerenga za nkhondo ndi kulingalira za chiŵerengero cha ovulala nkosiyana ndi kuŵerenga za Adnan wamng’ono, mnyamata wazaka zisanu ndi zinayi wa ku Bosnia yemwe amayi ake anaphedwa pomwe bomba linawononga nyumba yawo. Atate ake a Adnan anawomberedwa ndi kufa mwezi umodzi chabe pambuyo pake pamene anali kuyenda limodzi mkhwalala. Mlongo wake anakha mwazi mpaka kufa iye akuona milungu ingapo chabe pambuyo pake, atavulazidwa ndi bomba pa bwalo la sukulu. Madokotala omwe ankathandiza Adnan pa kupsinjika maganizo anapeza kuti mnyamatayo anali wakufa mtima, wosakhudzidwa mtima ndi kalikonse​—wosafunanso kudziŵa kalikonse. Pamene anali maso, mantha ndi kukumbukira zakale kumamvuta, maloto oipa anamusoŵetsa tulo usiku. Adnan siwoŵerenga chabe m’nkhani. Ndi mwana wovutika; ndipo amamvetsa chisoni.

Nzoteronso ndi mavuto ena a dziko. Kuŵerenga za njala nkosiyana kwambiri ndi kuona chithunzi cha mtsikana wa zaka zisanu wa mimba yofufuma ndi timiyendo towonda, wokanthidwa ndi njala. Nkosiyana kwambiri kuŵerenga za chiwawa ndi kumva za mkazi wamasiye wachikulire womenyedwa mwankhanza, kulandidwa, ndi kuchitidwa mizambi. Kumva za kusweka kwa banja nkosiyana kwambiri ndi kumva za nakubala amene mwadala anazunza mwana wake mwakummana chakudya ndi kumchitira zosayenera mwankhanza.

Nzopweteka mtima kuŵerenga zoterezi. Koma nzoipirapo chotani nanga ngati wina wa miliri ya dziko imeneyi ugwera ife mwachindunji! Ngati inuyo mwavutika, zochitika za dziko lonsezi zomvedwa m’lipoti la dziko lonse zingakhale zoŵaŵirapo. Nzoopsa kuona kuti kuvutika ndi upandu, nkhondo, njala, ndi matenda zikuwonjezereka pamlingo waukulu kuposa ndi kalelonse m’mbiri ya anthu. Zotsatira pa kulimbana ndi zovuta za m’zaka za zana lino la 20 nzovuta ndithu​—kuthedwa nzeru, mantha, ndi kupsinjika maganizo nzofala.

Anthu a zipembedzo zambiri akufunafuna mayankho a mafunso ovuta monga akuti, Nchifukwa ninji zinthu zili zovuta chonchi? Kodi mtundu wa anthu ukuloŵera kuti?

Zachisoni, lero ndi mwakamodzikamodzi kuti zipembedzo zipereke mayankho okhutiritsa. Pamene munaona funso pa chikuto cha magazini ino, mwinamwake munakayikira​—nzomveka ndithu. Zipembedzo zosunga mwambo kaŵirikaŵiri zimayesa kunena zomwe m’Baibulo mulibe​—tsiku ndi ola lenileni la mathedwe a dziko. (Onani Mateyu 24:36.) Ofalitsa a magazini ino amafuna kuti Baibulo linene lokha. Mungakhale odabwa kuona kuti malongosoledwe a Baibulo a masiku otsiriza ali oona ndi anzeru. Ndipo Baibulo silingonena chifukwa chake zinthu zaipa. Limaperekanso chiyembekezo chamtsogolo, chomwe nchotonthoza kwenikweni. Tikukupemphani kulingalira nkhani zotsatira kuti muone ndi motani m’mene izi zili.

[Mawu a Chithunzi patsamba 3]

Jobard/​Sipa Press

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena