Kodi Mungakhulupirire mwa Mulungu wa Umunthu Wake?
“SUYENERA kukhulupirira Mulungu kuti ukhale Mkristu . . . Ndife amodzi a osintha zinthu tsopano, koma m’zaka za zana la 21 tchalitchi sichidzakhalanso ndi Mulungu monga mwa mwambo wake,” anatero mtsogoleri wa chipembedzo wamkulu wa pa yunivesite ku Britain. Ankalankhulira gulu la Sea of Faith limene ansembe achibritishi pafupifupi zana limodzi amachirikiza. “Okana Mulungu achikristu” ameneŵa amati chipembedzo chinayambitsidwa ndi anthu ndi kuti, monga momwe membala wina ananenera, Mulungu ndi “ganizo chabe.” Iwo samaganiziranso zakuti kuli Mulungu wosaoneka.
“Mulungu ngwakufa” anali mawu otchuka m’ma 1960. Ankasonyeza maganizo a wafilosofi wachijeremani Friendrich Nietzsche wa m’zaka za zana la 19 ndipo anapatsa achinyamata ambiri chodzikhululukira chomwe ankafuna kuti azichita zokonda zawo, anyamata ndi asungwana kumakhala malo amodzi popanda ukwati, kugwiritsira ntchito mankhwala osokoneza bongo mosaopa mwambo uliwonse. Koma kodi ufulu umenewu unatsogolera anyamata otsogola ameneŵa, monga momwe amadziŵikira, kukhala ndi moyo wachimwemwe wokhutiritsa kwambiri?
M’zaka zomwezo, bishopu wa Anglican John A. T. Robinson anafalitsa buku loyambitsa mkangano lotchedwa Honest to God. Atsogoleri achipembedzo anzake ambiri anamdzudzula chifukwa cholingalira kuti Mulungu “ali chabe malingaliro obwera chifukwa cha zinthu zosiyanasiyana zimene anthu aona.” Profesa wa maphunziro a zaumulungu Keith Ward anafunsa kuti: “Kodi chikhulupiriro mwa Mulungu ndi mwambo chabe wachikale, umene tsopano anzeru ausiya?” Poyankha funso lake lomwe, anati: “Palibe chinthu chofunika kwambiri m’zipembedzo lerolino choposa kufufuzanso chidziŵitso chonena za Mulungu monga momwe chinalili kale.”
Kugwirizanitsa Kuvutika ndi Mulungu wa Umunthu Wake
Ambiri omwe amakhulupirira mwa Mulungu wa umunthu wake zimawavuta kugwirizanitsa pakati pa chikhulupiriro chawo ndi masoka ndiponso mavuto amene amaona. Mwachitsanzo, m’March 1996, ana aang’ono 16, pamodzi ndi mphunzitsi wawo, anaomberedwa ndi kuphedwa ku Dunblane, Scotland. “Sindingathe kumvetsetsa cholinga cha Mulungu,” anatero mayi wina atathedwa nzeru. Chisoni chimene tsokali linabweretsa chinalembedwa pakhadi lokhala ndi maluŵa panja pa sukulu ya anawo. Linali ndi mawu akuti, “NCHIFUKWA NINJI?” Poyankha, wansembe wa ku Cathedral ya Dunblane anati: “Sizingatheke kulongosola. Sitingathe kuyankha kuti nchifukwa ninji zoterezi zachitika.”
Pambuyo pake chaka chomwecho, mtsogoleri wotchuka wachinyamata wa Church of England anaphedwa mwa nkhanza. Church Times inalengeza kuti mpingo wogwidwa chisoniwo unamva dikoni wamkulu wa ku Liverpool akunena za “kugogoda pa chitseko cha Mulungu ndi mafunso akuti nchifukwa ninji? nchifukwa ninji?” Mtsogoleri wachipembedzo ameneyu nayenso analibe mawu otonthoza ochokera kwa Mulungu wa umunthu wake.
Nchiyani nanga chomwe tiyenera kukhulupirira? Nkwanzeru kukhulupirira mwa Mulungu wa umunthu wake. Ndiyo kiyi yoyankhira mafunso ovuta amene afunsidwa pamwambawo. Tikupemphani kupenda umboni wolembedwa m’nkhani yotsatira.
[Chithunzi patsamba 3]
Khadilo linafunsa kuti “Nchifukwa Ninji?”
[Mawu a Chithunzi]
NEWSTEAM No. 278468/Sipa Press