Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w97 11/15 tsamba 5-7
  • Dziko Lolungama Siloto!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko Lolungama Siloto!
  • Nsanja ya Olonda—1997
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Nchifukwa Ninji Munthu Walephera?
  • Dziko Lolungama Lidzakhalapodi​—Motani?
  • Moyo wa m’Dziko Lolungama
  • Yehova Amakonda Chilungamo
    Nsanja ya Olonda—2007
  • Kodi Zinthu Zopanda Chilungamo Zidzatha Padzikoli?
    Nkhani Zina
  • Kodi Mulungu Adzachitapodi Kanthu Ponena za Chisalungamo?
    Nsanja ya Olonda—1989
  • “Kodi Mulungu Alibe Chilungamo?”
    Yandikirani Yehova
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1997
w97 11/15 tsamba 5-7

Dziko Lolungama Siloto!

“CHILUNGAMO ndicho chinthu chimene munthu amachifunitsitsa padziko lapansi,” anatero Daniel Webster, wodziŵa bwino za kayendetsedwe ka boma wa ku America. Ndipo Baibulo limati: “Yehova akonda chilungamo.” (Salmo 37:28, NW) Pokhala atapangidwa m’chifanizo cha Mulungu, mwamuna ndi mkazi oyambawo anali ndi mikhalidwe yaumulungu, kuphatikizapo kutsata chilungamo.​—Genesis 1:26, 27.

Malemba amafotokozanso za ‘anthu amitundu akukhala opanda lamulo, akuchita mwa okha za lamulo.’ Choncho iwo “aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m’mitima yawo, ndipo chikumbumtima chawo chichitiranso umboni pamodzi nawo, ndipo maganizo awo wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana.” (Aroma 2:14, 15) Inde, anthu anapatsidwa chikumbumtima​—nzeru za mkati zokhoza kuzindikira chabwino ndi choipa. Mwachionekere, munthu amafuna chilungamo mwachibadwa.

Chinthu chinanso chochititsa kufuna chilungamo ndicho chilakolako cha chimwemwe, popeza Salmo 106:3 limati: “Odala iwo amene asunga chiweruzo, iye amene achita chilungamo nthaŵi zonse.” Komabe, kodi nchifukwa ninji munthu walephera kudzetsa dziko lolungama?

Nchifukwa Ninji Munthu Walephera?

Chifukwa chachikulu chimene chalepheretsa kukhazikitsa dziko lolungama ndicho chilema chimene tinatengera kwa makolo athu oyambirira, Adamu ndi Hava. Baibulo likufotokoza kuti: “Uchimo unaloŵa m’dziko lapansi mwa munthu mmodzi, ndi imfa mwa uchimo; chotero imfa inafikira anthu onse, chifukwa kuti onse anachimwa.” (Aroma 5:12) Chilemacho ndicho uchimo. Ngakhale kuti analengedwa opanda uchimo, Adamu ndi Hava anaganiza zopandukira Mulungu ndipo chotero anadzisandutsa anthu ochimwa. (Genesis 2:16, 17; 3:1-6) Nchifukwa chake iwo anapatsira ana awo choloŵa cha malingaliro auchimo ndi oipa.

Kodi mikhalidwe imeneyi ya umunthu monga dyera ndi tsankhu siili zotsatirapo za malingaliro auchimo? Ndipo kodi mikhalidwe imeneyi sindiyo imasonkhezera kupanda chilungamo padziko lapansi? Ndithudi, dyera ndilo limayambitsa makhalidwe owononga mwadala zinthu zachilengedwe ndi kuponderezana pazachuma. Tsankhu ndilodi limachititsa kumenyana kwautundu ndi kuchitirana zoipa chifukwa cha kusiyana khungu. Mikhalidwe imeneyi imasonkhezeranso anthu kuba, kunyenga, ndi kuchita zinthu zimene zimavulaza ena.

Ngakhale kuti timayesetsa ndi zolinga zabwino kwambiri kuti tichite chilungamo ndi kuchita zabwino koma nthaŵi zambiri timalephera kutero chifukwa cha ziyambukiro zathu zauchimo. Mtumwi Paulo iye mwini anavomereza kuti: “Pakuti chabwino chimene ndichifuna, sindichichita; koma choipa chimene sindichifuna, chimenecho ndichichita.” Iye akupitiriza kufotokoza za kulimbanaku, motere: “Pakuti monga mwa munthu wa mkati mwanga, ine ndikondwera ndi chilamulo cha Mulungu: koma ndiona lamulo lina m’ziŵalo zanga, lilikulimbana ndi lamulo la mtima wanga, ndi kundigonjetsa kapolo wa lamulo la m’ziŵalo zanga.” (Aroma 7:19-23) Mofananamo, ifenso lerolino tili ndi kulimbana kumodzimodzi. Nchifukwa chake kupanda chilungamo kumachitika kaŵirikaŵiri.

Ulamuliro wa anthu wathandiziranso kudzetsa kupanda chilungamo padziko lapansi. M’dziko lililonse muli malamulo ndi anthu amene amaonetsetsa kuti malamulowo akutsatiridwa. Inde, kulinso oweruza ndi mabwalo a milandu. Zoonadi, anthu ena a mapulinsipulo abwino ayesetsa kuchirikiza ufulu wachibadwidwe wa anthu ndiponso kuonetsetsa kuti chilungamo chikuchitidwa kwa onse mofanana. Komabe, nthaŵi zambiri zoyesayesa zawo zalephera. Chifukwa ninji? Pofotokoza m’mawu achidule zifukwa zambirimbiri zimene zapangitsa kulephera kwawo, Yeremiya 10:23 akuti: “Inu Yehova, ndidziŵa kuti njira ya munthu siili mwa iye mwini; sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” Popeza kuti ngwotalikirana ndi Mulungu, munthu sangathe kukhazikitsa dziko lolungama mpang’ono pomwe.​—Miyambo 14:12; Mlaliki 8:9.

Chopinga chachikulu pa zoyesayesa za anthu za kukhazikitsa dziko lolungama ndiye Satana Mdyerekezi. Baibulo limanena momveka bwino kuti mngelo wopandukayo Satana ndiye “wambanda” ndi “wabodza” woyamba ndiponso limati “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (Yohane 8:44; 1 Yohane 5:19) Mtumwi Paulo akumutcha “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano.” (2 Akorinto 4:3, 4) Pokhala wodana ndi chilungamo, Satana amachita mulimonse mmene angathere kuti asonkhezere zoipa. Malinga ngati iye apitirizabe kulamulira dziko lapansi, kupanda chilungamo kwa mitundu yonse ndi masoka ake otsatirapo zidzasautsabe mtundu wa anthu.

Kodi zimenezi zikutanthauza kuti kupanda chilungamo sikungathetsedwe nkomwe mumtundu wa anthu? Kodi dziko lolungama silingakhalepo nkomwe?

Dziko Lolungama Lidzakhalapodi​—Motani?

Kuti dziko lolungama loyembekezeredwalo likhalepodi, mtundu wa anthu uyenera kudalira amene angathetse zinthu zimene zimayambitsa kupanda chilungamo. Koma kodi ndani amene angachotseretu uchimo ndi kuwononga Satana ndi ulamuliro wake? Mwachionekere, palibe munthu aliyense kapena bungwe lililonse la anthu limene lingakwanitse ntchito yovuta imeneyo. Yehova Mulungu yekha ndiye amene angachite zimenezo! Ponena za iye, Baibulo limati: “Thanthwe, ntchito yake ndi yangwiro; pakuti njira zake zonse ndi chiweruzo [“chilungamo,” NW]; Mulungu wokhulupirika ndi wopanda chisalungamo; iye ndiye wolungama ndi wolunjika.” (Deuteronomo 32:4) Ndipo popeza kuti “akonda chilungamo,” Yehova akufuna kuti mtundu wa anthu usangalale ndi moyo wa m’dziko lolungama.​—Salmo 37:28.

Ponena za makonzedwe a Mulungu a kudzetsa dziko lolungama, mtumwi Petro analemba kuti: “Monga mwa lonjezano lake tiyembekezera miyamba yatsopano, ndi dziko latsopano m’menemo mukhalitsa chilungamo.” (2 Petro 3:13) “Miyamba yatsopano” imeneyi si thambo lenileni latsopano ayi. Mulungu analenga thambo lathuli langwiro, ndipo limampatsa ulemerero. (Salmo 8:3; 19:1, 2) “Miyamba yatsopano” imeneyi ndiyo ulamuliro watsopano wa padziko lapansi. “Miyamba” imene ilipoyi ndiyo maboma opangidwa ndi anthu. Posachedwapa, pankhondo ya Mulungu ya Armagedo, maboma ameneŵa adzachotsedwa ndipo m’malo mwake kudzakhala “miyamba yatsopano”​—Ufumu wake wakumwamba, kapena kuti boma lake. (Chivumbulutso 16:14-16) Mfumu ya Ufumu umenewo ndiye Yesu Kristu. Popeza kuti lidzakhala litathetseratu ulamuliro wa anthu, boma limeneli lidzalamulira kosatha.​—Danieli 2:44.

Nanga “dziko latsopano” ndilo chiyani? Si pulaneti latsopano ayi, popeza kuti Mulungu analenga dziko lapansi langwiro kuti anthu akhalemo, ndipo chifuno chake nchakuti likhale kosatha. (Salmo 104:5) “Dziko latsopano” limeneli likutanthauza anthu ena atsopano. (Genesis 11:1; Salmo 96:1) “Dziko” limene lidzawonongedwa ndiwo anthu amene amadzipanga kukhala mbali ya dongosolo loipa la zinthu lilipoli. (2 Petro 3:7) “Dziko latsopano” limene lidzaloŵa m’malo mwake ndiwo atumiki oona a Mulungu, amene amadana ndi zoipa ndiponso amene amakonda makhalidwe abwino ndi chilungamo. (Salmo 37:10, 11) Choncho, dziko la Satana lidzatha psiti.

Koma kodi Satana chidzamchitikira nchiyani? Mtumwi Yohane analosera kuti: “[Kristu Yesu] anagwira chinjoka, njoka yakaleyo, ndiye Mdyerekezi ndi Satana, nammanga iye zaka chikwi, namponya kuphompho, natsekapo, nasindikizapo chizindikiro pamwamba pake, kuti asanyengenso amitundu.” (Chivumbulutso 20:1-3) Satana womangidwa ndi unyoloyo sadzakhalanso ndi chisonkhezero chilichonse mongadi wandende yapansi yamdima. Chidzakhala chimasuko chotani nanga ku mtundu wa anthu, chimene chidzakhala monga kalambulebwalo wa dziko lolungama! Ndipo pamapeto a zaka chikwizo, Satana adzasakazidwa kwakuti sadzakhalaponso.​—Chivumbulutso 20:7-10.

Komabe, kodi chidzachitika nchiyani ndi uchimo wa choloŵa? Yehova wapereka kale maziko ochotsera uchimo. ‘Mwana wa munthu [Yesu Kristu] anadza . . . kudzapereka moyo wake dipo la anthu ambiri.’ (Mateyu 20:28) Mawu akuti “dipo” amasonyeza mtengo woombolera andende. Yesu anapereka mtengo wa moyo wake wangwiro waumunthu monga dipo loombolera mtundu wa anthu.​—2 Akorinto 5:14; 1 Petro 1:18, 19.

Nsembe ya dipo ya Yesu ingatipindulitsenso ngakhale lerolino. Mwa kuikhulupirira, tingakhale oyera pamaso pa Mulungu. (Machitidwe 10:43; 1 Akorinto 6:11) Mu ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu, dipolo lidzatheketsa mtundu wa anthu kumasuka kotheratu ku uchimo. Buku lomaliza la m’Baibulo limafotokoza mophiphiritsira za “mtsinje wa madzi a moyo” wotuluka kumpando wachifumu wa Mulungu, ndipo m’gombe lake muli mitengo yobala zipatso yokhala ndi masamba “akuchiritsira nawo amitundu.” (Chivumbulutso 22:1, 2) Zimene Baibulo likusonyeza pano zimaimira makonzedwe osangalatsa kwambiri a Mlengi a kuthetsa uchimo wa mtundu wa anthu pamaziko a nsembe ya dipo ya Yesu. Makonzedwe ameneŵa adzagwiradi ntchito yake bwino lomwe pamene adzamasula kotheratu anthu omvera ku uchimo ndi imfa.

Moyo wa m’Dziko Lolungama

Talingalirani za mmene moyo udzakhalira mu ulamuliro wa Ufumuwo. Upandu ndi chiwawa zidzakhala zinthu zakale. (Miyambo 2:21, 22) Kupanda chilungamo pazamalonda kudzatheratu. (Salmo 37:6; 72:12, 13; Yesaya 65:21-23) Mikhalidwe yonse yosankhana pamakhalidwe, chifukwa cha kusiyana khungu, mitundu, ndi mafuko idzafafanizidwa. (Machitidwe 10:34, 35) Nkhondo ndi zida zankhondo sizidzakhalaponso. (Salmo 46:9) Akufa miyandamiyanda adzawabwezeretsa ku moyo wa m’dziko lopanda chisalungamo. (Machitidwe 24:15) Aliyense adzasangalala ndi umoyo wangwiro ndi wathanzi. (Yobu 33:25; Chivumbulutso 21:3, 4) Baibulo likutitsimikizira kuti: “[Yesu Kristu] adzatulutsa chiweruzo [“chilungamo,” NW] m’zoona.”​—Yesaya 42:3.

Pakali pano, tingayang’anizane ndi kupanda chilungamo, koma tiyenitu tipeŵe kukhalanso opanda chilungamo. (Mika 6:8) Ngakhale pamene tikupirira chifukwa cha kuyang’anizana ndi kupanda chilungamo, tipitirizetu kukhala achidaliro. Dziko lolungama lolonjezedwalo lidzafikadi posachedwapa. (2 Timoteo 3:1-5; 2 Petro 3:11-13) Mulungu Wamphamvuyonse wapereka mawu ake, ndipo ‘adzachita chimene afuna.’ (Yesaya 55:10, 11) Ino ndiyo nthaŵi yokonzekera kudzakhala m’dziko lolungama limenelo mwa kuphunzira zimene Mulungu amafuna kwa ife.​—Yohane 17:3; 2 Timoteo 3:16, 17.

[Chithunzi patsamba 7]

Mikhalidwe yonse ya kupanda chilungamo idzathetsedwa m’dziko latsopano la Mulungu lolonjezedwalo

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena