Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 2/15 tsamba 32
  • Kodi Mulungu Adzawononga Dziko?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mulungu Adzawononga Dziko?
  • Nsanja ya Olonda—1998
Nsanja ya Olonda—1998
w98 2/15 tsamba 32

Kodi Mulungu Adzawononga Dziko?

MOGWIRIZANA ndi zimene ananena Papa John Paul II, anthu angayang’ane mtsogolo ndi chidaliro. Iye anati, m’mbiri yonse ya anthu, “anthu akhala akuchimwa, mwinamwake machimo akulu kupambana amene anthu anachita chigumula chisanafike.” Ngakhale ndi choncho, papayo anati, “mwa mawu apangano limene Mulungu anapanga ndi Nowa timazindikira kuti palibe tchimo limene lingapangitse Mulungu kuwononga dziko limene iye mwini analenga.”

Kodi ndi zoona kuti Mulungu sadzawononga dzikoli? Baibulo limati pambuyo pa Chigumula, Mulungu anati kwa Nowa: “Zamoyo zonse sizidzamalizidwanso konse ndi madzi a chigumula; ndipo sikudzakhalanso konse chigumula chakuwononga dziko lapansi.” (Genesis 9:11) Papayo anati ndi mawu amenewa, Mulungu “anadzipereka pa kutetezera dziko lapansi kukuwonongedwa.”

Baibulo limasonyeza bwino lomwe kuti Mlengi sadzalola dziko lathuli kuti liwonongedwe. “Dziko lingokhalabe masiku onse,” limatero Baibulo. (Mlaliki 1:4) Koma pali zambiri zimene tingaphunzire kuchokera ku Chigumula​—zina zimene papa sanazitchulepo.

Yesu ananena kuti mikhalidwe padziko lapansi panthaŵi ya kukhalapo kwake idzakhala “monga masiku a Nowa,” pamene anthu “sanadziŵa kanthu, kufikira kumene chigumula chinadza, chinapululutsa iwo onse.” (Mateyu 24:37-39) Mofananamo, mtumwi Petro analemba kuti monga mmene “dziko lapansi la masiku aja, pomizika ndi madzi, lidawonongeka,” chomwechonso “tsiku la chiweruzo ndi chiwonongeko cha anthu osapembedza” likuopseza dziko lamakono.​—2 Petro 3:5-7.

Kodi Yesu ndi Petro anaiŵala pangano la Mulungu ndi Nowa? Kutalitali! Monga momwe Mulungu ananenera m’pangano ndi Nowa, iye sadzagwiritsira ntchito madzi a chigumula kuti athetse dongosolo la zinthu lilipoli. M’malo mwake adzagwiritsira ntchito mphamvu za “Mfumu ya mafumu, ndi Mbuye wa ambuye,” Yesu Kristu. (Chivumbulutso 19:11-21) Motero, mogwirizana ndi zimene Baibulo limanena, dziko lapansi silidzawonongedwa, koma “dziko” la anthu oipa mosakayikira lidzatha. (Miyambo 2:21,22; Chivumbulutso 11:18) Pambuyo pake, “olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.”​—Salmo 37:29.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena