Chilango—Nchopindulitsa kwa Onse
M’MAWU a Mulungu, Baibulo, kodi mawu ogwiritsiridwa ntchito ponena za chilango amatanthauzanji? Nauni yachihebri yakuti mu·sarˈ ndiponso mtundu wina wa verebu wakuti ya·sarˈ zimatanthauza “chilango,” “kukhaulitsa,” “kuwongolera,” “chilimbikitso.” Mu Septuagint yachigiriki ndiponso m’Malemba Achigiriki Achikristu, nauni yake yakuti pai·deiˈa ndi verebu yakuti pai·deuˈo kwenikweni zili ndi matanthauzo ofananawo. Mawu akuti pai·deiˈa, otengedwa ku mawu akuti pais, otanthauza “mwana,” kwenikweni amatanthauza zimene zimafunika polera ana—chilango, malangizo, maphunziro, kuwongolera, ndi kukhaulitsa.
Kumene Chimachokera Ndiponso Cholinga Chake
Posonyeza chikondi chake, Yehova amapereka chilango kwa anthu ake. (Miyambo 3:11, 12) Iye amawapatsa malangizo amene amawongolera malingaliro olakwika ndi kuumba nzeru zawo ndi khalidwe lawo. Kwa Aisrayeli a m’nthaŵi ya Mose, chilango chinaphatikizapo kuona zisonyezero za ukulu wa Mulungu. Panali zisonyezero za mphamvu yosayerekezereka pamene Yehova anaweruza milungu yonse ya Igupto, kumasula anthu ake, ndi kuwononga gulu lankhondo la Aigupto m’Nyanja Yofiira. Kunali ziweruzo zoopsa zimene zinaperekedwa kwa Aisrayeli osamvera. Ndiponso analandira zakudya ndi madzi mozizwitsa pamodzi ndi maphunziro a kufunika kwa kumvera ndi kugwiritsira ntchito zonse zimene Yehova akunena. Chilango chonsechi chinawachititsa kukhala odzichepetsa ndipo chinakhomereza mwa iwo za kufunika kwa kuopa Yehova ndi mantha oyenera, ofunikira kusonyezedwa mwachikhulupiriro ndi kumvera.—Deuteronomo 8:3-5; 11:2-7.
Kaŵirikaŵiri chilango cha Yehova chimadza kudzera mwa oimira ake, anthu audindo oikidwapo mwalamulo. Mwisrayeli amene ananamizira mkazi wake kuti sanali namwali pomkwatira anali kulangidwa ndi akulu amene anatumikira monga oweruza. (Deuteronomo 22:13-19) Makolo amaimira Yehova pamene alanga ana awo moyenerera. Ndipo ana ayenera kuona chilango chotero monga chikondi cha makolo, cholinganizidwa kaamba ka ubwino wawo wokhalitsa. (Miyambo 1:8; 6:20-23; 22:15; 23:13, 14; Aefeso 6:4) Mumpingo wachikristu, akulu amagwiritsira ntchito Mawu a Mulungu popereka chilango—uphungu, kuwongolera, ndi kudzudzula. (2 Timoteo 3:16) Cholinga cha chilango cha Yehova choperekedwa kwa Akristu atalakwa ndicho kuwatulutsa mu uchimo umene agweramo ndi kuwatetezera kuti asalandireko chiweruzo chowatsutsa chimene chidzaperekedwa padziko losaopa Mulungu limeneli. (1 Akorinto 11:32) Monga mutu wa mpingo wachikristu, Yesu Kristu, posonyeza chikondi chake, amaonetsetsa kuti chilango choyenera chikuperekedwa.—Chivumbulutso 3:14, 19.
Chilango choŵaŵa kwambiri ndicho kuchotsedwa mumpingo. Mtumwi Paulo anachigwiritsira ntchito popereka Humenayo ndi Alesandro “kwa Satana.” (1 Timoteo 1:20) Pokhala atachotsedwa mumpingo, iwo anakhalanso mbali ya dziko lolamulidwa ndi Satana.—1 Akorinto 5:5, 11-13.
Zizunzo zimene Yehova angalole kugwera atumiki ake zingakhale chilango, kapena kuti maphunziro, amene angabale chipatso chabwino cha chilungamo, chimene munthu angasangalale nacho mumtendere chiyesocho chitatha. (Ahebri 12:4-11) Ngakhale Mwana wa Mulungu anakhala mkulu wa ansembe womvera ena chifundo chifukwa cha mavuto amene Atate ake analola kuti amgwere.—Ahebri 4:15.
Zotsatirapo za Kumvera Ndiponso za Kunyalanyaza
Anthu oipa, opusa, kapena a khalidwe lopanda pake amasonyeza kuti amada chilango cha Yehova mwa kuchikana kotheratu. (Salmo 50:16, 17; Miyambo 1:7) Zotsatirapo zoipa za kupusa kumeneku zimaitana chilango chowonjezereka, kaŵirikaŵiri kukhaulitsidwa kwadzaoneni. Monga momwe mwambi umanenera kuti: “Mwambo wa zitsiru ndi utsiru.” (Miyambo 16:22) Atha kudzidzetsera okha umphaŵi, manyazi, matenda, ngakhalenso imfa yamwadzidzidzi. Mbiri ya Aisrayeli imasonyeza kuti zinthu zambiri zingatayike. Iwo sanamvere chilango choperekedwa monga chidzudzulo ndi kuwongolera kudzera mwa aneneri. Iwo sanamvere chilango choperekedwa pamene Yehova sanawatetezere ndipo sanawadalitse. Pomalizira pake, iwo analandira chilango choŵaŵa cholengezedwa pasadakhale—kugonjetsedwa ndi kutengeredwa kuukapolo.—Yeremiya 17:23; 32:33; Hoseya 7:12-16; Zefaniya 3:2.
Mosiyana ndi zimenezo, kulandira chilango, pamodzi ndi kuopa Yehova ndi mantha oyenera, zimapangitsa munthu kukhala wanzeru, wotha kugwiritsira bwino ntchito chidziŵitso, ndipo zimenezo zimamthandiza kupeŵa kusweka maganizo ndi kuvutika. Mwa kuchilabadira, chilango cholandiridwa moyamikira chingathandizire kutalikitsa moyo wa munthu tsopano ndiponso chimapereka lonjezo la kukhala moyo kosatha mtsogolo. Choncho, moyenerera, chilango chiyenera kulemekezedwa kwambiri.—Miyambo 8:10, 33-35; 10:17.
Chilango Chimabala Zipatso Zabwino
Anthu ali ndi chikhoterero chauchimo chokonda kuipidwa ndi chidzudzulo pamodzi ndi mtumiki waumunthu amene wagwiritsiridwa ntchito kuchipereka. Koma kudzilola kukhala ndi chikhoterero chimenechi kumapangitsa munthu kukhala wofanana ndi nyama yosaganiza ndiponso yopanda khalidwe; monga momwe mwambi wouziridwa umanenera kuti: “Wakuda chidzudzulo apulukira.” (Miyambo 12:1) Mosiyana ndi zimenezo, wamasalmo Davide, amene anadzudzulidwa mobwerezabwereza iyemwini, analemba kuti: “Akandipanda munthu wolungama ndidzati nchifundo: akandidzudzula, ndidzakuyesa mafuta a pamutu; mutu wanga usakane.”—Salmo 141:5.
Monga momwe taonera, tonsefe tifunikira chilango. Nchofunika kwa amuna ndi akazi, achinyamata ndi achikulire, amene akhala m’choonadi kwa nthaŵi yaitali ndiponso atsopano. Choncho, tiyenera kuyembekezera kulandira chilango, ngakhale kuchifunafuna. Phunzirani Mawu a Mulungu ndi kuona zimene amanena zimene zingakhale uphungu kwa inu. (2 Timoteo 3:16, 17) Pezekani pamisonkhano ndipo mvetserani mosamala kuti muone zimene zikukhudza inuyo. (Ahebri 10:24, 25) Ngati chilango chachikondi cha m’Malemba chaperekedwa kwa inu mwachindunji, chilandireni ndi mtima wonse m’njira imene chaperekedwera. Gwiritsirani ntchito maphunziro alionse owongolera amene amachokera kwa Yehova.
Paulo anauza Ahebri kuti: “Chilango chilichonse, pakuchitika, sichimveka chokondwetsa, komatu choŵaŵa; koma chitatha, chipereka chipatso cha mtendere, kwa iwo ozoloŵeretsedwa nacho, ndicho cha chilungamo.” (Ahebri 12:11) Choncho, ngakhale kuti chilango chingatipweteketse mtima nthaŵi zina, zotsatirapo zake zimakhala zabwino. Kulandira chilango kungatipangitse kukhala pakati pa awo amene amasangalatsa Yehova. Chilango chidzatithandiza ‘kuyenda mokwanira, kuchita chilungamo, ndi kunena zoonadi mumtima mwathu.’ (Salmo 15:1, 2) Choncho, tonsefe tiyeni tizilandira chilango.