Kodi Anapanga Zonsezi Ndani?
PODUTSA m’nkhalango ina yoŵirira ku Cambodia, Henri Mouhot, Mfalansa woyendera malo wa m’zaka za zana la 19, anafika paphompho lalikulu lachemba lozungulira kachisi. Pamtunda wapafupifupi kilomita imodzi kuchokera pamene iye anaimirira, anaona nsanja zisanu za kachisiyo zotalika mamita oposa 60. Imeneyi inali Angkor Wat, chipilala chachikulu kwambiri chachipembedzo padziko lonse lapansi. Pamene Mouhot anachitumba, chinali chitakhalapo kale kwa zaka mazana asanu ndi aŵiri, koma osawonongeka ndi kusintha kosiyanasiyana kwa nyengo.
Mouhot atangochiyang’ana, anazindikira nthaŵi yomweyo kuti chimango chimenecho chokutidwa ndi ndere chinali ntchito ya manja a munthu. “Chinamangidwa ndi katswiri wina wakale lomwe wa luso ngati la Michengelo wotchukayo, ndipo nchachikulu kwambiri kuposa chimango chilichonse chomangidwa ndi Agiriki kapena Aroma,” iye analemba motero. Ngakhale kuti chinali chitasiyidwa kwa zaka mazana ambiri, iye sanakayike konse kuti chimango chodabwitsacho, chinali naye wochimanga.
Ndipotu buku lokhala ndi chidziŵitso lolembedwa zaka mazana ambiri zapitazo linagwiritsira ntchito malingaliro ofananawo pofotokoza chifukwa chake dziko lapansi tikukhalamoli lili ntchito ya Wopanga. Dzikoli liyenera kuti linalengedwa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Pakuti nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.” (Ahebri 3:4) Ena angatsutse mafotokozedwe ameneŵa, akumati: ‘Zinthu zachilengedwe nzosiyana ndi zinthu zopangidwa ndi munthu.’ Komabe, si asayansi onse amene amagwirizana ndi chitsutso chimenecho. Atavomereza kuti “zinthu zamoyo nzosiyana ndi zinthu zosapuma,” Michael Behe, wachiŵiri kwa profesa woona za madzi osiyanasiyana a m’thupi la zamoyo pa Yunivesite ya Lehigh, anafunsa kuti: “Kodi tinganene kuti zamoyo zinachita kulinganizidwa mwaluntha?” Iye anapitirizabe kufotokoza kuti asayansi tsopano akulinganiza masinthidwe ena ndi ena m’matupi a zamoyo mwa njira zotchedwa genetic engineering. Mwachionekere, zinthu zopanda moyo ndi zamoyo zomwe zingalinganizidwe ndi kupangidwa! Ponena za tinthu ting’onong’ono tosatheka kutiona ndi maso monga maselo amoyo, Behe anafotokoza za kucholoŵana kwa maselo ena opangidwa ndi mbali zina zodaliranso pa maselo ena amoyo. Kodi iye ananenanji pomalizira pake? “Chotsatirapo cha khama lonseli lofufuza selo—kufufuza moyo kuyambira pa mamolekyu—chinasonyeza bwino lomwe kuti panali ‘wopanga!’”
Ofufuza zakuthambo ndi ofufuza zachilengedwe akhala akufufuzanso mwakhama za mkhalidwe wa zachilengedwe ndi zinthu zakuthambo ndipo apeza zinthu zina zodabwitsa. Mwachitsanzo, tsopano akudziŵa kuti ngati patakhala kusintha kwakung’onong’ono pazinthu zosasintha, chilengedwe chonse sichingakhale ndi chinthu chamoyo.a Wofufuza zakuthambo, Brandon Carter, anatcha zochitika zimenezi kukhala malunji odabwitsa. Koma ngati mutapeza zinthu zodabwitsa zogwirizana zochitika mwamalunji komanso motsatira dongosolo lake, kodi simungalingalire kuti panali wina amene anazipanga?
Ndithudi, ‘zinthu za mipangidwe yocholoŵana ndi zochitika mwamalunji’ ndiponso zolinganizidwa bwino zimenezi zili naye Wozipanga. Ndani? “Kungakhale kovuta kwambiri kuzindikira wopangayo pogwiritsira ntchito njira zasayansi,” anatero Profesa Behe, ndipo anasiya ntchito imeneyi m’manja mwa “afilosofi ndi azaumulungu” kuti ayese kupeza yankho lake. Mwina inu panokha mungalingalire kuti nkhaniyi njosafunika. Komabe, ngati munalandira phukusi lomangidwa bwino lokhala ndi zinthu zimene munali kuzifuna, kodi simungafune kudziŵa munthu amene anatumiza phukusilo kwa inu?
Talandira phukusi limenelo mophiphiritsira—phukusi lodzazidwa ndi mphatso zamtengo wapatali zimene zimapangitsa kuti tikhalebe ndi moyo ndiponso kuti tizisangalala ndi moyowo. Phukusi limenelo ndilo dziko lapansi, kuphatikizapo zinthu zonse zopezeka mmenemo zomwe zimathandiza kuchirikiza moyo. Kodi sitingafune kupeza yemwe anatipatsa mphatso zimenezi?
Ndithudi, Wotumiza phukusi limenelo analitumizira pamodzi ndi kalata. “Kalata” imeneyi ndiyo buku lanzeru lakale limene taligwira mawu poyambirira paja—Baibulo. M’mawu ake oyambirira, Baibulo limafotokoza momveka bwino za yemwe anatipatsa phukusi limeneli kuti: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1.
Mu “kalata” yakeyi Mlengiyo amatchulamo dzina lake kuti: ‘Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, . . . , nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka mmenemo, Iye amene amapatsa anthu a mmenemo mpweya.’ (Yesaya 42:5) Inde, Yehova ndilo dzina la Mulungu amene anapanga thambo nalenga amuna ndi akazi padziko lapansi. Koma kodi Yehovayo ndani? Kodi iye ndi Mulungu wamtundu wanji? Ndipo kodi nchifukwa ninji anthu onse a padziko lapansi ayenera kumumvera?
[Mawu a M’munsi]
a “Zinthu zosasintha” ndizo mikhalidwe yooneka kusasintha m’chilengedwe chonse. Zitsanzo zake ziŵiri ndizo liŵiro la kuunika ndi kugwirizana kwa mphamvu yokoka ndi kulemera kwa chinthu.
[Chithunzi patsamba 3]
Angkor Wat anamangidwa ndi anthu
[Chithunzi patsamba 4]
Mutalandira mphatso, kodi simumafunanso kudziŵa amene waitumiza?