Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • T-23 tsamba 2-6
  • Yehova—Kodi Iye Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Yehova—Kodi Iye Ndani?
  • Yehova—Kodi Iye Ndani?
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Ndani Anazipanga?
  • Tanthauzo la Dzina Lake
  • Mikhalidwe Yaikulu ya Yehova
  • Mapindu a Kudziŵa Yehova
  • Kodi Anapanga Zonsezi Ndani?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kodi Yehova Ndani?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Mmene Mungam’dziŵire Mulungu
    Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
  • Bukitsani Kuti Yehova Ndiye Mulungu Woona Yekha
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
Onani Zambiri
Yehova—Kodi Iye Ndani?
T-23 tsamba 2-6

Yehova—Kodi Iye Ndani?

PODUTSA m’nkhalango ina yoŵirira ku Cambodia, Henri Mouhot, Mfalansa woyendera malo wa m’zaka za zana la 19, anafika paphompho lalikulu lachemba lozungulira kachisi. Linali Angkor Wat, chipilala chachikulu kwambiri chachipembedzo padziko lonse lapansi. Mouhot atangochiyang’ana, anazindikira nthaŵi yomweyo kuti chimango chimenecho chokutidwa ndi ndere chinali ntchito ya manja a munthu. “Chinamangidwa ndi katswiri wina wakale lomwe waluso ngati la Michengelo, ndipo nchachikulu kwambiri kuposa chimango chilichonse chomangidwa ndi Agiriki kapena Aroma,” iye analemba motero. Ngakhale kuti chinali chitasiyidwa kwa zaka mazana ambiri, iye sanakayike konse kuti chimango chodabwitsacho, chinali naye wochimanga.

Ndipotu buku lokhala ndi chidziŵitso lolembedwa zaka mazana ambiri zapitazo linagwiritsira ntchito malingaliro ofananawo, likumati: “Pakuti nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.” (Ahebri 3:4) Koma ena anganene kuti, ‘Zinthu zachilengedwe nzosiyana ndi zinthu zopangidwa ndi munthu.’ Komabe, si asayansi onse amene amavomereza malingaliro otero.

Atavomereza kuti “zinthu zamoyo nzosiyana ndi zinthu zosapuma,” Michael Behe, wachiŵiri kwa profesa woona za madzi osiyanasiyana a m’thupi la zamoyo pa Yunivesite ya Lehigh, ku Pennsylvania, U.S.A., anafunsa kuti: “Kodi tinganene kuti zamoyo zinachita kulinganizidwa mwaluntha?” Iye anapitiriza kufotokoza kuti asayansi tsopano akulinganiza masinthidwe ena ndi ena m’matupi a zamoyo mwa njira zotchedwa genetic engineering. Inde, zinthu zopanda moyo ndi zamoyo zomwe “zingapangidwe”! Atapenda maselo amoyo omwe ndi ang’onoang’ono kwambiri moti sangaoneke ndi maso, Behe anaona kucholoŵana kodabwitsa kwa maselo opangidwa ndi mbali zina zodaliranso pa maselo ena kuti zigwire ntchito. Kodi iye ananenanji pomalizira pake? “Chotsatirapo cha khama lonseli lofufuza selo—kufufuza moyo kuyambira pa mamolekyu—chinasonyeza bwino lomwe kuti panali ‘wopanga!’”

Choncho, kodi ndani amene Anapanga zinthu za mipangidwe yocholoŵana zimenezi?

Kodi Ndani Anazipanga?

Yankho likupezeka m’buku lakale lokhala ndi chidziŵitso limene taligwira mawu poyambirira paja—Baibulo. M’mawu ake oyambirira, Baibulo limayankha mosavuta ndi momveka bwino za yemwe anapanga zinthu zonse kuti: “Pachiyambi Mulungu adalenga kumwamba ndi dziko lapansi.”—Genesis 1:1.

Podzisiyanitsa ndi ena onenedwa kuti Mulungu, Mlengi amadzizindikiritsa ndi dzina lapadera kuti: ‘Atero Mulungu Yehova, Iye amene analenga thambo, . . . nayala ponse dziko lapansi, ndi chimene chituluka mmenemo, Iye amene amapatsa anthu a mmenemo mpweya.’ (Yesaya 42:5, 8) Yehova ndilo dzina la Mulungu amene anapanga thambo nalenga amuna ndi akazi padziko lapansi. Koma kodi Yehovayo ndani? Kodi iye ndi Mulungu wamtundu wanji? Ndipo kodi nchifukwa ninji inuyo muyenera kumumvera?

Tanthauzo la Dzina Lake

Choyamba, kodi dzina la Mlengi, Yehova, limatanthauzanji? Dzina la Mulungu limeneli limalembedwa ndi zilembo za Chihebri zinayi (יהוה) ndipo limapezeka pafupifupi nthaŵi 7,000 m’mbali yachihebri ya Baibulo. Dzina limeneli lili mumpangidwe wa kupangitsa wa verebu la Chihebri lakuti ha·wahʹ (“kukhalapo”) ndipo motero limatanthauza “Amapangitsa Kukhalapo.” Mmawu ena tinganene kuti, Yehova mwanzeru amadzipangitsa kukhala chilichonse chimene akufuna kukhala pofuna kukwaniritsa zifuno zake. Iye amakhala Mlengi, Woweruza, Mpulumutsi, Wochirikiza Moyo, ndi zinanso kuti akwaniritse malonjezo ake. Ndiponso, galamala ya verebu la Chihebrilo imasonyeza ntchito imene ikukwaniritsidwabe. Zimenezi zikusonyeza kuti Yehova akudzipangitsabe kukhala wokwaniritsa zifuno zake. Inde, iye ndi Mulungu wamoyo!

Mikhalidwe Yaikulu ya Yehova

Baibulo limasonyeza Mlengi ndi Wokwaniritsa malonjezo ake ameneyu kukhala munthu wochititsa chidwi kwambiri. Yehova iye mwini anaulula mikhalidwe yake ikuluikulu akumati: “Yehova, Yehova, Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa.” (Eksodo 34:6, 7) Yehova akunenedwa kuti ndi Mulungu wokoma mtima. Mawu achihebri amene anagwiritsidwa ntchito pano angatembenuzidwenso kuti “chikondi chodalirika.” Pokwaniritsa chifuno chake chosatha, Yehova modalirika akupitirizabe kusonyeza chikondi kwa zolengedwa zake. Kodi simungayamikire chikondi chimenecho?

Ndiponso Yehova sakwiya msanga ndipo amakhululukira machimo athu mofulumira. Nkosangalatsa kukhala pafupi ndi munthu amene safuna zifukwa mwa ife koma amakhala wofunitsitsa kutikhululukira. Komabe, zimenezo sizitanthauza kuti iye amalolera zinthu zoipa. Iye anati: “Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa.” (Yesaya 61:8) Monga Mulungu wachiweruzo, iye salekerera kwanthaŵi zonse ochimwa osalapa amene amapitirizabe kuchita zinthu zoipazo. Choncho, tingatsimikizire kuti panthaŵi yake yoikika, Yehova adzathetsa kupanda chilungamo kumene kwatizinga m’dzikoli.

Kuchita moyenerera zonse ziŵiri chikondi ndi chiweruzo panthaŵi imodzimodziyo kumafunika kukhala wanzeru. Yehova amalinganiza mikhalidwe iŵiri imeneyi modabwitsa pamene achita nafe zinthu. (Aroma 11:33-36) Ndithudi, nzeru zake zingapezeke kulikonse. Chilengedwe chodabwitsa chimachitira umboni zimenezi.—Salmo 104:24; Miyambo 3:19.

Komabe, kukhala ndi nzeru zokha sikokwanira. Kuti zonse zimene zimabwera m’maganizo mwake zichitikedi, Mlengi ayeneranso kukhala ndi mphamvu zonse. Baibulo limasonyeza kuti iye ali Mulungu woteroyo: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; . . .  ndi mphamvu zake zazikulu, . . .  palibe imodzi isoŵeka.” (Yesaya 40:26) Ndithudi, Yehova amalamulira “mphamvu zake zazikulu” kuti akwaniritse chifuno chake. Kodi mikhalidwe imeneyi sikukopani kuti muyandikane ndi Yehova?

Mapindu a Kudziŵa Yehova

Yehova ‘sanalenga [dziko lapansi] mwachabe,’ koma “analiumba akhalemo anthu” amene ali ndi unansi watanthauzo ndi iyeyo. (Yesaya 45:18; Genesis 1:28) Iye amasamalira zolengedwa zake za padziko lapansi. Anapatsa mtundu wa anthu chiyambi chabwino m’mudzi wokhala ngati munda, paradaiso. Anthuwo akuwononga mudziwu ndipo Yehova sasangalala nazo. Komabe, mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake, Yehova adzachititsa kuti chifuno chake choyambirira chokhudza anthu ndi dziko lapansi chikwaniritsidwe. (Salmo 115:16; Chivumbulutso 11:18) Adzabwezeretsa Paradaiso padziko lapansi kaamba ka awo amene akufuna kumumvera ngati ana ake.—Miyambo 8:17; Mateyu 5:5.

Buku lomaliza la m’Baibulo limafotokoza moyo umene mungasangalale nawo mu Paradaiso ameneyo kuti: “Adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Umenewu ndiwo moyo umene Yehova akufuna kuti inu mukhale nawo. Iye alidi Atate wokoma mtima chotani nanga! Kodi muli wofunitsitsa kuphunzira zambiri ponena za iye ndi zimene zikufunikira kwa inu kuti mudzakhale m’paradaiso?

Kusiyapo ngati tasonyeza lina, Baibulo limene tagwiritsira ntchito ndi Revised Nyanja (Union) Version. Komabe tatsatira Orthography yatsopano.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena