Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • la mutu 5 tsamba 18-19
  • Mmene Mungam’dziŵire Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mmene Mungam’dziŵire Mulungu
  • Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
  • Nkhani Yofanana
  • Kodi Yehova Ndani?
    Nsanja ya Olonda—1998
  • Kodi Dzina la Mulungu Ndi Ndani?
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2019
  • Dzina la Mulungu
    Galamukani!—2017
  • Kodi Mulungu Ndani?
    Nsanja ya Olonda—2002
Onani Zambiri
Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
la mutu 5 tsamba 18-19

Mutu 5

Mmene Mungam’dziŵire Mulungu

1. N’chifukwa chiyani kum’dziŵa Mulungu kuli kofunika kwambiri?

KODI mukafuna uphungu, simumapita kwa munthu amene muma’dalira? Kunena zoona, ngati wopereka uphunguyo mumam’dalira, mudzakhala ndi mtima wofuna kuulabadira, kaya mapindu ake ndi a nthaŵi yomweyo kapena ndi a m’tsogolo. Kuti mupinduledi ndi uphungu wothandiza wa m’Baibulo, muyenera kum’dziŵa Wolemba wake wamkulu. Inde, ndipo iyeyo akhoza kukuonani ngati “bwenzi” lake!—Yesaya 41:8.

2. Dzina la Mulungu ndi tanthauzo lake n’zofunika kwambiri, chifukwa chiyani?

2 Ngati mukufuna kupalana ubwenzi ndi munthu wina, mosakayikira mumafuna kuti mum’dziŵe dzina lake. Kodi Mulungu amene analemba Baibulo ali ndi dzina? Iye mwiniyo anati: “Ine ndine Yehova; dzina langa ndi lomweli; ndipo ulemerero wanga Ine sindidzapereka kwa wina, ngakhale kunditamanda kwa mafano osemedwa.” (Yesaya 42:8) “Yehova,” limene amalilemba choncho הוהי (kuŵerenga kuchokera kumanja kupita kumanzere) m’chinenero cha Chihebri, ndilo dzina lake. Dzina limeneli limapezeka pafupifupi ka 7,000 m’Malemba Achihebri mu Baibulo. Tanthauzo lodziŵika la dzina la Mulungulo n’lakuti “Amachititsa Kukhala,” kutanthauza kuti Yehova amadzichititsa kukhala aliyense amene angafunikire kukhala kuti akwaniritse zolinga zake. Komanso, m’Chihebri dzina lake linalembedwa m’mawu osonyeza kuti chinthu chili m’kati mochitika. Kodi zimenezo zikutanthauzanji? Zikutiuza kuti Yehova wadzipangitsa ndipo akudzipangitsabe kukhala amene afunikira kukhala kotero kuti akwaniritse zolinga zake. Iye ndi Mulungu wamoyo, osati mphamvu chabe ayi!

3. Kodi muli ndi zifukwa zotani zom’tamandira Yehova?

3 Yehova anakhala Mlengi. (Genesis 1:1) Iye ali “Mulungu wamoyo, amene analenga zakumwamba ndi zapansi, ndi nyanja, ndi zonse zili momwemo.” (Machitidwe 14:15) Yehova analenga zonse, kuphatikizapo anthu aŵiri oyambirira, Adamu ndi Hava. Choncho, Mulungu ndiye “chitsime cha moyo.” (Salmo 36:9) Iye anakhalanso Wosunga moyo. Choncho, “sanadzisiyira iye mwini wopanda umboni, popeza anachita zabwino, nakupatsani inu zochokera kumwamba mvula ndi nyengo za zipatso, ndi kudzaza mitima yanu ndi chakudya ndi chikondwero.” (Machitidwe 14:17) Mu Africa ndi ku Asia, anthu ambiri amalambira makolo awo akufa chifukwa chakuti ndiwo anawapatsa moyo. Kodi iwo sayenera kuyamikira kwambiri Mlengi ndi Wosunga moyo wathu, Uyo amene analenga anthu aŵiri oyambirira ndi kuwapatsa mphamvu zoberekera? Kusinkhasinkha mfundo imeneyo kungakusonkhezereni kudzuma kuti: “Muyenera inu, Ambuye wathu, ndi Mulungu wathu, kulandira ulemerero ndi ulemu ndi mphamvu; chifukwa mudalenga zonse, ndipo mwa chifuniro chanu zinakhala, nizinalengedwa.”—Chivumbulutso 4:11.

4. Kodi mikhalidwe ina yaikulu ya Yehova ndi yotani?

4 Mwa kuŵerenga Baibulo, mutha kum’dziŵa Mlengi wanu, Yehova, ndi kuphunzira kuti ndi Mulungu wa mtundu wanji. Limasonyeza kuti “Mulungu ndiye chikondi.” (1 Yohane 4:16; Eksodo 34:6, 7) Pamene muŵerenga Baibulo kuchokera ku Genesis mpaka Chivumbulutso, mudzapeza nkhani zambiri zosonyeza kuti iye alidi Mulungu wachikondi. Bwanji osakhala ndi chizoloŵezi choŵerenga Mawu a Mulungu tsiku ndi tsiku kotero kuti mum’dziŵe Mlengi wanu? Phunzirani Baibulo mosamalitsa mothandizidwa ndi awo amene amadziŵa bwino nkhani zake. (Machitidwe 8:26-35) Pochita zimenezo, mudzaona kuti iye alinso Mulungu wa chilungamo, amene sadzapitiriza kulolera zoipa mpaka kalekale. (Deuteronomo 32:4) Kusonyeza chikondi ndi chilungamo panthaŵi imodzi kumakhala kovuta kwa munthu, koma mu nzeru zake, Yehova amatha kusonyeza ziŵirizo pamlingo woyenera nthaŵi imodzi. (Aroma 11:33; 16:27) Pokhala Mulungu Wamphamvuyonse, iye ali ndi mphamvu zochita chilichonse chimene angafune kuti akwaniritse zolinga zake. (Genesis 17:1) Yesani kugwiritsa ntchito uphungu wanzeru umene mumapeza m’Baibulo, ndipo mudzam’zindikira kwambiri Mlengi wanuyo, podziŵa kuti uphungu wake umakhala wokupindulitsani nthaŵi zonse.

5. Kodi inuyo panokha mungam’dziŵe motani Mulungu?

5 Koma pakalinso njira imodzi imene mungam’fikire nayo Mulungu. Ndiyo kudzera m’pemphero. Yehova ali “Wakumva pemphero.” (Salmo 65:2) Iye “angathe kuchita koposaposatu zonse zimene tizipempha.” (Aefeso 3:20) Komabe, kodi mungam’ganizire bwanji “mnzanu” amene amangobwera kwa inu pamene akufuna thandizo? Mwachidziŵikire simudzamuona kukhala munthu wabwino kwambiri. Mofananamo, inunso muyenera kugwiritsa ntchito mwayi wa pemphero osati kungopempha Mulungu zimene mukuzisoŵa, komanso kum’yamikira ndi kum’tamanda.—Afilipi 4:6, 7; 1 Atesalonika 5:17, 18.

[Chithunzi patsamba 18]

Dzina la Mulungu limene limapezeka m’malemba Achihebri m’buku la Yesaya

[Chithunzi patsamba 19]

Bwanji osam’fikira Yehova m’pemphero?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena