Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 5/1 tsamba 5-7
  • Kodi Yehova Ndani?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Yehova Ndani?
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Tanthauzo la Dzina Lake
  • Mikhalidwe Yaikulu ya Yehova
  • Mulungu wa Mitundu Yonse
  • Mapindu a Kudziŵa Yehova
  • Yehova—Kodi Iye Ndani?
    Yehova—Kodi Iye Ndani?
  • Mmene Mungam’dziŵire Mulungu
    Moyo Wokhutiritsa—Mmene Mungaupezere
  • Bukitsani Kuti Yehova Ndiye Mulungu Woona Yekha
    Lambirani Mulungu Woona Yekha
  • Chifukwa Chake Tiyenera Kudziwa Dzina la Mulungu
    Dzina la Mulungu Limene Lidzakhala Kosatha
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1998
w98 5/1 tsamba 5-7

Kodi Yehova Ndani?

YEHOVA anauza mmodzi wa alambiri ake okhulupirika kuti: “Palibe munthu adzandiona ine ndi kukhala ndi moyo.” (Eksodo 33:20) “Mulungu ndiye Mzimu,” ndipo anthu sangamuone ndi maso awo aumunthu. (Yohane 4:24) Kuona dzuŵa mwachindunji nthaŵi imene lili pamutu kungavulaze maso athu. Momwemonso kungakhale kovulaza kuona Magwero a mphamvu yaikulu kwambiri imene inalenga dzuŵa lathu loŵala mwamphamvu chotero. Inde, Mphamvu imene inalenganso madzuŵa ena osaŵerengeka omwe ali kuthambo.

Komano sitifunikira kuona Mulungu kuti timdziŵe. Baibulo limatiuza za Amene anapanga phukusi lokongolali, dziko lapansi, ndipo limavumbulanso mikhalidwe yake. Choncho, nkofunika kwambiri kufufuza m’Baibulo kuti tidziŵe za Atate amene anatipatsa moyo natipatsanso mudzi woti tisangalalemo ndi moyo umenewo.

Tanthauzo la Dzina Lake

Maina onse ali ndi matanthauzo, ngakhale kuti ambiri sangawadziŵe lerolino. Mwachitsanzo, dzina lotchuka kwambiri lakuti Davide limachokera kumawu achihebri amene amatanthauza “Wokondedwa.” Dzina la Mlengi, Yehova, lilinso ndi tanthauzo. Kodi limatanthauzanji? M’chinenero choyambirira cha Baibulo chachihebri, dzina la Mulungu linalembedwa m’zilembo zinayi, YHWH, ndipo limapezeka pafupifupi nthaŵi 7,000 m’mbali yachihebri ya Baibulo. Dzina la Mulungu limeneli limatanthauza kuti “Amapangitsa Kukhalapo.” Limasonyeza kuti Yehova mwanzeru amadzipangitsa kukhala chilichonse chimene akufuna kukhala pofuna kukwaniritsa zifuno zake. Iye ndi Mlengi, Woweruza, Mpulumutsi, Wochirikiza Moyo, chotero iye angakwaniritse malonjezo ake. Ndiponso, dzina lakuti Yehova m’Chihebri lili m’gulu la mawu amene amasonyeza ntchito imene ikukwaniritsidwabe. Inde, Yehova akudzipangitsabe kukhala wokwaniritsa zifuno zake. Iye ndi Mulungu wamoyo!

Mikhalidwe Yaikulu ya Yehova

Baibulo limafotokoza kuti Mlengi ndi “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachoonadi; wakusungira anthu osaŵerengeka chifundo, wakukhululukira mphulupulu ndi kulakwa ndi kuchimwa.” (Eksodo 34:6, 7) Mawu akuti “ukoma mtima” anatembenuzidwa kuchokera kumawu achihebri atanthauzo kwambiri. Amatanthauza kukoma mtima kumene kumadziphatika kuchinthu china mpaka chifuno chake ku chinthucho chitakwaniritsidwa. Angatembenuzidwenso kuti “chikondi chodalirika.” Kukoma mtima kwa Yehova kumadziphatika mwachikondi kwa zolengedwa zake ndipo kumakwaniritsa chifuno chake chodabwitsa. Kodi simungayamikire chikondi chimenecho chochokera kwa Amene anakupatsani moyo?

Yehova sakwiya msanga ndipo amakhululukira machimo athu mofulumira. Nkosangalatsa kukhala pafupi ndi munthu wotero. Komabe, zimenezo sizitanthauza kuti iye amavomereza zinthu zoipa. Iye anati: “Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa.” (Yesaya 61:8) Monga Mulungu wachiweruzo, iye sadzalekerera mpaka muyaya ochimwa osalapa amene amapitirizabe kuchita zinthu zoipazo. Choncho, tingatsimikizire kuti panthaŵi yake yoikika, Yehova adzathetsa kupanda chilungamo kumene kuli padziko lapansi. Iye sadzanyalanyaza anthu ovutika.

Sikwapafupi kuchita moyenerera zonse ziŵiri chikondi ndi chiweruzo panthaŵi imodzimodziyo. Ngati ndinu kholo, kodi mumaona kuti nkovuta kulinganiza nthaŵi yoperekera chilango, mmene mungachiperekere ndi ukulu wake kwa ana anu pamene alakwa? Kuweruza moyenerera ndiponso kuchitira chifundo panthaŵi imodzimodziyo kumafuna nzeru yaikulu. Yehova amasonyeza kwambiri mkhalidwe umenewo pamene aweruza anthu. (Aroma 11:33-36) Ndithudi, nzeru za Mlengi zimapezeka kulikonse, mwachitsanzo zimapezeka m’chilengedwe chake chodabwitsa chotizinga.​—Salmo 104:24; Miyambo 3:19.

Komabe, kukhala ndi nzeru zokha sikokwanira. Kuti akwaniritse chifuniro chake, Mlengi ayeneranso kukhala ndi mphamvu, ndipo Baibulo limafotokoza kuti iye ali ndi mphamvu zazikulu, ndipo limati: “Kwezani maso anu kumwamba, muone amene analenga izo, amene atulutsa khamu lawo ndi kuziŵerenga; azitcha zonse maina awo, ndi mphamvu zake zazikulu, ndi popeza ali wolimba mphamvu, palibe imodzi isoŵeka.” (Yesaya 40:26) Yehova amachita zinthu mogwiritsira ntchito “mphamvu zake zazikulu.” Kodi mkhalidwe umenewo sungakukopeni kuti muyandikane naye?

Mulungu wa Mitundu Yonse

‘Koma kodi Yehova sali Mulungu wa “Chipangano Chakale,” Mulungu wa Israyeli wakale?’ mungafunse chotero. Nzoona kuti Yehova anadzivumbula kwa Aisrayeli. Komabe, popeza kuti analenga banja loyambirira, Yehova ndiye Mulungu “amene kuchokera kwa Iye fuko lonse . . . la padziko alitcha dzina.” (Aefeso 3:15) Ngati mumakhulupirira kuti nkoyenerera kulemekeza makolo anu akale, kodi sikungakhalenso koyenerera kulemekeza Amene anapereka moyo kwa munthu woyamba, kholo lathu, amene ali maziko a mitundu yonse imene ili padziko lapansi lerolino?

Mlengi wa mtundu wa anthu si wopanda nzeru. Zoonadi, nthaŵi ina iye anali paunansi wapadera ndi mtundu wa Israyeli. Koma ngakhale panthaŵiyo, iye anali kulandira onse amene anaitana pa dzina lake. Mfumu yanzeru ya Israyeli popemphera kwa Yehova inati: “Kunena za mlendo, wosati wa anthu anu Aisrayeli, koma wakufumira m’dziko lakutali chifukwa cha dzina lanu, . . . mverani inu m’Mwamba mokhala inu, ndipo chitani monga mwa zonse mlendoyo azipempha kwa inu; kuti anthu onse a dziko lapansi adziŵe dzina lanu.” (1 Mafumu 8:41-43) Lerolinonso, anthu a mitundu yonse angadziŵe Yehova ndi kukhala paunansi wopindulitsa ndi iye. Koma kodi zimenezo zikukukhudzani motani?

Mapindu a Kudziŵa Yehova

Pongobwerezanso fanizo la m’nkhani yapitayo, ngati munalandira phukusi lomangidwa mokongola, ndithudi mungafune kudziŵa cholinga cha mphatso imeneyo. Kodi iyenera kugwiritsiridwa ntchito motani ndipo iyenera kusamaliridwa motani? Mofananamo, tifunikira kudziŵa cholinga cha Mulungu potilengera dziko lapansi. Baibulo limanena kuti iye “sanalilenga mwachabe,” koma “analiumba akhalemo anthu.”​—Yesaya 45:18.

Komabe, anthu ambiri, sakusamalira mphatso imeneyi ya Mlengi. Iwo akuwononga dziko lapansi, ndipo Yehova sasangalala ndi zimenezo. Komabe, mogwirizana ndi tanthauzo la dzina lake, Yehova ali wotsimikiza mtima kukwaniritsa chifuno chake choyambirira chokhudza anthu ndi dziko lapansi. (Salmo 115:16; Chivumbulutso 11:18) Iye adzakonzanso dziko lapansi nalipereka monga choloŵa kwa awo amene akufunitsitsa kukhala monga ana ake omvera.​—Mateyu 5:5.

Buku lomaliza la m’Baibulo limafotokoza mmene zinthu zidzakhalira panthaŵi imene zidzachitika zimenezo kuti: “Taonani, chihema cha Mulungu chili mwa anthu; ndipo adzakhalitsa nawo, ndi iwo adzakhala anthu ake, . . . ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:3, 4) Palibenso amene adzagwetsa misozi chifukwa cha chisoni kapena kulira chifukwa cha imfa ya wokondedwa. Palibenso amene adzafuula kufuna chithandizo atasoŵa chochita kapena amene adzavutika ndi kupweteka kwa matenda akupha. Ngakhale ‘imfa idzathetsedwa.’ (1 Akorinto 15:26; Yesaya 25:8; 33:24) Zimenezi zikufotokoza za moyo umene poyambirira Yehova anafuna kuti tikhale nawo pamene analenga makolo athu oyambirira.

Ndithudi, mutha kuona chitsanzo cha mikhalidwe ya m’paradaiso imeneyo nthaŵi yomwe ino pakati pa alambiri a Yehova. Iye akuwauza kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” (Yesaya 48:17) Yehova ndi Atate wachifundo amene amatiphunzitsa, ife ana ake, njira yabwino kwambiri yokhalira ndi moyo. Zitsogozo zake kwa anthu zimapereka, osati chiletso chosayenerera, koma chitetezero chachikondi. Ngati tizitsatira tidzakhala ndi mtendere weniweni ndi chimwemwe, monga momwedi kwalembedwera kuti: “Koma Ambuye [“Yehova,” NW] ndiye Mzimuyo; ndipo pamene pali Mzimu wa Ambuye [“Yehova,” NW] pali ufulu.” (2 Akorinto 3:17) Mwa kutsatira zitsogozo zolembedwa m’Baibulo, awo amene amamvera ulamuliro wake tsopano lino ali ndi mtendere wa m’maganizo umene tsiku lina udzadzaza dziko lonse la mtundu wa anthu.​—Afilipi 4:7.

Yehova ali Atate wokoma mtima chotani nanga! Kodi mukufuna kuphunzira zambiri ponena za Amene anapanga chilengedwe chonse chodabwitsa? Amene akufuna kutero adzapeza mapindu ochuluka ngakhale tsopano lino. Ndipo mtsogolomu madalitso ake adzakhala osatha.

[Chithunzi patsamba 5]

Dzina la Mulungu lolembedwa m’zilembo zinayi zachihebri limapezeka pamakoma a matchalitchi ambiri akale

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena