Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 6/1 tsamba 8
  • Kugwiritsira Ntchito Mpata Uliwonse

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kugwiritsira Ntchito Mpata Uliwonse
  • Nsanja ya Olonda—1998
  • Nkhani Yofanana
  • Ana a Sukulu a Mboni Ayamikiridwa
    Nsanja ya Olonda—1988
  • “Dzanja la Yehova Linali Nawo”
    Nsanja ya Olonda—1989
Nsanja ya Olonda—1998
w98 6/1 tsamba 8

Olengeza Ufumu Akusimba

Kugwiritsira Ntchito Mpata Uliwonse

A MBONI ZA YEHOVA amadziŵika bwino padziko lonse lapansi chifukwa cha ntchito yawo yophunzitsa za m’Baibulo. Koma iwo amachitanso maprogramu ena amenenso amapindulitsa anthu. Iwo amayamikiridwa kwambiri chifukwa cha kuthandiza anthu kumeneku, monga momwe zokumana nazo zotsatirazi za ku Ecuador zikusonyezera.

◻ Oyang’anira fakitale ina yaikulu anakonza zokhala ndi kosi yokhudza makhalidwe abwino a pabanja kwa antchito awo. Woyang’anira zosoŵa za antchito anapempha ansembe achikatolika kuti adzakhalepo koma iwo sanafikepo. Wansembe wina anauza woyang’anirayo kuti panali ansembe ochepa kwambiri amene akuidziŵa nkhaniyo ndipo mwina palibe aliyense amene angadzapezekepo. Atamva zimenezi, wa Mboni wina wogwira ntchito pomwepo analinganiza kuti mbale amene nthaŵi zambiri amafola gawo lamalonda adzachezere fakitaleyo.

Tsiku lotsatira, wa Mboniyo anafikira woyang’anira zosoŵa za antchito uja namsonyeza autilaini ya nkhani zimene analingalira kuti adzakambitsirane pakosipo. Iye anasankha nkhani zosiyanasiyana kuchokera m’zofalitsa zosiyanasiyana za Watch Tower Society. Woyang’anirayo anachita chidwi kwambiri. Iye anasankha nkhani zitatu zoti adzakambitsirane​—mgwirizano wa anthu, makhalidwe abwino a pantchito, ndiponso makhalidwe abwino a pabanja. Kenaka anapanga makonzedwe akuti antchito onse aphunzire zimenezo.

Ogwira ntchitowo anagaŵidwa m’magulu asanu ndi aŵiri, gulu lililonse lokhala ndi anthu 30, ndipo atawagaŵa abale atatu oyeneretsedwa anafotokoza nkhanizo kwa maguluwo. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Antchito ambiri anapempha kuti akachezeredwe kunyumba kwawo, ndipo zothandizira kuphunzira Baibulo zokwanira 216 zinagaŵiridwa. Oyang’anira fakitaleyo anakondwera kwambiri ndipo anapempha a Mboniwo ngati angalinganizenso maphunziro ena.

◻ Posachedwapa, dziko la Ecuador linakhazikitsa lamulo lololeza kuti aziphunzitsa zachipembedzo m’masukulu. Mlongo wina mmishonale anafikira mkazi wina yemwe ndi mphunzitsi wamkulu pasukulu ina yapulaimale nafunsa za mmene lamulo latsopanolo linali kugwirira ntchito. Mphunzitsi wamkuluyo anafotokoza kuti anayesa kuyambitsa programu ya kulambira Mariya koma palibe chilichonse chimene chinachitika. Pamene mlongoyo ananena kuti kulambira kotero kungadzetse mavuto kwa ana amene sali a Katolika, mphunzitsiyo anavomereza. “Komabe,” anatero mmishonaleyo, “tili ndi programu yophunzitsa za makhalidwe abwino kuchokera m’Baibulo ndipo maphunzirowo sakakamiza munthu kuloŵa chipembedzo china chilichonse.” Mphunzitsiyo anayankha kuti: “Nanga mungabwere liti? Kodi mungabwere mkucha?” Mmishonaleyo atamsonyeza buku la Kumamumvetsera Mphunzitsi Wamkuru’yo, analingalira zoti adzaphunzitse za mutu wakuti “Achimwemwe Ali Amtendere.”

Atabweranso ulendo wina, mmishonaleyo anatha maola atatu akuchezera makalasi asanu ndi aŵiri osiyanasiyana ndipo mphunzitsi uja anali kumvetsera nthaŵi yonseyo. Atamaliza kucheza ndi kalasi lachisanu, wophunzira wina anati: “Aphunzitsi, timati mukachezerenso kalasi lachisanu ndi chimodzi. Amakonda kutizunza ndi kuyambitsa ndewu!” Mphunzitsi wina anati: “Nkhani yokhudza chiwawa njofunika kwambiri kukambitsirana. Tifunikira nthaŵi yambiri yoti tidzakambitsirane nkhani imeneyi.”

Makonzedwe anapangidwa odzachita maulendo obwereza pasukuluyo kuti adzakambitsirane nkhani zina monga zakuti kumvera ndiponso kunama. Choncho pakali pano, zotsatirapo zake nzabwino kwambiri. Tsopano pamene mlongo mmishonaleyo ayenda mumsewu, ana amamthamangira ndi kumlonjera ndi kumfunsa mafunso a m’Baibulo. Ena amamsonyeza kwa makolo awo mosangalala. Kuwonjezera pamenepo, anakhazikitsa phunziro la Baibulo lapanyumba ndi ana aŵiri a pasukulupo.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena