Ripoti la Olengeza Ufumu
Ana a Sukulu a Mboni Ayamikiridwa
KODI inu monga wophunzira m’sukulu, muli wamanyazi ponena za kulankhula m’malo mwa chikhulupiriro chanu? Zokumana nazo ziri pansizi zikuvumbulutsa kuti Mboni zachichepere zimenezi zinali zopanda mantha kusungilira chikhulupiriro chawo cha Chikristu ndipo zinayamikiridwa kaamba ka kuchita tero.
◻ Ku sukulu mu Australia, ophunzira anapatsidwa kulemba nkhani yachidule pa Krisimasi, koma mphunzitsi ananena kwa Mboni ya zaka 11 kuti: “Ndikudziŵa kuti uli mmodzi wa Mboni za Yehova, chotero sungalembe ponena za zikondwerero za Krisimasi. Ungalembe nkhani yosiyana pa ‘Mbiri ya Krisimasi.’” Mlongo wachichepereyo anakonza nkhaniyo, kugwiritsira ntchito chidziŵitso choyenerera kuchokera ku zofalitsidwa za Sosaite ndi mabukhu ena olozerako. Ku kudabwitsidwa kwa kalasiyo, mphunzitsiyo anachitira ndemanga kuti chidziŵitsocho chinali chabwino koposa ndipo cholongosoka m’mbiri yakale. “Pa nkhani zonse zimene ndalandira, yako iri yabwino koposa m’kalasi,” anatero mphunzitsiyo. Monga chotulukapo chake, Mboni yachichepereyo inagawira broshuwa imodzi ya School, magazini 15, bukhu limodzi la Youth, ndi mabukhu aŵiri a Mungathe Kukhala ndi Moyo ndi aphunzitsi ake ndi ophunzira anzake.
◻ M’sukulu ina mu Australia, ana asanu ndi atatu a Mboni analangizidwa ndi mphunzitsi wobwerekera masana aliwonse kaamba ka milungu itatu yomalizira ya sukulu, popeza iwo sakanatenga mbali m’machitachita a Krisimasi. Iye kenaka anachita ndemanga kwa mayi wa ena a anawo: “Mbali imene ndinachita inali kokha yaing’ono. Aphunzitsi ochepa anabwera ndi kufunsa mmene zinthu zinali kuyendera. Ndinanena kwa iwo kuti: ‘Sichitanthauza kanthu za chimene mumalingalira za chipembedzo chawo ndi njira imene amakanira kuchita machitachita ena, iri ndi gulu labwino koposa la ana limene ndagwira nalo ntchito.’” Milungu yochepa pambuyo pake pamene anafikiridwa mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba, iye ananena kuti: “Ndinaiwala, kodi munapereka zimene ndinanena ponena za ana ku sukulu? Ndikufuna kuti aliyense adziwe.”
◻ Kuchokera ku United States kwachokera chokumana nacho ichi cha wophunzira pa sukulu yapamwamba wa zaka za kubadwa 17 amene kalasi lake la lamulo linadzilowetsa mozama m’kukambitsirana kwa kuyenera kwa kugwirizana ndi ufulu wa chipembedzo ndi kudzipatula kwa Tchalitchi ndi Boma. Ziŵiri za nkhanizo zinakhudza Mboni za Yehova ndi nkhani ya mwazi. Mlongo wachichepereyo anapeza kuti ripoti lomwe linali kukambitsiridwalo linali la mbali imodzi ndipo loipa m’chigwirizano ndi chowonadi cha Baibulo pa mwazi ndipo anauza mphunzitsi wake chimenecho. Iye anavomereza mwakumpatsa iye mwaŵi wa kulankhula ku kalasilo. Asanayambe nkhani yake, ophunzirawo anaganiza kuti mabwalo a milandu anali kupanga chosankha chabwino m’kukakamiza Mboni kulandira mwazi motsutsana ndi zikhumbo zawo. Koma pambuyo pakumva m’tsutsano wozikidwa pa Baibulo, kalasilo linavomereza mwachiyanjo motsutsana ndi zosankha za bwalo la milandulo. Mlongo wathu anasangalatsidwa pamene ambiri a ophunzirawo anamufikira ndi kumufunsa kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka ponena za zikhulupiriro za Mboni za Yehova. Iye tsopano akunena kuti amayamikira mokulira kuti sukulu iri gawo lake lapadera.
Inde, inu ana a sukulu muli ndi gawo lapadera. Pamene muli ndi mwaŵi, pitirizani mwachifundo kuthandiza ophunzira anzanu kuphunzira ukulu wa chifuno cha Mulungu, ndipo inu mudzapeza chiyamikiro osati kokha kuchokera kwa ena komanso kuchokera kwa Yehova iyemwini!—Yobu 40:14.