Lipoti la Olengeza Ufumu
Ana Asukulu a ku Nigeria Adalitsidwa Chifukwa cha Kukhulupirika
MTUMWI Paulo analemba kuti: “Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.” (Aroma 12:18) Ana asukulu a Mboni za Yehova ku Nigeria amagwiritsira ntchito uphungu umenewu, ngakhale pamene akuzunzidwa. Monga chotulukapo, Yehova amawadalitsa.
◻ Mphunzitsi wina sanakonde Mboni za Yehova mpang’ono ponse. Pamene anasonkhana nthaŵi ina m’mawa, anainatira Mboni zonse kutsogolo ndi kuzilamula kuimba nyimbo yafuko. Izo zinakana, zikumafotokoza kuti zinafuna kudzipereka kotheratu kwa Mulungu. Ndiyeno mphunzitsiyo anazitulutsira kubwalo zonse ndi kuziuza kudula udzu. Panthaŵiyo, ophunzira ena anapitiriza kuphunzira.
Mboni yachikulire inatenga brosha ya School and Jehovah’s Witnesses niipereka kwa mphunzitsiyo, ikumafotokza kaimidwe kauchete ka Mboni za Yehova. Komabe, mphunzitsiyo anakana kukambitsirana nkhaniyo ngakhale kulandira broshayo. Kwenikwenidi, iye panthaŵi yomweyo anakhwimitsa chilango cha anawo.
Mboni zachicheperezo zinapitiriza kupirira chilangocho ndipo zinadulabe udzuwo ngakhale pamene mphunzitsiyo sanalipo. Tsiku lina mphunzitsiyo anabisala ndi kuwapenyerera pamene anapitiriza kugwira ntchito akuimba nyimbo Zaufumu. Anakondweretsedwa kwambiri kotero kuti anawabwezera m’kalasi, akumafotokoza kudabwa kwake ndi khalidwe lawo. Kodi chotulukapo nchotani? Tsopano mphunzitsiyo akuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova!
Ndithudi, ana asukulu ameneŵa anadalitsidwa chifukwa cha kukhulupirika kwawo kwa Yehova ndi malamulo ake amakhalidwe abwino.—Miyambo 10:22.
◻ Ruth ndi mabwenzi ake anadalitsidwanso chifukwa cha kukhulupirika kwawo ku chifuno cha Yehova chonena za ‘kusakhala a dziko lapansi.’ (Yohane 17:16) Ruth, yemwe ali ndi zaka 18, anayamba upainiya pamene anali ndi zaka 12. Iye ndi Mboni zina analandira chitsutso kwa aphunzitsi a pasukulupo chifukwa chokana kuimba nyimbo yafuko. Mphunzitsi wina anapempha kuwonana ndi makolo a asungwanawo. Pambuyo popereka chifukwa mwakugwiritsira ntchito brosha ya School, mphunzitsiyo anakhutiritsidwa ndipo sanavutitsenso ophunzirawo.
Komabe, tsiku lina mphunzitsi wochokera ku India anatukwana ndi kulanga mmodzi wa asungwanawo pamaso pakalasi pamene msungwanayo anakana kuimba nyimbo yafuko. Msungwanayo anachinjiriza chikhulupiriro chake molimba mtima ndipo mphunzitsiyo anamtenga kupita kukawonana ndi mphunzitsi wamkulu pasukulupo. Pamene anafika kumeneko, Mboni yachichepereyo inapeza kuti wachiŵiri kwa mphunzitsi wamkuluyo analiponso. Anadabwa kwambiri kuwona kuti mphunzitsi wamkuluyo ndi wachiŵiri wake anayamba kuseka. Akumatembenukira kwa mphunzitsiyo, mphunzitsi wamkuluyo anati: “Adona, musadzivute ndi asungwanawa. Ngakhale mutawapha, iwo angakonde kufa koposa kuimba nyimbo yafuko. Kodi simunamve za iwo?” Iye ndi womthandiza wake analankhula za chikhulupiriro ndi kulimba mtima kwa Mboni za Yehova. Akumalankhula kwa msungwanayo, mphunzitsi wamkuluyo anati anali wachisoni chifukwa cha kumchititsa manyazi. Ndiyeno anawonjezera kuti: “Pitiriza m’ntchito zako zokhulupirika. Ndimakhumbira chipembedzo chako ndi kaimidwe kako kolimba mtima ponse paŵiri kunja ndi kusukulu kuno.” Pambuyo pake, mphunzitsi wotsutsayo anapepesa kwa Mboniyo, nanena kuti tsopano anamvetsetsa kaimidwe kauchete ka Mboni.
Ana ameneŵa anatsatira chitsanzo cha Ahebri atatu omwe sanaswe umphumphu wawo kwa Mulungu mwakugwadira chifano, ndi wa Danieli, amene anakana kuleka kupemphera kwa Yehova. Amuna ameneŵa anadalitsidwa ndi Yehova chifukwa anali okhulupirika ku malamulo olungama a Mulungu.—Danieli, mitu 3 ndi 6.