Chochitika Chosaiŵalika ku France
“SITIKUFUNA MZINDA WA YEHOVA!” anafotokoza motero mapepala omatidwa m’tauniyo. “Tiyeni Tigwirizane Kutsutsa Ntchito ya Yehova” linalimbikitsa motero gulu lina lotsutsa. Kwenikweni nkhani mazanamazana za m’manyuzipepala zinafalitsa zimenezi kwa anthu onse. Mapempho anasainidwa, ndipo mipukutu ya matrakiti oposa theka la miliyoni onena zimenezi anasefukira m’mabokosi olandiriramo makalata. Kodi ntchito imeneyi yomwe inayambitsa phokoso m’tauni yabata ya Louviers ya kumpoto chakumadzulo kwa France inali ntchito yanji? Inali ntchito yomanga ofesi yatsopano yanthambi ndi nyumba zogonamo zomwe Mboni za Yehova zinali kuyembekezera kumanga.
Yehova Akulitsa
Ntchito ya Mboni za Yehova ku France inayambika cha kumapeto kwa zaka za zana la 19. Malo oyamba a mabuku anatsegulidwa mu 1905 ku Beauvène, kummwera kwa France, ndipo mu 1919, ofesi yaing’ono inayamba kugwira ntchito ku Paris. Ofesi yanthambi inatsegulidwa mwalamulo mumzindamo mu 1930, ndipo chaka chotsatira ogwira ntchito mu ofesimo anakakhala kunyumba ya Beteli ya ku Enghien-les-Bains, kumpoto kwa Paris. Nkhondo Yadziko II itatha, banja la Beteli linakakhalanso ku Paris, ndipo mu 1959 nthambiyo inasamutsidwira kunyumba yansanjika zinayi ku Boulogne-Billancourt, kumalire a kumadzulo a likululo.
Chifukwa cha kufutukuka kwa ntchito yolalikira Ufumu, mu 1973 makina osindikizira ndi zipangizo zotumizira katundu anazisamutsira ku Louviers, mtunda wa makilomita 100 kumadzulo kwa Paris, koma maofesi anakhalabe ku Boulogne-Billancourt. Komabe, kuwonjezeka kwa chiŵerengero cha ofalitsa ku France kunapangitsa kuti nyumba za ku Louviers zikhale zosakwanira, ngakhale kuti anazikuzako mu 1978 ndi 1985. Choncho, analingalira zomanga pamalo aakulu ndi kusonkhanitsira pamalo amodzi banja lonse la Beteli. Si onse amene anasangalala ndi ntchito imeneyi, monga momwe tafotokozera poyambirira paja. Mosasamala kanthu za chitsutso chimenecho, malo omangapo anapezeka pamtunda wa kilomita imodzi ndi theka kuchokera pamene panali nyumba yosindikiziramo. Panapita zaka zisanu ndi chimodzi akugwira ntchito yakalavula gaga, ndipo pomalizira pake, patapita zaka 23 akukhala malo osiyanasiyana, banja lonse la Beteli linayamba kukhalira pamodzi ku Louviers mu August 1996.
Choncho, panali chisangalalo chachikulu pamene unyinji wa anthu achimwemwe okwanira 1,187, kuphatikizapo mamembala 300 a pabanja la Beteli la ku France, ndiponso nthumwi 329 zochokera kunthambi zina 42, anasonkhana Loŵeruka, November 15, 1997, kudzamvetsera nkhani yopatulirira yokambidwa ndi Mbale Lloyd Barry, wa m’Bungwe Lolamulira. Komabe, popeza kuti kupatulirako kunachitika panthaŵi ya udani waukulu ndiponso pamene nkhani zabodza zinapitirizabe kufalitsidwa m’manyuzipepala ncholinga chotsutsa Mboni za Yehova m’dziko lonse la France, analingalira kuti Mboni zonse za ku France zidzasangalale nawo pa chipambano chimenechi. Chotsatirapo chake, Lamlungu, November 16, msonkhano wapadera wa mutu wakuti “Khalanibe m’Chikondi cha Kristu” unalinganizidwa pa Villepinte Exhibition Center, chakumpoto kwa Paris. Mboni za Yehova zonse za ku France kuphatikizapo Mboni zolankhula Chifalansa za ku Belgium ndi Switzerland zinaitanidwa, kuphatikizapo mipingo ya ku Britain, Germany, Luxembourg, ndi Netherlands.
Msonkhano Wochititsa Chidwi
Anayamba kukonzekera msonkhanowo patatsala miyezi isanu ndi umodzi kuti uchitike. Kenaka, patangotsala milungu iŵiri yokha kuti tsiku lopatuliralo lifike, oyendetsa malole amtengatenga a ku France anachita sitalaka, ndipo anatseka misewu ikuluikulu ndi malo omwetsera mafuta. Kodi mipando ndi zipangizo zina zidzafika nthaŵi yabwino? Kodi misewu yotsekedwayo idzalepheretsa abale kuti asabwere? Onse anakondwera kwambiri pamene sitalakayo inatha patapita mlungu umodzi wokha, ndipo misewu inatsegulidwanso. Lachisanu madzulo, asanafike mapeto a mlungu umenewo yomwe inali nthaŵi yopatulira, malole 38 anapititsa mipando 84,000 kumaholo aŵiri aakulu kwambiri omwe anabwerekedwa kaamba ka chochitikacho. Abale ndi alongo akomweko oposa 800 anagwira ntchito usiku wonse mpaka Loŵeruka mmaŵa nthaŵi ya 9:30 a.m., kuika mipandoyo mmalo mwake, kukonza pulatifomu, kuika zipangizo zokuzira mawu, ndiponso ma TV aakulu kwambiri okwanira asanu ndi anayi.
Lamlungu mmaŵa nthaŵi ya 6:00 a.m., zitseko zinatsegulidwa, ndipo gulu la anthu linayamba kuloŵa. Masitima ahayala okwanira 17 anabweretsa Mboni zoposa 13,000 m’likululo. Abale ndi alongo oposa 200 anafika pamalo osiyanasiyana okwerera sitima kukalonjera alendowo ndi kuwaperekeza m’magulumagulu kumalo a msonkhanowo. Mlongo wina anati makonzedwe achikondi ameneŵa anawapangitsa “kudzimva osungika ndiponso achimwemwe.”
Ena anafika ku Paris pandege kapena pamagalimoto. Komabe, ambiri anafika m’mabasi 953, ndipo Mboni zokhala m’Paris zinagwiritsira ntchito zoyendera za onse popita ku Exhibition Center. Ambiri anayenda usiku wonse kapena anachoka kunyumba kwawo mmamaŵa, koma anali ndi chimwemwe chachikulu pamene anapezeka pamsonkhanopo. Kulonjerana kwachimwemwe ndi kupsompsonana kwachikondi kunali kuchitika pakati pa mabwenzi amene anakhala zaka zambiri asanaonane. Zovala zokongola za anthu a m’maiko osiyanasiyana zinatsimikizira kuti m’gulu la anthulo munali anthu ochokera m’maiko osiyanasiyana. Mosakayika konse, panali kuchitika chinthu chinachake chachilendo.
Pamene imafika nthaŵi yoyamba programuyo, pa 10:00 a.m., mipando yonse inali itadzaza, komatu anthu ena mazanamazana anali kufikabe mphindi iliyonse. Kulikonse kumene munthu angaone, kunali nkhope zambirimbiri zomwetulira. Anthu ena zikwizikwi anakhalabe choimirira kapena kukhala pansi penipeni. Mu mzimu wa mutu wankhani wa msonkhanowo, achinyamata ambiri anaimirira mwachikondi kuti achikulire ndiwo akhale pampando. “Tinali achimwemwe chotani nanga kupereka mipando yathu kwa abale ndi alongo amene sitinkawadziŵa, koma amene timawakonda kwambiri!” analemba motero mwamuna wina ndi mkazi wake. Ambiri anasonyeza mzimu wabwino wodzimana ndipo anati: “Tinaimirira tsiku lonse pafupi ndi mipando yomwe tinaika nawo usiku wonse wa Lachisanu. Koma kupezekapo kokhako kunatipangitsa kudzazidwa ndi chiyamiko choperekedwa kwa Yehova.”
Mosasamala kanthu za kutopa ndi kukhala omangika, nthumwi zinamvetsera mwatcheru zedi pamene anali kufotokoza za malipoti a kumaiko ena ndiponso pankhani zokambidwa ndi Lloyd Barry ndi Daniel Sydlik, yemwenso ndi wa m’Bungwe Lolamulira. Mbale Barry anakamba nkhani ya mutu wakuti “Yehova Awonjezera Mphamvu Iye Amene Alibe Mphamvu,” ndipo anagogomezera mwaphamphu mmene Yehova wadalitsira anthu ake mwa kuwawonjezera mosasamala kanthu za ziyeso zosiyanasiyana. Mbale Sydlik anakamba nkhani ya mutu wakuti “Odala Anthu Amene Mulungu Wawo ndi Yehova.” Nkhani zonse ziŵirizo zinalidi zapanthaŵi yake polingalira za chitsutso chomwe Mboni za Yehova zikuyang’anizana nacho ku France. Mbale Sydlik anafotokoza kuti chimwemwe chenicheni sichidalira pazinthu zakunja ayi koma chimadalira pa unansi wathu ndi Yehova ndiponso mmene ifeyo timaonera moyo. Omvetsera anaomba m’manja mwamphamvu poyankha funso lake lakuti, “Kodi ndinu achimwemwe?”
Mlongo wina yemwe anali “wosoŵa chimwemwe” pambuyo pake analemba kuti: “Mwadzidzidzi ndinazindikira kuti ndingapeze chimwemwe. Ndinali kupanga zoyesayesa zosayenera, ndipo kudzera m’nkhani imeneyi, Yehova anandisonyeza mmene ndingasinthire.” Mbale wina anati: “Tsopano ndikufuna kumenyera zolimba kuti ndisangalatse mtima wa Yehova. Sindikufuna kuti chinthu china chindichotsere chimwemwe chimene ndayamba kumva mkati mwanga.”
Pamene msonkhanowo unafika pamapeto, tcheyamani analengeza mwaphamphu chiŵerengero cha opezekapo: 95,888—kusonkhana kwakukulu koposa kwa Mboni za Yehova m’France!
Atamaliza nyimbo yotsekera, yomwe ambiri anaimba ali ndi misozi yachimwemwe m’maso mwawo, ndiponso litatha pemphero lomaliza, abalewo ananyamuka ulendo wakumudzi koma kwinaku akufuna kumangokhalabe. Anthu ena anaona chikondi ndi ubwenzi wa pamsonkhanopo. Oyendetsa mabasi ananena mawu ambiri olimbikitsa ponena za khalidwe la nthumwizo. Iwo anachitanso chidwi chifukwa cha dongosolo lomwe linatheketsa mabasi 953 kuchoka pa Exhibition Center m’maola aŵiri okha osatsekerezana mpang’ono pomwe! Khalidwe la nthumwizo linayamikiridwanso ndi ogwira ntchito m’masitima ndi m’zoyendera za onse. Panabuka makambitsirano ambiri osangalatsa, ndipo panaperekedwa umboni wabwino.
“Chitsime cha m’Chipululu”
Mtumwi Paulo analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino, . . . tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.” (Ahebri 10:24, 25) Ndithudi, msonkhano wapadera umenewu unali wolimbikitsa kwambiri kwa onse, unali monga “chitsime cha m’chipululu” malinga nkunena kwa mlongo wina. “Tinachokapo titapatsidwa nyonga, kulimbikitsidwa, kumangiriridwa, ndiponso otsimikiza mtima kuposa kale lonse kutumikira Yehova mokondwera,” analemba motero abale a kunthambi ya Togo. “Amene anali osweka mtima anapita kunyumba ali achimwemwe,” anatero woyang’anira dera wina. “Abale anasonkhezeredwa ndi kulimbikitsidwa,” wina anatero. “Kuyambira kalekale sitinadzimveko kukhala oyandikana kwambiri ndi gulu la Yehova monga momwe tachitira,” analemba motero mwamuna wina ndi mkazi wake.
“Phazi langa liponda pachidikha: m’masonkhano ndidzalemekeza Yehova,” anatero wamasalmo. (Salmo 26:12) Misonkhano yachikristu yotere imathandiza onse kupezanso chichirikizo chodalirika chauzimu pakati pa zopinga. “Mosasamala kanthu za zizunzo zimene tidzayang’anizana nazo,” anatsimikiza motero mlongo wina, “zochitika zapadera zimenezi zakhomerezedwa m’mitima mwathu ndipo zidzatitonthoza nthaŵi zonse.” Mofananamo, woyang’anira woyendayenda wina analemba kuti: “Pamene tidzayang’anizana ndi nthaŵi zovuta, chikumbukiro cha chifaniziro chimenechi cha Paradaiso chidzatithandiza kupirira.”
“Mpatseni Yehova, inu, mafuko a mitundu ya anthu, mpatseni Yehova ulemerero ndi mphamvu,” limalimbikitsa motero Salmo 96:7. Mosakayika konse, kupatulidwa kwa nthambi yatsopano ku France kunasonyeza chipambano chachikulu cha Yehova. Ndiye yekhayo amene anapangitsa kuti ntchitoyo itheke pakati pa chitsutso champhamvu ndi chowandacho. Mboni za Yehova ku France zili zotsimikiza mtima kuposa kale lonse ‘kukhalabe m’chikondi cha Kristu’ ndiponso ‘kuŵalitsa kuunika kwawo.’ (Yohane 15:9; Mateyu 5:16) Onse amene anapezeka pa programu yopatulirayo ali ndi malingaliro ofanana ndendende ndi malingaliro a wamasalmo akuti: “Ichi chidzera kwa Yehova; nchodabwiza ichi pamaso pathu.”—Salmo 118:23.
[Chithunzi patsamba 26]
Daniel Sydlik
[Chithunzi patsamba 26]
Lloyd Barry
[Chithunzi patsamba 26]
Anthu 95,888 anapezeka paprogramu yapadera pa Villepinte Exhibition Center
[Zithunzi patsamba 28]
Zikwizikwi za amene anapezekapo anaimirira kapena kukhala pansi penipeni kumvetsera