Kodi Mariya Anafa Imfa Yachibadwa?
MALINGA nkunena kwa nyuzipepala ya ku Vatican yotchedwa L’Osservatore Romano, chiphunzitso chachikatolika cha Kutengeredwa Kumwamba [Assumption] chimati: “Thupi ndi mzimu wa Namwali Wopanda Tchimo, yemwe sanadetsedwe ndi tchimo loyambirira, zinatengeredwa kumwamba mu ulemerero wakumwamba, pamene moyo wake wapadziko lapansi unatha.” Chiphunzitsochi chapangitsa akatswiri ena a zaumulungu achikatolika kulingalira kuti Mariya “sanafe koma anangokwezedwa kuchoka m’moyo wapadziko lapansi kuloŵa mu ulemerero wakumwamba,” inatero nyuzipepalayo.a
Posachedwapa, Papa Yohane Paulo Wachiŵiri anafotokoza malingaliro osemphana ndi chiphunzitsochi. Pa Msonkhano wa Onse womwe unachitikira ku Vatican pa June 25, 1997, iye anati: “Chipangano Chatsopano sichinena chilichonse chokhudza zomwe zinachitika pa imfa ya Mariya. Kusanenapo kanthu kumeneku kungatipangitse kulingalira kuti imfa yakeyo inali yachibadwa, zomwe zinapangitsa kuti pasanenedwe chilichonse chachilendo. . . . Malingaliro onena kuti iye sanafe imfa yachibadwa akuonetsa kuti alibe umboni weniweni.”
Mawu ameneŵa a Papa Yohane Paulo akuvumbula cholakwa chachikulu cha chiphunzitso cha Khalidwe la Munthu Wopanda Tchimo. Ngati amake a Yesu “sanadetsedwe ndi tchimo loyambirira,” kodi Mariya akanafa bwanji “imfa yachibadwa,” yomwe imachitika chifukwa cha tchimo lopatsidwa ndi Adamu wochimwayo? (Aroma 5:12) Kusatsimikiza kumeneku kwa ziphunzitso zachipembedzo kukuchitika chifukwa cha kaonedwe kolakwika ka Tchalitchi cha Katolika ponena za amake a Yesu. Nzosadabwitsa kuona kuti m’Tchalitchi cha Katolika, pali kuwonjezeka kwa magaŵano ndi chisokonezo chifukwa cha nkhaniyi.
Pamene Baibulo limanena kuti Mariya anali wodzichepetsa, wokhulupirika, ndiponso wodzipereka, ilo silinena kuti zimenezi zinachitika chifukwa chakuti anali “wobadwa wopanda tchimo” ayi. (Luka 1:38; Machitidwe 1:13, 14) Baibulo limanena mosapita m’mbali kuti: “Onse anachimwa, naperewera pa ulemerero wa Mulungu.” (Aroma 3:23) Inde, Mariya anali ndi tchimo la choloŵa ndiponso anali wopanda ungwiro mofanana ndi anthu ena onse, ndipo palibe umboni wakuti iye sanafe imfa yachibadwa.—Yerekezerani ndi 1 Yohane 1:8-10.
[Mawu a M’munsi]
a Onani nkhani yakuti “Kutengeredwa Kumwamba—Chiphunzitso Choikidwa Chovumbulidwa ndi Mulungu?” mu Nsanja ya Olonda ya February 15, 1994, masamba 26-9.