Kodi ndi Mlandu Wayani?
Anthu ambiri amaimba mlandu Mulungu kuti ndiye amadzetsa mavuto awo. Mwambi wa m’Baibulo umati: “Uchitsiru wa munthu uwononga moyo wake, kenaka aimba mlandu Ambuye.” (Miyambo 19:3, The New English Bible) Komabe, kulingalira kuti Mulungu ndiye amadzetsa masoka a munthu nkofanana ndi kuimba mlandu wokonza galimoto kuti ndiye amapangitsa ngozi zochuluka zomwe zimagwera anthu chifukwa choyendetsa galimoto ataledzera.
Mulungu anapatsa anthu chitsogozo chothandiza chopezeka m’Mawu ake, Baibulo. Mwa kuphunzira nkhokwe imeneyi ya mabuku ndi kukhala mogwirizana ndi malamulo ndi mapulinsipulo opezeka mmenemo, tingapeŵe mavuto ambiri a m’moyo. Koma kuchita zinthu mosiyana ndi chitsogozo cha Mulungu kumadzetsa mavuto. Mwachitsanzo, anthu amadyaidya, osuta, amamwaimwa, kapena anthu ochita zinthu zoipa nthaŵi zambiri amadzetsa mavuto pa thanzi lawo. (Luka 21:34; 1 Akorinto 6:18; 2 Akorinto 7:1) Mtumwi wachikristuyo Paulo analemba kuti: “Chimene munthu achifesa, chimenenso adzachituta. Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m’thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.”—Agalatiya 6:7, 8.
Nkopindulitsadi kwambiri kukhala mogwirizana ndi malamulo ndi mapulinsipulo a Mulungu! Ngati tichita zimenezo, tidzaona kuti lonjezo la Mulungu lonenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya nloonadi, pamene anati: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo. Mwenzi utamvera malamulo anga mtendere wako ukanakhala ngati mtsinje, ndi chilungamo chako monga mafunde a nyanja.”—Yesaya 48:17, 18.