Kukhala ndi Kulalikira Pafupi ndi Volokano
“NZOCHITITSA mantha. Zingakhale ngati mapeto a dziko amene Baibulo limanena. Tifunikira kukhala maso nthaŵi zonse ndi kukhalanso ndi kaimidwe kabwino pamaso pa Yehova Mulungu.” Ananena motero Víctor, mmodzi wa Mboni za Yehova, polongosola zimene anaona mwa kukhala pafupi kwambiri ndi volokano yotchedwa Popocatépetl, yodziŵikanso kuti Popo, ku Mexico.
Volokano yosokosera imeneyi yakhala ikusimbidwa m’maiko ambiri chiyambire 1994.a Akuluakulu aboma analengeza kuti chilichonse chimene chili pamtunda wa makilomita 30 kuchokera pamalo amene phirilo limaphulikira chili m’dera langozi kwambiri. Mbali yakumwera ya phirilo ndi yoopsadi chifukwa malo ophulikira a phirilo adapendekera chakumeneko ndipo kuli makwaŵa ambiri mmene matope a volokanoyo angadzere kuchokera pamalo ophulikirawo.
Kwenikweni anthu ambiri amadabwa kuti nchiyani chikanachitikira Mzinda wa Mexico ngati phirilo likanaphulika kwambiri. Kodi mzindawo uli pangozi? Ndiye palinso anthu amene akukhala m’dera la Morelos kumwera kwa phirilo. Kodi anthu onse a m’dera limeneli alinso pangozi? Ndipo kodi zimatha bwanji pamene anthu akhala m’tsinde mwa volokano osadziŵa chimene chingachitike tsiku ndi tsiku?
Kuopsa kwa Volokanoyi
Mzinda wa Mexico uli pamtunda wa makilomita pafupifupi 70 kumpoto chakumadzulo kwa Popocatépetl, ngakhale kuti madera ena a mzindawo ali pamtunda wa makilomita 40 chabe. Malinga nkunena kwa akuluakulu a boma, dera lonse la mzindawo, lokhala ndi anthu 20,000,000, silili m’dera langozi. Komabe, mogwirizana ndi mmene mphepo ingayendere, mzindawu ungakhudzidwe ngati phirilo litatulutsa phulusa lochuluka.
Kaŵirikaŵiri phulusa la m’phirimo limavutitsa kwambiri mbali ya kummaŵa kwa phirilo. M’dera limeneli muli mzinda wa Puebla ndi mizinda ndi matauni ena ang’onoang’ono angapo, kumene kuli anthu pafupifupi 200,000 amene akukhala m’dera langozi kwambiri. Lamlungu, pa May 11, 1997, phirili linatulutsa phulusa lochuluka kwambiri limene linagwera m’dera lonse limeneli, mpaka kukafika m’dera la Veracruz, lomwe lili chakummaŵa pamtunda wa makilomita oposa 300. Kumwera kwa phirili, m’dera la Morelos, kuli mizinda ndi matauni ochuluka amene ali ndi anthu pafupifupi 40,000 amene angakhalenso pangozi kwambiri.
Mboni za Yehova zikukhala ndi kugwira ntchito m’malo ameneŵa. Mu Mzinda wa Mexico zilimo zoposa 90,000 m’mipingo ngati 1,700. Nthambi ya Watch Tower Society ili kumpoto chakummaŵa kunja kwa Mzinda wa Mexico, pamtunda wa makilomita pafupifupi 100 kuchokera kuvolokanoyo. Antchito odzifunira oposa 800 akutumikira panthambipo, kuphatikizaponso ena 500 omwe akugwira ntchito yachimango chachikulu. Onseŵa sali m’dera langozi.
M’dera la Morelos, muli mipingo pafupifupi 50 ya Mboni za Yehova momwe muli ofalitsa Ufumu oposa 2,000. Ina mwa mipingoyi, yomwe ili ku Tetela del Volcán ndi Hueyapan, ili pamtunda wa makilomita pafupifupi 20 kuchokera pamalo amene phirilo limaphulikira. Ndiponso, chakummaŵa m’dera la Puebla, kuli mipingo yomwe ili ndi ofalitsa pafupifupi 600 omwe akukhala pamtunda wa makilomita 20 kufika 30 kuchokera kuphirilo. Mipingo imeneyi ingakhaledi pangozi yaikulu.
Mboni za Yehova Zili Zokangalikabe
Mboni za Yehova m’derali sizinaleke ntchito yawo yolalikira ngakhale kuti nkoopsa tero. Zatsatiranso ndandanda yawo ya misonkhano yachikristu, imene imawapangitsa kumva kukhala ogwirizana ndi odalirana m’mikhalidwe yovuta imeneyi. (Ahebri 10:24, 25) Mpingo wina unatumiza lipoti ili: “Anthu asintha kwambiri maganizo awo pa uthenga wabwino wa Ufumu. Mwachitsanzo, pamudzi wina waung’ono anthu 18 anavomera maphunziro a Baibulo a panyumba.”
Mpingo wina, womwe uli pamtunda wa makilomita 20 kuchokera kuvolokanoyo, unati: “Tawonjezereka kwambiri. Mpingo uno unakhazikitsidwa mu November 1996. Patangotha miyezi isanu ndi umodzi, anthu 10 anayeneretsedwa kumachita nawo utumiki wa kumunda. Ofalitsa ena amakhala pamtunda wa makilomita pafupifupi 20 chabe kuchokera pamalo amene phirilo limaphulikira. Misonkhano yachikristu imachitikanso kumeneko, ndipo amakhala ndi anthu pafupifupi 40 opezekapo.”
Magdalena, amene amakhala ku San Agustín Ixtahuixtla, Puebla, makilomita 25 okha kuchokera kuphirilo, wakhala akuchititsa maphunziro a Baibulo mokangalika. Analongosola zimene zinachitika tsiku lina phirilo litaphulika kwambiri.
“Tinadziŵitsidwa kuti tichoke m’nyumba zathu, ndipo tinachokadi—phulusa lili kugwa. Ngakhale kuti zinali zadzidzidzi, ndinaganizira za banja la a Dorado limene ndimaphunzira nalo Baibulo. Ndinapita ndi abale ena kunyumba kwa a Dorado kukawathandiza kusamukira kumalo otetezereka. Mu mzinda wapafupi nawo wa Puebla, komiti yopereka chithandizo ya Mboni za Yehova inali itakonzeka kale. Banja la a Dorado linachita chidwi kwambiri ndi mmene tonse anatilandirira kumeneko. Tinapatsidwa malo ogona m’malo osiyanasiyana amene abale athu achikristu anali atatikonzera kale. Ngakhale kuti tinali kutali ndi kwathu, palibe chomwe chinali kutisoŵa. Banjali linafikapo pamisonkhano ingapo ku Nyumba ya Ufumu, koma anadabwa kuti abale omwe anali asanawaonepo anali kuwasonyeza chikondi. Milungu ingapo titabwerera kwathu, banjali linayamba kufika pamisonkhano yonse mokhazikika. Posakhalitsa anayeneretsedwa kukhala ofalitsa uthenga wabwino. Aŵiri mwa iwo anabatizidwa. Atumikirapo monga apainiya othandiza kwa miyezi ingapo ndipo akukonzekera kuti ayambe utumiki waupainiya wokhazikika.”
Martha, mtsikana wazaka 20 amene amakhala pamtunda wa makilomita 21 kuchokera pamalo pamene phirilo limaphulikira, sanalole kuti kulemala kumlepheretse kulalikira pampata uliwonse. Anaphunzira choonadi zaka zitatu zapitazo pamene phirilo linayambanso kuphulika. M’malo mogwiritsa ntchito njinga ya anthu olemala, imene ingakhale yovuta kugwiritsa ntchito kumalo otsetsereka kumene amakhala, amakwera pabulu kupita kukalalikira. Amapitanso kumisonkhano pabuluyo. Martha ndi woyamikira kwambiri kwa Yehova kuti ali mu ubale wachikondi, popeza kuti amadalira alongo a mumpingo kumthandiza kukwera ndi kutsika pabuluyo. Mwezi uliwonse amathera maola oposa 15 ali mu utumiki.
M’malo akutali ameneŵa, Mboni za Yehova kaŵirikaŵiri zimavutitsidwa ndi anthu a pamudzi kuti azichita nawo mapwando a maholide a chipembedzo. Ku Tulcingo, mudzi womwe uli pamtunda wa makilomita 20 kuchokera kuphirilo, munthu wina anatumidwa kuti akatenge zopereka za mapwandowo kwa Mboni. Mofatsa abale anamlongosolera chifukwa chake iwo sangachite nawo maholide a chipembedzo. Munthuyo anaumirira kwambiri kuti atenge ndalamazo kwa abalewo kotero kuti anayamba kugwirizana nawo, namazindikira zikhulupiriro zawo. Anasangalala kupeza mayankho a mafunso ake m’Baibulo lake lachikatolika. Iye, mkazi wake ndi mwana wawo wamkazi, akhala akufika pamisonkhano mokhazikika kwa chaka tsopano ndipo mwamunayo wasonyeza kuti akufuna kukhala wofalitsa wa uthenga wabwino.
Kodi Mungakonzekere Motani?
Akatswiri ofufuza za volokano amafufuza ndi kutulutsa lipoti lokhudza kuopsa kwa Popocatépetl, koma palibe aliyense amene amadziŵadi zimene zidzachitika kaya kuti zidzachitika liti. Malinga ndi zimene ofalitsa nkhani ndi anthu okhala pafupi ndi phirilo amanena, volokanoyo ingathovoke nthaŵi iliyonse. Nzoopsadi. Zoonadi, akuluakulu a boma ndi okhudzidwa kwambiri ndipo amafuna kuchita chilichonse chimene angathe kuti akhale okonzeka kuthandiza ngati phirilo litaphulika mwadzidzidzi. Koma nzomveka kuti ayenera kupereka chenjezo mwanzeru popeza kuti safuna kuchititsa gulu la anthu kuyamba kusamuka pamene ngoziyo sili pafupi kuchitika. Nanga kodi munthu angachitenji?
Mwambi wa m’Baibulo umati: “Wochenjera aona zoipa, nabisala; koma achibwana angopitirira, nalipitsidwa.” (Miyambo 22:3) Choncho njira yanzeru ndiyo kuchita zinthu zofunikira kuti munthu utsimikizire kuti uli pamalo otetezereka pamene mwayiwo udakalipo, ‘osangopitirira’ ngati kuti palibe chimene chidzachitika, mukumaseŵera ndi mphamvu zachilengedwe zoopsa zoterozo. Mboni za Yehova kumeneko zimaganiza choncho pankhaniyi.
Posachedwapa, oimira Watch Tower Society ochokera kunthambi ya m’dzikolo anakumana ndi oyang’anira oyendayenda m’dera la Puebla, amene amafika kumipingo imene ili m’dera langozilo. Anagwirizana kuti oyang’anira oyendayendawo ndi mamembala a komiti yopereka chithandizo akacheze ndi banja lililonse limene likukhala pamtunda wa makilomita 25 kuchokera pamalo amene phirilo limaphulikira. Mabanjawa anathandizidwa kulingalira za kusamuka m’dera langozilo zisanafike povuta. Kayendedwe ndi malo ogona anakonzedwa kuti anthu 1,500 asamukire mu mzinda wa Puebla. Mabanja ena anakakhala ndi achibale awo m’mizinda ina.
Chenjezo Lokulirapo
Utsi, moto, ndi kugunda kwa Popocatépetl ndi umboni waukulu wakuti phirilo latsala pang’ono kuphulika. Onse amene akufuna kupulumuka ayenera kulabadira machenjezo operekedwa ndi akuluakulu aboma ndi kutsatira malangizo mosamalitsa. Mboni za Yehova zomwe zili m’dera limene phirilo lingaphulikire zimakhala zatcheru nthaŵi zonse kuti zitsimikizire kuti zili zotetezereka ndi kutinso zithandize ena kuona ngoziyo ndi kuchitapo kanthu mwamsanga.
Pamlingo wokulirapo, Mboni za Yehova zili zatcheru ku zochitika zadziko mogwirizana ndi maulosi a Baibulo. Nkhondo, zivomezi, njala, matenda, ndi upandu zili zowononga mofanana ndi zochitika za volokano. Ndi mbali ya zizindikiro zosiyanasiyana zimene Yesu Kristu ananena kuti zidzasonyeza “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano.” Ngakhale kuti palibe aliyense amene akudziŵa nthaŵi yeniyeni imene mapetowo akubwera, ndi zosakayikitsa kuti abweradi ndipo alidi pafupi kwambiri.—Mateyu 24:3, 7-14, 32-39.
Chofunika kwambiri lerolino nchakuti anthu kulikonse komwe ali alabadire chenjezo la Yesu lakuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha.” (Luka 21:34) Mwachionekere imeneyi ndi njira yanzeru kuitsatira. Monga mmene zizindikiro za kuphulika kwa phiri siziyenera kutengedwa mopepuka, sitiyenera kunyalanyaza kufika kwa Mwana wa munthu, Yesu Kristu, amene analimbikitsa kuti: “Chifukwa chake khalani inunso okonzekeratu; chifukwa munthaŵi mmene simuganizira, Mwana wa munthu adzadza.”—Mateyu 24:44.
[Mawu a M’munsi]
a Magazini ya Galamukani! ya March 8, 1997 (Chingelezi), inanenapo za volokano yoopsayi.
[Zithunzi patsamba 23]
Martha (ali pabuluyo) pamodzi ndi ena akuchitira umboni pafupi ndi Popocatépetl