Ntchito ‘Yoyeneradi Kulemekezedwa’
MTUMWI Petro analimbikitsa Akristu anzake kuti: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino.” (1 Petro 2:12) Kwa zaka zambiri Mboni za Yehova ku Italy zasonyeza mayendedwe abwino amenewo poyera. Motsatira tanthauzo la malangizo a Yesu a ‘kulalikira pamachindwi a nyumba,’ iwo amachita ntchito yawo yonse yachikristu poyera, moonekera kwa onse. (Mateyu 10:27; Yohane 18:20) Chotero, pamene loya wachitaliyana ndi wansembe wina anafalitsa zinenezo zonena kuti Mboni za Yehova ndi “kagulu kosakhala kachipembedzo chenicheni” ndi kunena kuti ndi amodzi mwa “magulu achinsinsi amene amakola anthu,” Mboni zinawasumira mlandu chifukwa cha mawu awo oipitsa dzina lawo.
Atawazenga mlandu nthaŵi yoyamba, bwalolo linagamula kuti loyayo ndi wansembeyo sanaswe lamulo lililonse. Komabe, pa July 17, 1997, Bwalo la Apilo la ku Venice linatsutsa chigamulo cha bwalo loyambalo, ndipo linawapezadi ndi mlandu anthu aŵiriwo. Bwalo la Apilo linati: “Nkhani zonse ziŵiri zofalitsidwazi zili ndi mawu amene angaipitsedi mbiri ya otsatira chipembedzo cha ‘Mboni za Yehova.’ Nzoonekeratu kuti cholinga cha nkhanizo chinali chonyazitsa otsatira chipembedzochi pamaso pa anthu onse.” Bwalolo linanena kuti nkhanizo “sizinalembedwe monga mwa ufulu wa utolankhani ndi kutsutsa mwalamulo.” Bwalo limenelo linalipiritsa faindi oneneza aŵiriwo ndi kuwalamulanso kuti alipire ndalama zonse zimene bwalo linatayirapo pa mlanduwo, kuphatikizapo ndalama zonse zimene Mboni zinatayirapo pamilandu yonse iŵiri.
M’chigamulo chake cholembedwa, Bwalo la Apilo la ku Venice linati: “Kusalolera ndiponso kutengeka maganizo ndi chipembedzo kungaletsedwe kokha mwa kusamala ndi kuchirikiza ufulu wonse woperekedwa ndi Malamulo [a Italy].” Chigamulo chimenecho chikusonyezadi kuti ntchito ya Mboni za Yehova si yachinsinsi kapena yosakhala yachipembedzo. “Kunena kuti a Mboni nawonso ndi gulu lachinsinsi,” linatero bwalolo, “ndiko kusalemekeza ngakhale umboni woperekedwa ndi zimene zachitikadi m’mbiri, chifukwa chakuti chipembedzo chimenechi chikupezeka m’mizinda yambiri ndipo ntchito yofala yotembenuza anthu imene imachitidwa ndi mamembala ake, makamaka pamasiku a Lamlungu ndi pamaholide ena, njodziŵika kwambiri ndipo njoyeneradi kulemekezedwa chifukwa cha kuyesayesa kwawo, mosasamala kanthu za zimene munthu angaganize ponena za chiphunzitso chimene amalalikira.” Chotero, mbiri ya ulaliki wachangu ndi mayendedwe abwino a Mboni za Yehova ku Italy zathandizira kutsutsa malingaliro oipa a anthu.—Mateyu 5:14-16; 1 Petro 2:15.