“Wabala Ndani Madontho a Mame?”
MTOLANKHANI wina wa m’zaka za zana la 19 anafotokoza kuti madontho a mame ndiwo “majuwelo amadzi a dziko lapansi, opangidwa ndi mphepo.” Mlengi wathu anafunsa kholo lakale Yobu kuti: “Wabala ndani madontho a mame?” (Yobu 38:28) Mulungu anali kukumbutsa Yobu kuti mame amtengo wapataliwo analengedwa ndi Mulungu.
Kusiyapo kukongola kwake konyezimira konga majuwelo, m’Baibulo, mame amaimira madalitso, chonde, kuchuluka, ndi kusungidwa kwa moyo. (Genesis 27:28; Deuteronomo 33:13, 28; Zekariya 8:12) M’nyengo yotentha, ndiponso yopanda mvula ya ku Israyeli, “mame a ku Hermoni” anachirikiza zomera za m’dzikolo, ndipo motero anachirikizanso anthu ake. Phiri la Hermoni lokhala ndi nkhalango ndi chipale chofeŵa pamwamba pake limatulutsabe nthunzi imene imasandulika kukhala mame ambiri. Wamasalmo Davide anayerekezera chitsitsimulo chimene mame ameneŵa amadzetsa ndi kukondweretsa kwa kukhala pamodzi ndi olambira anzathu a Yehova.—Salmo 133:3.
Malangizo a mneneri Mose kwa Israyeli anali abwino ndiponso otsitsimula, ngati madontho a mame. Iye anati: “Maneno anga agwe ngati mame; ngati mvula yowaza pamsipu, ndi monga madontho a mvula pazitsamba.” (Deuteronomo 32:2) Lerolino, Mboni za Yehova zikulengeza uthenga wopatsa moyo wonena za Ufumu wa Mulungu kumalekezero a dziko lapansi. (Mateyu 24:14) Mulungu akupereka chiitano chakuti: “Idzani. Ndipo wakumva ludzu adze; iye wofuna, atenge madzi a moyo kwaulere.” (Chivumbulutso 22:17) Anthu mamiliyoni ambiri m’mitundu yonse akulandira chitsitsimulo chauzimu chochokera kwa Mulungu, chimene chingachirikize moyo kwamuyaya.