Pamene Mitima Yonga Mwala Imvetsera
MU 1989, MBONI ZA YEHOVA KU POLAND zinaloledwa mwalamulo monga gulu lachipembedzo. M’kupita kwa nthaŵi, Mboni zimene zinamangidwa chifukwa cha uchete wawo wachikristu zinamasulidwa ndipo zinasiya akaidi anzawo ambirimbiri amene anafuna kuphunzira zambiri ponena za Baibulo kwa Mbonizo. Nayi nkhani ya mmene kundende ina yotero, Mboni za Yehova zimayesetsera kuthandiza awo amene poyamba anali ndi mitima yonga mwala kuti ikhudzidwe ndi mphamvu ya Mawu a Mulungu.
KU WOŁÓW, tauni yokhala ndi anthu 12,000 kummwera cha kumadzulo kwa Poland, kuli ndende ina yazaka 200 kumene ena mwa apandu ovutitsa kwambiri a m’Poland amawasungira. Kuyambira pamene ntchito ya Mboni za Yehova inaloledwa mwalamulo, izo zayesetsa kubweretsa uthenga wabwino wa Ufumu kwa akaidi a kumeneko, ndipo amachita zimenezo ndi changu chochititsa chidwi.
Choyambitsa zimenezi ndi kalata ya Unduna wa Zachilungamo m’February 1990 yolembedwa kwa oyang’anira ndende onse m’Poland. Kalatayo inawauza kuti iwo sayenera “kuvutitsa” akaidi alionse ofuna kulandira zofalitsa za Watch Tower kapena ofuna kuonana ndi Mboni za Yehova. Mboni, zina pokhala kuti zinakhalamo zaka zambiri m’ndende ya Wołów, zinali kuwadziŵa bwino apandu ambiri ovuta kwambiri amene anali m’ndendeyo. Komabe, iwo anadalira Yehova kuti adalitse zoyesayesa zawo kuti achititse choonadi cha Baibulo kufeŵetsa mitima yolimba ngati mwala ya akaidi ena.
Kuiyamba Ntchitoyo
“Tinavutika kuti tiyambitse pologalamu imeneyi,” anatero Mbale Czesław amene analoledwa kumachezera ndende ya ku Wołów. Iye amakhala mumzinda wa Wrocław, umene uli pamtunda wamakilomita ngati 40. “Tinakhala ndi makambitsirano ataliatali ambirimbiri ndi oyang’anira ndende kuti aone kuti ‘mapemphero’ athu adzapindulitsa akaidi.”
Kuwonjezera pavutoli, akukumbukira motero Paweł wantchito mnzake wa Czesław, “ofisala wina wamkulu analimbikira kunena kuti akaidi amangonamizira mapemphero pamene kwenikweni amafunako zinthu zakuthupi.” Koma pamene anthu atatu amene poyamba anali apandu oopsa anadzipereka kuti abatizidwe mu 1991, oyang’anira ndende anasintha malingaliro awo, ndipo tinayamba kugwirizana bwino.
“Tinayamba mwa kuchitira umboni kwa akaidi, kwa mabanja awo amene anali kudzawachezera m’ndendemo, ndiponso kwa oyang’anira ndende,” akufotokoza motero Czesław. “Ndiyeno tinaloledwa kumalalikira uthenga wabwino m’zipinda zonse zandende, chinthu chachilendo kwambiri. Pomalizira pake, titapeza ochita chidwi oyambirira, tinapatsidwa holo ina yaing’ono yochititsiramo maphunziro a Baibulo ndi kuchitiramo misonkhano yachikristu.” Inde, Yehova anatsegula njira yofikira mitima yonga mwala ya akaidi.
Pologalamu Yamaphunziro Yothandiza Kwambiri
Posapita nthaŵi holo yaing’ono imeneyo inacheperatu. Popeza kuti akaidi obatizidwa ndiponso abale ochokera kunja onse anali kuchita ntchito yolalikira, akaidi ambiri okwanira 50 anayamba kupezeka pamisonkhano. “Kwa zaka zoposa zitatu, tinkachitira misonkhano yonse mmenemo, ndipo nthaŵi zonse akaidiwo anali kupezeka pamisonkhano yamlungu ndi mlungu,” anafotokoza motero mmodzi mwa akulu akumeneko. Choncho m’May 1995 anawapatsa holo ina yaikulu kuti aziigwiritsira ntchito.
Kodi abale otsogolera amamdziŵa bwanji munthu amene angathe kumabwera kumisonkhano ya m’ndendemo? “Tili ndi mpambo wa akaidi osonyeza chidwi chenicheni ndi choonadi,” akufotokoza motero Mbale Czesław ndi Mbale Zdzisław. “Ngati mkaidi sakupita patsogolo kapena ngati amaphonya misonkhano popanda zifukwa zomveka, motero akumasonyeza kuti sayamikira makonzedwe ameneŵa, timamfafaniza pampambowo ndi kuuza woyang’anira ndende wamkulu.”
Pamaphunziro awo a Baibulo, abale amaphunzitsanso akaidiwo mmene angakonzekerere bwino misonkhano ndi mmene angagwiritsirire ntchito bwino mabuku athu. Choncho, pamene akaidi abwera kumisonkhano, amakhala okonzekera bwino ndipo amatengamo mbali momasuka. Amapereka ndemanga zolimbikitsa, kugwiritsira ntchito Mabaibulo awo mwaluso, ndi kumaona uphunguwo monga wawowawo, nthaŵi zambiri m’ndemanga zawo akumaphatikizamo mawu monga akuti, ‘Ndaona kuti ndiyenera kumachita zakuti ndi zakuti.’
“Maphunziro a Baibulo 20 onse pamodzi akuchititsidwa m’ndende ya ku Wołów. Asanu ndi atatu mwa amenewo akuchititsidwa ndi akaidi ofalitsa asanu ndi atatu,” akutero mlembi wa mpingowo. Iwo akhalanso ndi zotsatirapo zabwino polalikira kuchipinda ndi chipinda ndiponso poyendayenda m’ndendemo. Mwachitsanzo, pamiyezi khumi, kuyambira m’September 1993 mpaka m’June 1994, iwo anagaŵira mabuku 235, pafupifupi mabrosha 300, ndi magazini 1,700. Posachedwapa, aŵiri mwa oyang’anira ndende anapempha kuti akhale ndi maphunziro a Baibulo.
Misonkhano Yapadera Idzetsa Chimwemwe
M’kupita kwa nthaŵi, anawonjezerapo mbali ina papologalamu imeneyo yophunzitsa m’ndende, ndiyo misonkhano yapadera. Oyang’anira oyendayenda ndi abale ena ofikapo anali kupereka nkhani zazikulu za mapologalamu a msonkhano wadera ndi msonkhano wapadera watsiku limodzi m’nyumba ya maseŵero olimbitsa thupi. Msonkhano wapadera woyamba unachitika mu October 1993. Akaidi 50 anapezekapo, ndiponso “mabanja athunthu, kuphatikizapo akazi ndi ana aang’ono, abwera kuchokera ku Wrocław,” inatero nyuzipepala yotchedwa Słowo Polskie, ndipo onse pamodzi anali 139. Nthaŵi ya kupuma papologalamu ya msonkhanowo inawapatsa mpata wodya chakudya chokonzedwa ndi alongo, ndiponso mayanjano abwino achikristu.
Misonkhano yapadera inanso isanu ndi iŵiri yoteroyo inachitidwanso kuyambira pamenepo, ndipo mapindu ake sanafike chabe kwa a m’ndendewo komanso kwa anthu akunja kwa ndende. Pamene Mboni ina yaikazi inafikira munthu amene kale anali m’ndende ya Wołów amene tsopano amakhala m’tauni, munthuyo poyamba sanafune. Koma pamene anauzidwa kuti mkaidi winawake wakhala Mboni, mwamunayo anadabwa kuti: “Wakupha uja tsopano ndi Mboni?” Pachifukwa chimenecho, iye analola phunziro la Baibulo.
Kusandulika Kodabwitsa Kuchitika
Kodi pologalamu yaikulu yophunzitsa imeneyi yafeŵetsadi mitima yonga mwala ya akaidi? Aloleni adzisimbire okha.
“Makolo anga sindinkawadziŵa chifukwa chakuti ananditaya ndili wamng’ono, ndipo ndinali kupwetekedwa mtima kwambiri kuti panalibe wondikonda,” anatero mosabisa Zdzisław, mwamuna woganiza kwambiri mwachibadwa. “Ndidakali wamng’ono, ndinayamba kuchita zaupandu, ndipo m’kupita kwa nthaŵi ndinapha munthu. Kudziimba mlandu kunandisonkhezera kulingalira za kudzipha, ndipo ndinalakalaka chiyembekezo chenicheni. Ndiyeno, mu 1987, ndinapeza magazini ya Nsanja ya Olonda. M’magazini imeneyo ndinaphuziramo za chiyembekezo cha chiukiriro ndi cha moyo wosatha. Nditazindikira kuti panali padakali chiyembekezo, ndinasiya kuganiza za kudzipha ndipo ndinayamba kuphunzira Baibulo. Tsopano Yehova ndi abale andiphunzitsa tanthauzo la chikondi.” Kuchokera mu 1993, munthu ameneyu amene kale anali wakupha wakhala mtumiki wotumikira ndiponso mpainiya wothandiza, ndipo chaka chatha anakhala mpainiya wokhazikika.
Nayenso Tomasz analandira phunziro la Baibulo mosavuta. “Koma zimenezo sizinali zochokera pansi pa mtima,” iye anatero mosapita m’mbali. “Ndinali kuphunzira kokha chifukwa chakuti ndinali kukonda kudzionetsera pofotokozera ena zikhulupiriro za Mboni za Yehova. Koma choonadi cha Baibulo sindinali kuchitsatira. Tsiku lina, ndinaganizaganiza ndiyeno ndinasankha kupita kumsonkhano wachikristu. Akaidi obatizidwa anandilandira ndi manja aŵiri. Ndinazindikira kuti m’malo moyesa kudzionetsera ndi chidziŵitso changa ndinayenera kufeŵetsa mtima wanga wonga mwala ndi kusanduliza maganizo anga.” Tomasz anayamba kuvala umunthu watsopano wachikristu. (Aefeso 4:22-24) Lerolino, ndi Mboni yodzipatulira, yobatizidwa ndipo amasangalala ndi kulalikira kuchipinda ndi chipinda.
Kuvutitsidwa ndi Mabwenzi Akale
Awo amene anaphunzira choonadi cha Baibulo m’ndende anavutitsidwa koopsa ndi anthu amene kale anali mabwenzi awo m’zipinda zawo ndiponso ndi oyang’anira ndende. Mmodzi mwa iwo anati: “Anali kundinyoza ndi kunditukwana nthaŵi zonse. Koma ndinali kukumbukira mawu olimbikitsa a abale. Iwo anandiuza kuti ‘Musaleke kupemphera kwa Yehova. Muziŵerenga Baibulo lanu ndipo mudzakhala pamtendere mumtima mwanu.’ Zimenezo zinandithandiza kwambiri.”
“Akaidi anzanga anali kungondinyoza,” anatero Ryszard mbale wolimbikira wobatizidwa. “Iwo anali kundichenjeza kuti: ‘Uzipita kumisonkhano yako, koma osayesa kudzionetsera ndi kudziyesa wabwino kuposa ena, wamva?’ Pamene ndinasintha makhalidwe anga chifukwa cha kugwiritsira ntchito mapulinsipulo a m’Baibulo, ndinavutikirapo. Anagudula bedi langa, kumwazamwaza mabuku anga ofotokoza Baibulo, ndi kuipitsa mbali yanga ya chipinda chathu. Ndinapemphera kwa Yehova kuti andipatse nyonga ndi kudziletsa ndiyeno ndinayamba kuyeretsa mbali yangayo popanda kunena kalikonse. Pambuyo pake, iwo anasiya kundivutitsa.”
“Akaidi anzathu akaona kuti tatsimikiza mtima kutumikira Yehova,” anasimba motero akaidi ena obatizidwa, “mavutowo amasintha. Amayamba kunena kuti, ‘Uzikumbukira kuti tsopano suyenera kumwa, kusuta, kapena kunama.’ Mavuto ngati amenewo amakuthandiza kulamulira thupi lako, kusiya msanga makhalidwe oipa kapena kumwerekera kulikonse. Zimakuthandizanso kukulitsa zipatso za mzimu.”—Agalatiya 5:22, 23.
Kukhala Atumiki a Mulungu Odzipatulira
Mwa chilolezo cha oyang’anira ndende, ubatizo woyamba unachitikira m’nyumba yamaseŵero m’ngululu ya 1991. Zdzisław ndiye anali wopita kuubatizo ndipo anali wachimwemwe. Akaidi 12 anapezekapo, ndipo abale ndi alongo 21 ochokera kunja anapezekapo pachochitikacho. Msonkhanowo unawalimbikitsa kwambiri akaidiwo. Ambiri a iwo anapita patsogolo kwambiri moti akaidi enanso aŵiri anabatizidwa pambuyo pake chaka chomwecho. Patapita zaka ziŵiri, mu 1993, ubatizo unachitika kaŵiri, ndipo akaidi enanso asanu ndi aŵiri anasonyeza kudzipatulira kwawo kwa Yehova!
Posimba za ubatizo umene unachitika m’December, nyuzipepala yakomweko yotuluka masiku onse, Wieczór Wrocławia, inati: “Anthu akudzazana m’nyumba yamaseŵeroyo, onse akumapatsana moni ndi kugwirana chanza. Kulibe mlendo. Iwo akupanga banja limodzi lalikulu, ogwirizana m’maganizo awo, makhalidwe awo, ndiponso pakutumikira Mulungu mmodzi, Yehova.” “Banja limodzi lalikulu” limenelo panthaŵiyo linali ndi anthu 135, kuphatikizapo akaidi 50. Tiyeni tionane ndi ena a iwo.
Jerzy, amene anabatizidwa m’June, anasimba kuti: “Ngakhale kuti choonadi cha Baibulo ndinachimva zaka zambiri kumbuyoko, kwenikweni mtima wanga unali wamwala. Chinyengo, kusudzula mkazi wanga woyamba, chiwerewere ndi Krystyna, mwana wapathengo, ndi kuponyedwa m’ndende kaŵirikaŵiri—ndiwo unali moyo wanga.” Ataona mmene apandu ena oopsa anakhalira Mboni adakali m’ndende, iye anayamba kudzifunsa kuti: ‘Kodi inenso sindingakhale mwamuna wabwinopo?’ Anapempha kukhala ndi phunziro la Baibulo nayamba kupezeka pamisonkhano. Komabe, zinthu zinadzasinthiratu atamva kwa loya wina waboma kuti Krystyna anakhala mmodzi wa Mboni za Yehova zaka zitatu zapitazo. “Ndinazizwa kotheratu!” anatero Jerzy. “Ndinalingalira kuti: ‘Nanga ine? Kodi ndikutani?’ Ndinaona kuti ngati ndikufuna kuti Yehova andiyanje ndiyenera kukonza moyo wanga.” Chotero, panali kuyanjananso kosangalatsa m’ndende—iyeyo ndi Krystyna ndi mwana wawo wamkazi wazaka 11, Marzena. Posapita nthaŵi, analembetsa ukwati wawo. Ngakhale kuti adakali m’ndende ndipo akukumanabe ndi zovuta, Jerzy posachedwapa anadziphunzitsa chinenero cholankhula ndi manja ndipo akuthandiza akaidi ogontha.
Mirosław anayamba zaupandu adakali pasukulu ya pulaimale. Ankatengeka maganizo kwambiri ndi zimene anzake anali kuchita, ndipo posapita nthaŵi anayamba kuchita zomwezo. Iye anafwamba kapena kumenya anthu ambiri. Ndiyeno anaponyedwa m’ndende. “Nditapeza kuti ndili m’ndende, ndinapita kwa wansembe wina kuti azindithandiza,” anatero Mirosław. “Koma anandikhumudwitsa kwambiri. Choncho ndinaganiza zodzipha mwa kumwa poizoni.” Patsiku lomwe anafuna kudziphalo, anasamutsidwira ku chipinda china. Kumeneko anakapezako kope la Nsanja ya Olonda limene linali kunena za cholinga cha moyo. “Ndinaona kuti chidziŵitso chake chosavuta kumvacho nchimene ndinali kufunikira,” anawonjezera motero. “Tsopano ndinafuna kukhala ndi moyo! Choncho ndinapemphera kwa Yehova ndi kupempha Mboni kuti ndikhale ndi phunziro la Baibulo.” Iye anapita patsogolo mwamsanga paphunziro lake la Baibulo ndipo anabatizidwa mu 1991. Tsopano akutumikira monga mpainiya wothandiza m’ndendemo, ndipo anapatsidwa mwayi wolalikira kuchipinda ndi chipinda.
Kudzafika pano, akaidi 15 onse pamodzi anabatizidwa. Zaka zawo zokhala m’ndende zonse pamodzi zifika 260. Ena anamasulidwa asanakwanitse zaka zawo. Chilango cha mkaidi wina cha zaka 25 chinachepetsedwa ndi zaka 10. Ndiponso ambiri amene anasonyeza chidwi m’ndende anakhala Mboni zobatizidwa atamasulidwa. Ndiponso, pali akaidi enanso anayi m’ndendemo amene akukonzekera ubatizo.
Oyang’anira Ndende Avomereza
“Kusintha maganizo kwa akaidiwo kumaonekeratu,” linatero lipoti la ndendeyo. “Ambiri amasiya kusuta, ndipo zipinda zawo zimakhala zaudongo. Kusintha khalidwe kumeneku kumaonekera mwa akaidi ambiri.”
Nyuzipepala yotchedwa Życie Warszawy inanena kuti oyang’anira ndende ya ku Wołów anavomereza zonena kuti “otembenukawo amakhala a khalidwe labwino; savutitsa alonda a ndende ngakhale pang’ono.” Nkhaniyo inanenanso kuti awo amene amamasulidwa asanakwanitse zaka zawo zachilango amagwirizana bwino ndi Mboni za Yehova ndipo samachitanso zaupandu.
Nanga woyang’anira ndende wamkulu anatipo bwanji? “Ntchito ya Mboni za Yehova m’ndendeyi njokhumbirika ndiponso njothandiza kwambiri,” iye anatero. Woyang’anira ndende wamkuluyo akuvomereza kuti “akamaphunzira Baibulo [ndi Mboni], zosankha zawo ndi kachitidwe kawo ka zinthu kamasintha, kuwapatsa chitsogozo chatsopano m’moyo wawo. Amachita zinthu mwanzeru ndiponso mwaulemu. Ndi antchito akhama, osavutitsa ngakhale pang’ono.” Ndemanga zabwino zimenezi za oyang’anira zimasangalatsadi Mboni zimene zimagwira ntchito ndi akaidi m’ndende ya ku Wołów.
Mboni zochezera ndendeyo zimazindikira bwino lomwe mawu a Yesu akuti: “Ndizindikira zanga, ndi zanga zindizindikira Ine. . . . Zidzamva mawu anga; ndipo zidzakhala gulu limodzi, mbusa mmodzi.” (Yohane 10:14, 16) Ngakhale malinga a ndende sangatsekereze Mbusa Wabwino, Yesu Kristu, posonkhanitsa anthu onga nkhosa. Mboni za ku Wołów zimayamikira kuti zili ndi mwayi wochita utumiki wosangalatsa umenewu. Ndipo zikuyang’ana kwa Yehova kuti apitirize kuzidalitsa pothandiza mitima yambiri yonga mwala kumvetsera uthenga wabwino wa Ufumu chimaliziro chisanafike.—Mateyu 24:14.
[Bokosi patsamba 27]
Vuto la Munthu Wamkulu Amene Ali Ngati Mwana
“Atakhala m’ndende kwa nthaŵi yaitali, mkaidi nthaŵi zambiri samadziŵanso kuti zimakhala bwanji kukhala mfulu, kapena kudzikhalira pawekha,” zikutero Mboni zogwirira ntchito m’ndende ya ku Wołów. “Kwenikweni vuto limene tili nalo ndilo vuto la munthu wamkulu amene ali ngati mwana, munthu amene atamasulidwa m’ndende samadziŵa kudzisamalira. Ndiye chifukwa chake ntchito ya mpingo imaposa pa kungomphunzitsa choonadi cha Baibulo. Tiyenera kumkonzekeretsa kukhala monga mmene ena onse amakhalira, kumchenjeza za zinthu zoopsa zatsopano ndi ziyeso zimene angakumane nazo. Ngakhale kuti timasamala kusapereka chitetezo chonkitsa, tiyenera kumthandiza kuyambiranso m’moyo.”