Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w98 12/15 tsamba 29
  • Katswiri wa Maphunziro Asintha Deti la Malembo a Pamanja a Baibulo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Katswiri wa Maphunziro Asintha Deti la Malembo a Pamanja a Baibulo
  • Nsanja ya Olonda—1998
Nsanja ya Olonda—1998
w98 12/15 tsamba 29

Katswiri wa Maphunziro Asintha Deti la Malembo a Pamanja a Baibulo

Malinga ndi kunena kwa Carsten Peter Thiede, katswiri wachijeremani wa maphunziro a malembo a pamanja agumbwa, akuti pali umboni weniweni wakuti zidutswa zitatu zagumbwa za Uthenga Wabwino wa Mateyu (zodziŵika monga Magdalen Papyrus) zinalembedwa m’zaka za zana loyamba.

Atayerekezera zidutswazi (zokhala ndi mbali za chaputala cha Mateyu 26) ndi kalata yakale ya malonda yopezeka ku Igupto, Thiede ananena kuti kalata ya ku Igupto njofanana ndi “Magdalen Papyrus monga mapasa​—m’maonekedwe ndi m’kalembedwe ka liwu lililonse palokha.” Thiede ndi wolemba mnzake Matthew D’Ancona ananena m’buku lawo lakuti Eyewitness to Jesus​—Amazing New Manuscript Evidence About the Origin of the Gospels kuti kufanana kwa zikalata ziŵiri zimenezi kukusonyeza kuti zinalembedwa pafupifupi panthaŵi imodzi. Liti? Kalata ya malonda ili ndi deti la “‘M’chaka cha 12 cha Nero Ambuye, Epeiph 30’​—chimene malinga ndi kalenda yathu ndi July 24, 66 [C.E.].”

“Deti limeneli, ngati nlolondola, nlofunika kwambiri,” anatero Polofesa Phillip W. Comfort, mu nkhani yofalitsidwa mu Tyndale Bulletin, “chifukwa limaika malembo a pamanja a Uthenga Wabwino wa Mateyu m’zaka za zana lomwelo limene unalembedwa.” Ndiponso lingapangitse Magdalen Papyrus kukhala zidutswa zakale kwambiri za Uthenga Wabwinowo zimene zilipo.

[Chithunzi patsamba 29]

Magdalen Papyrus, umenewu ndiwo ukulu wake

[Mawu a Chithunzi]

Mwa chilolezo cha President and Fellows of Magdalen College, Oxford

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena