Kodi Mudzamvera Chenjezo?
A 19 May, 1997, chimphepo chinadutsa chigawo cha Chittagong ku Bangladesh. M’tauni ya Cox Bazaar chimphepo chimenechi chinali kuthamanga pa mtunda wa makilomita 250 pa ola. M’madera a m’midzi, nyumba za udzu zinasesedwa, kungotsala zizindikiro zakuti panali nyumba. Mitengo ndi mapolo a telefoni zinazuka; zina zinathyoka pakati mpakati ngati mivi ya machesi. Mutu wa nkhani m’nyuzipepala ya Bhorar Kagoj unanena kuti anthu okwanira 105 anaphedwa ndi chimphepo chimenechi.
Oona za nyengo amaneneratu malo amene akuganiza kuti chimphepocho chidzadutsa kutatsala maola pafupifupi 36. Mosakayikira, miyoyo yambiri inapulumuka chifukwa anthu zikwi mazanamazana anabisala m’nyumba zobisaliramo chimphepo zakonkire.
Kwa zaka zoposa zana limodzi, Mboni za Yehova zakhala zikulengeza uthenga wonena za chiwonongeko chimene chili pafupi kuchitika choopsa kwambiri kuposa chimphepo china chilichonse. Baibulo limachitcha “tsiku la Yehova lalikulu ndi loopsa.” (Yoweli 2:31) Mwa kumvera mauthenga a aneneri ochenjeza opezeka m’Baibulo, tingapulumuke mkwiyo wake.—Zefaniya 2:2, 3.
Mboni za Yehova si aneneri opereka uthenga wa chiweruzo, ayi. Wawo ndi uthenga wopatsa chiyembekezo. Amafuna kuthandiza anthu kuti aphunzire za Ufumu wa Mulungu, umene posachedwapa udzachotsa kusalungama konse padziko lapansi. Mawu a Mulungu, Baibulo, limatiuza kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: inde, udzayang’anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—Salmo 37:10, 11.
[Mawu a Chithunzi patsamba 32]
WHO/League of Red Cross