Njira ya Chikondi Silephera
“Funitsitsani mphatso zoposa. Ndipo ndikuonetsani njira yokoma yoposatu.”—1 AKORINTO 12:31.
1-3. (a) Kodi kuphunzira kusonyeza chikondi kukufanana motani ndi kuphunzira chinenero china? (b) Kodi ndi zinthu ziti zimene zingapangitse kuphunzira kusonyeza chikondi kukhala kovuta?
KODI munayesapo kuphunzira chinenero china? N’zovuta, kunena mwachidule. Komatu mwana wamng’ono angaphunzire chinenero mwa kumangochimvetsera. Ubongo wake umasunga mamvekedwe ndi matanthauzo a mawu pamene akuyankhulidwa, moti posapita nthaŵi mwanayo amayamba kuchiyankhula bwino chinenerocho, mwinanso mosaphophonya. Si mmene zilili ndi akulu. Mobwerezabwereza timafufuza m’dikishonale ya chinenero chinacho, kungoti tidziŵe mawu ake angapo osavuta. Koma m’kupita kwa nthaŵi ndiponso mwa kuchiphunzira mokwanira, timayamba kulingalira m’chinenero chatsopanocho ndiponso kuchiyankhula kumakhala kosavuta.
2 Kuphunzira kusonyeza chikondi kuli ngati kuphunzira chinenero china. Zoonadi, anthu amabadwa ndi mlingo winawake wa mkhalidwe waumulungu umenewu. (Genesis 1:27; yerekezerani ndi 1 Yohane 4:8.) Komabe, kuphunzira kusonyeza chikondi kumafuna kuyesetsa kwambiri—makamaka lerolino, pamene chikondi chachibadwidwe chikusoŵa kwambiri. (2 Timoteo 3:1-5) Nthaŵi zina zilidi motero m’banja mwenimwenimo. Inde, ambiri amakulira m’mikhalidwe yovuta mmene mawu osonyeza chikondi satchulidwa kwenikweni—ngati amatchulidwa n’komwe. (Aefeso 4:29-31; 6:4) Choncho kodi tingaphunzire motani kusonyeza chikondi—ngakhale ngati ifeyo sitinasonyezedwe chikondi kwenikweni?
3 Baibulo lingathandize. Pa 1 Akorinto 13:4-8, Paulo anapereka, osati mafotokozedwe wamba a chikondi, koma mafotokozedwe atsatanetsatane a mmene chikondi chapamwamba koposa chimenechi chimagwirira ntchito. Kupenda mavesi ameneŵa kudzatithandiza kudziŵa bwino mmene mkhalidwe waumulungu umenewu ulili ndiponso kudzatikonzekeretsa bwino kuusonyeza. Tiyeni tikambirane mbali zina za chikondi monga momwe Paulo anazifotokozera. Tidzaziika m’magulu akuluakulu atatu: khalidwe lathu lamasiku onse; kenako, tidzasumika maganizo pa unansi wathu ndi ena; ndiponso, pomalizira pake, chipiriro chathu.
Chikondi Chimatithandiza Kugonjetsa Kunyada
4. Kodi Baibulo limafotokozanji ponena za kaduka?
4 Atanena mawu ake oyamba ponena za chikondi, Paulo analembera Akorinto kuti: “Chikondi sichidukidwa.” (1 Akorinto 13:4) Munthu angadukidwe ndi zimene ena apeza kapena zimene achita. Kudukidwa kumeneku kumawononga—kuthupi, mumtima, ndiponso mwauzimu.—Miyambo 14:30; Aroma 13:13; Yakobo 3:14-16.
5. Kodi chikondi chingatithandize motani kuthetsa nsanje pamene taona kuti udindo wina wateokalase watipitirira?
5 Ponena za zimenezi, dzifunseni kuti, ‘Kodi ndimachita nsanje ndikaona kuti maudindo ena ateokalase andipitirira?’ Ngati mwayankha kuti inde, musataye mtima. Wolemba Baibulo Yakobo akutikumbutsa kuti anthu onse opanda ungwiro ‘amachita nsanje.’ (Yakobo 4:5) Kukonda mbale wanu kungakuthandizeni kukhalanso ndi maganizo abwino. Kungakupangitseni kukondwera ndi amene akukondwera ndi kusaona ngati mwanyozedwa pamene wina alandira dalitso kapena chiyamikiro.—Yerekezerani ndi 1 Samueli 18:7-9.
6. Kodi ndi mkhalidwe woipa wotani umene unabadwa mumpingo wa ku Korinto wa m’zaka za zana loyamba?
6 Paulo anawonjezera kuti chikondi “sichidziŵa kudzitamanda, sichidzikuza.” (1 Akorinto 13:4) Ngati tili ndi luso linalake kapena timadziŵa kuchita zinthu zakutizakuti, palibe chifukwa chodzitamandira nazo. Mwachionekere, limeneli ndilo linali vuto la amuna ena ofuna malo apamwamba amene anali ataloŵa mumpingo wakale wa ku Korinto. Mwina anali aluso kwambiri pofotokoza zinthu kapena ankayendetsa zinthu bwino kwambiri. Kudzionetsera kwawo kuyenera kuti nakonso kunapangitsa mpingowo kugaŵanika. (1 Akorinto 3:3, 4; 2 Akorinto 12:20) Zinthu zinafika poipa kwambiri moti pambuyo pake Paulo anadzudzula Akorintowo chifukwa cha ‘kulolana nawo opanda nzeru,’ amene Paulo powatsutsa anawatcha “atumwi oposatu.”—2 Akorinto 11:5, 19, 20.
7, 8. Sonyezani mogwiritsa ntchito Baibulo mmene tingagwiritsire ntchito maluso ena alionse achibadwa pochirikiza m’gwirizano.
7 Zofananazo zingachitikenso lerolino. Mwachitsanzo, ena angamakonde kudzitamandira pa zimene achita mu utumiki kapena chifukwa cha maudindo awo m’gulu la Mulungu. Ngakhale ngati tili ndi luso linalake kapena timadziŵa kuchita zinthu zina zimene ena mumpingo amalephera, kodi chimenecho chingakhale chifukwa chodzikuzira? Ndi iko komwe, tiyenera kugwiritsa ntchito maluso alionse achibadwa amene tingakhale nawo pochirikiza mgwirizano—osati kudzitukumula nawo.—Mateyu 23:12; 1 Petro 5:6.
8 Paulo analemba kuti ngakhale kuti mpingo uli ndi ziŵalo zambiri, “Mulungu analumikizitsa thupi.” (1 Akorinto 12:19-26) Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti ‘kulumikizitsa’ limatanthauza kusanganiza bwino, monga momwe amachitira posanganiza zinthu za maonekedwe osiyanasiyana kuti zikongole. Choncho palibe munthu mumpingo amene ayenera kudzikuza chifukwa cha maluso ake ndi kuyesa kulamulira ena. Kunyada ndi kufuna malo apamwamba n’zosafunika m’gulu la Mulungu.—Miyambo 16:19; 1 Akorinto 14:12; 1 Petro 5:2, 3.
9. Kodi Baibulo lili ndi zitsanzo zochenjeza zotani za anthu amene anali kutsata za iwo okha?
9 Chikondi “sichitsata za mwini yekha.” (1 Akorinto 13:5) Munthu wachikondi sachenjerera ena kuti apeze zimene akufuna. Baibulo lili ndi zitsanzo zochenjeza zokhudza nkhani imeneyi. Mwachitsanzo: Timaŵerenga za Delila, Yezebeli, ndi Ataliya—akazi amene anachenjerera ena kuti akwaniritse zolinga zawo zadyera. (Oweruza 16:16; 1 Mafumu 21:25; 2 Mbiri 22:10-12) Panalinso Abisalomu, mwana wa Mfumu Davide. Iye anali kufikira anthu obwera ku Yerusalemu kuti milandu yawo idzaweruzidwe. Ndiyeno anali kuneneza bwalo la mfumu mwamachenjera kuti silisamala za mavuto a anthuwo. Kenako ankanena mosapita mbali kuti bwalolo lingofunikira munthu wokoma mtima ngati iyeyo! (2 Samueli 15:2-4) Inde, Abisalomu sanali kufunira anthu ovutikawo zabwino, koma iye mwini. Pochita monga mfumu yodzilonga yokha, iye anakopa mitima ya anthu ambiri. Koma m’kupita kwa nthaŵi, Abisalomu anagonjetsedwa kotheratu. Atamwalira, sanaonedwenso kukhala wofunikira kuikidwa m’manda mwaulemu.—2 Samueli 18:6-17.
10. Kodi tingasonyeze motani kuti tikupenyereranso za ena?
10 Limeneli ndi chenjezo kwa Akristu lerolino. Kaya ndife amuna kapena akazi, mwina mwachibadwa timatha kusonkhezera anthu ena. Zingakhale zosavuta kwa ife kuchita zimene tikufuna, kunena kwake titero, mwa kuyankhula kwambiri kuposa ena pokambirana nawo kapena mwa kuumirira malingaliro ako kuti awo amene ali ndi malingaliro osiyana agonje. Koma ngati ndifedi achikondi, tidzapenyereranso za ena. (Afilipi 2:2-4) Sitidzapondereza ena kapena kuchirikiza malingaliro okayikitsa chifukwa cha chidziŵitso chathu kapena malo athu m’gulu la Mulungu, monga kuti malingaliro athu okha ndi amene angagwiritsidwe ntchito. M’malo mwake, tidzakumbukira mwambi wa m’Baibulo wakuti: “Kunyada kutsogolera kuwonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kupunthwa.”—Miyambo 16:18.
Chikondi Chimapangitsa Maunansi Kukhala Amtendere
11. (a) Kodi chikondi chokoma mtima komanso chosachita zosayenera tingachisonyeze m’njira zotani? (b) Kodi tingasonyeze motani kuti sitikondwera ndi chinyengo?
11 Paulo analembanso kuti chikondi chili “chokoma mtima” ndi kutinso “sichichita zosayenera.” (1 Akorinto 13:4, 5) Inde, chikondi sichidzatilola kukhala amwano, owola mkamwa, kapena opanda ulemu. M’malo mwake, tidzaganiziranso malingaliro a ena. Mwachitsanzo, munthu wachikondi adzapeŵa kuchita zinthu zimene zingavutitse chikumbumtima cha ena. (Yerekezerani ndi 1 Akorinto 8:13.) Chikondi “sichikondwera ndi chinyengo, koma chikondwera ndi choonadi.” (1 Akorinto 13:6) Ngati tikonda malamulo a Yehova, sitidzaona chisembwere ngati nkhani yaing’ono ndiponso sitidzakondwera ndi zinthu zimene Mulungu amadana nazo. (Salmo 119:97) Chikondi chidzatithandiza kukondwera ndi zinthu zomangirira osati zowononga.—Aroma 15:2; 1 Akorinto 10:23, 24; 14:26.
12, 13. (a) Kodi tiyenera kuchita motani wina akatilakwira? (b) Tchulani zitsanzo za m’Baibulo zosonyeza kuti ngakhale kukwiya pazifukwa zomveka kungatipangitse kuchita zinthu mosaganiza bwino?
12 Paulo analemba kuti chikondi “sichipsa mtima” (“sichikhala cha mtima wapachala,” Phillips). (1 Akorinto 13:5) Zoonadi, anthu opanda ungwirofe n’chibadwa chathu kuvutika maganizo kapena kukwiya wina akatilakwira. Komabe, n’kulakwa kusunga chakukhosi kwa nthaŵi yaitali kapena kukhalabe wokwiya. (Salmo 4:4; Aefeso 4:26) Ngakhale titakwiya pachifukwa chomveka, ngati sitidziletsa tingachite zinthu mosaganiza bwino, ndipo Yehova adzatiimba mlandu.—Genesis 34:1-31; 49:5-7; Numeri 12:3; 20:10-12; Salmo 106:32, 33.
13 Ena alola zophophonya za ena kukhudza chosankha chawo cha kupezeka pamisonkhano yachikristu kapena kukhala ndi mbali mu utumiki wakumunda. Kumbuyoko, ambiri mwa anthu ameneŵa anachita bwino pomenya nkhondo yolimba ya chikhulupiriro, mwinamwake mwa kupirira chitsutso cha banja lawo, kunyozedwa ndi anzawo akuntchito, ndi zina zotero. Anapirira zopinga zimenezo chifukwa chakuti anaziona ngati ziyeso za kukhulupirika kwawo, ndipo zinalidi motero. Koma kodi n’chiyani chimachitika Mkristu mnzawo akanena kapena kuchita kenakake kosasonyeza chikondi? Kodi ichinso si chiyeso cha kukhulupirika? Ndithudi n’chiyeso, popeza kuti ngati tikhalabe okwiya, ‘tingam’patse malo Mdyerekezi.’—Aefeso 4:27.
14, 15. (a) Kodi ‘kulemba cholakwa’ kumatanthauzanji? (b) Kodi tingam’tsanzire motani Yehova pa kukhala wokhululukira?
14 Ndiye chifukwa chake Paulo anawonjezera kuti chikondi “sichilingirira zoipa [“sichilemba zolakwa,” NW].” (1 Akorinto 13:5) Pamenepa anagwiritsa ntchito liwu la oŵerengera ndalama, mwachionekere akumapereka lingaliro la kulemba cholakwa cha wina m’buku la ngongole kuti chisaiŵalidwe. Kodi chingakhale chikondi kumakumbukira nthaŵi zonse mawu kapena zochita zimene zinatipweteketsa mtima, monga kuti nthaŵi ina yake m’tsogolo mudzazifuna? Ndife okondwa chotani nanga kuti Yehova samationa m’njira yopanda chifundo imeneyo! (Salmo 130:3) Inde, tikalapa, iye amafafaniza zolakwa zathu.—Machitidwe 3:19.
15 Tingatsanzire Yehova pankhaniyi. Sitiyenera kuvutika maganizo mopambanitsa ngati taona kuti wina watinyozera. Ngati tikwiya msanga, tingadzivulaze tokha kuposanso mmene munthu wotilakwirayo angativulazire. (Mlaliki 7:9, 22) M’malo mwake timayenera kukumbukira kuti chikondi “chikhulupirira zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:7) Inde, palibe aliyense wa ife amene akufuna kukhala wonyengeka msanga, komanso sitiyenera kumangokayikira zolinga za abale athu. Nthaŵi zonse ngati tingathe, tiyeni tisakayikire zolinga za ena.—Akolose 3:13.
Chikondi Chimatithandiza Kupirira
16. Kodi chikondi chingatithandize kukhala oleza mtima m’mikhalidwe yotani?
16 Kenako, Paulo anatiuza kuti “chikondi chikhala chilezere.” (1 Akorinto 13:4) Chimatipangitsa kupirira ziyeso, mwinamwake kwa nthaŵi yaitali. Mwachitsanzo, Akristu ambiri akhala m’mabanja okhala ndi zipembedzo zosiyana kwa zaka zambiri. Ena ndi mbeta, osati modzifunira, koma chifukwa chakuti sakupeza wokwatirana naye woyenera “mwa Ambuye.” (1 Akorinto 7:39; 2 Akorinto 6:14) Ndiyeno pali awo amene akuvutika ndi matenda ofooketsa. (Agalatiya 4:13, 14; Afilipi 2:25-30) Ndithudi, m’dongosolo lopanda ungwiroli, palibe munthu amene alibe mkhalidwe wina wofunika kupirira.—Mateyu 10:22; Yakobo 1:12.
17. Kodi n’chiyani chidzatithandiza kupirira zinthu zonse?
17 Paulo anatitsimikizira kuti chikondi “chikwirira zinthu zonse, . . . chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.” (1 Akorinto 13:7) Kukonda kwathu Yehova kudzatithandiza kuvutikira chilungamo mumkhalidwe wina uliwonse. (Mateyu 16:24; 1 Akorinto 10:13) Sitikulakalaka kufera chikhulupiriro iyayi. M’malo mwake, cholinga chathu ndicho kukhala amtendere ndiponso achete. (Aroma 12:18; 1 Atesalonika 4:11, 12) Ngakhale zili motero, ziyeso za chikhulupiriro zikabuka, timazipirira mokondwera monga mbali ya mtengo wa kukhala wophunzira wachikristu. (Luka 14:28-33) Pamene tikupirira, timayesa kukhala ndi maganizo abwino, tikumayembekeza kuti pakati pa ziyeso zimenezo padzatuluka zinthu zabwino.
18. Kodi chipiriro chimafunika motani ngakhale m’nyengo yabwino?
18 Chisautso sindicho mkhalidwe wokha wofuna chipiriro. Nthaŵi zina, kupirira kumangotanthauza kukhalitsa, kupitirizabe zochita zomwezo kaya pakhale ziyeso kapena zisakhalepo. Kupirira kumaphatikizapo kukhalabe ndi pologalamu yabwino ya zochita zauzimu. Mwachitsanzo, kodi mumatengamo mbali mokwanira mu utumiki, malinga ndi mikhalidwe yanu? Kodi mumaŵerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu ndi kuyankhula ndi Atate wanu wakumwamba m’pemphero? Kodi nthaŵi zonse mumapezeka pamisonkhano ya mpingo, ndipo kodi mumapindula pamene mulimbikitsana ndi okhulupirira anzanu? Ngati zili choncho, ndiye kuti panopa kaya muli m’nyengo yabwino kapena m’nyengo yovuta, mukupirira. Musaleme, “pakuti panyengo yake tidzatuta tikapanda kufooka.”—Agalatiya 6:9.
Chikondi—“Njira Yokoma Yoposatu”
19. Kodi chikondi ndi “njira yokoma yoposatu” motani?
19 Paulo anagogomezera kufunika kosonyeza chikondi mwa kutcha mkhalidwe waumulungu umenewu kuti “njira yokoma yoposatu.” (1 Akorinto 12:31) “Yoposatu” m’lingaliro lotani? Inde, Paulo anali atangolongosola kumene mphatso za mzimu, zimene zinali zofala pakati pa Akristu a m’zaka za zana loyamba. Ena anatha kulosera, ena anapatsidwa mphamvu yochiritsa matenda, ambiri anapatsidwa mphatso yoyankhula m’malirime. Mphatsodi zodabwitsa kwambiri! Koma Paulo anauza Akorinto kuti: “Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuŵa woomba, kapena nguli yolira. Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziŵe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe.” (1 Akorinto 13:1, 2) Inde, ngakhale zochita zimene zingakhale zofunika zimakhala “ntchito zakufa” ngati cholinga chake si chikondi cha pa Mulungu ndi anansi.—Ahebri 6:1.
20. Kodi n’chifukwa chiyani khama lili lofunika ngati tikufuna kukulitsa chikondi?
20 Yesu anatipatsanso chifukwa china chimene tiyenera kukulitsira mkhalidwe waumulungu umenewu wa chikondi. “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga,” iye anatero, “ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.” (Yohane 13:35) Mawu akuti “ngati” amapatsa Mkristu aliyense ufulu wodzisankhira kuphunzira kusonyeza chikondi. Ndi iko komwe, kungokhala m’dziko lina sikungatikakamize kuphunzira kuyankhula chinenero cha m’dzikolo. Kapenanso kungopezeka pamisonkhano pa Nyumba ya Ufumu kapena kuyanjana ndi Akristu anzathu mwa iko kokha sikungatiphunzitse kusonyeza chikondi. Kuphunzira “chinenero” chimenechi kumafuna khama.
21, 22. (a) Kodi tiyenera kutani ngati talephera kukwanitsa mbali inayake ya chikondi imene Paulo anaitchula? (b) Kodi tinganene motani kuti “chikondi sichitha nthaŵi zonse”?
21 Nthaŵi zina, mudzalephera kukwanitsa mbali inayake ya chikondi imene Paulo anatchula. Koma musataye mtima. Yesetsani moleza mtima. Pitirizani kufufuza m’Baibulo ndi kutsatira mapulinsipulo ake pochita zinthu ndi ena. Musaiŵale chitsanzo chimene Yehova iyemwini akutipatsa. Paulo analangiza Aefeso kuti: “Mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Kristu anakhululukira inu.”—Aefeso 4:32.
22 Monga momwe kuphunzira kuyankhula chinenero china kumakhala kosavuta m’kupita kwa nthaŵi, mudzapeza kuti kusonyeza chikondi kudzakhala kosavuta m’kupita kwa nthaŵi. Paulo anatitsimikizira kuti “chikondi sichitha nthaŵi zonse.” (1 Akorinto 13:8) Mosiyana ndi mphatso zozizwitsa za mzimu, chikondi sichidzatha kunthaŵi zonse. Choncho pitirizani kusonyeza mkhalidwe waumulungu umenewu. Ndiwo, monga momwe Paulo anautchera, “njira yokoma yoposatu.”
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi chikondi chingatithandize motani kuthetsa kunyada?
◻ Kodi chikondi chingatithandize m’njira zotani kuchirikiza mtendere mumpingo?
◻ Kodi chikondi chingatithandize motani kupirira?
◻ Kodi chikondi ndicho “njira yokoma yoposatu” motani?
[Chithunzi patsamba 19]
Chikondi chidzatithandiza kunyalanyaza zolakwa za okhulupirira anzathu
[Zithunzi patsamba 23]
Kupirira kumatanthauza kutsatirabe pologalamu ya zochita zathu zateokalase