“Ndinaona Mtendere Umene Unalipo”
MWAMUNA wina wolankhula Chijeremani anapita kumsonkhano wa Mboni za Yehova kuti “akaone mwachinsinsi” zochita zawo. Chifukwa chiyani? Anali n’cholinga chofuna “kuvumbula kagulu ka mpatuko kameneka ndi kuletsa anzake kusocheretsedwa nako.” Atabwerako, analembera anzake kalata yotsatirayi:
“N’tayandikira malo a msonkhanowo, n’nadzifunsa ngati bwaloli linali limenelidi. Panalibe ndi munthu mmodzi yemwe anali chilili kunja kwa bwaloli, ndipo pansi panalibe zinyalala kapena mabotolo a moŵa. N’tafika pafupi, ndinaona amuna aŵiri ali pakhomo la bwaloli. Anandipatsa moni ndi kundiuza kuti ndiloŵe.
“Ndinkaganiza kuti ndimva kulongolola kwa khamu la anthu ofika pa maloŵa, koma munali duu. Ndinaganiza kuti, ‘Mwina muli anthu ochepa chabe.’
“N’tangoloŵa, ndinachita chidwi ndi seŵero lomwe linali kuchitika papulatifomu. Pambuyo pake ndinaona kuti bwalo linali lodzaza kwambiri ndi khamu la anthu omvetsera mwatcheru. Ndinaona mtendere umene unalipo. Zomwe ndinamva ndi kuona m’chigawo chomaliza cha msonkhanowo zinandipatsa chidwi kwambiri.
“Ndili pakati pa Mbonizo, ndinaona nkhope zachimwemwe ndi makambitsirano achikondi. Nthaŵi yomweyo, ndinakakamizika kuganiza kuti, ‘Awadi ndi anthu a Mulungu!’”
M’malo ‘moletsa anzake kusocheretsedwa,’ mwamuna wachinyamatayu anawapempha kuti aziphunzira naye Baibulo. Zotsatira zake? Lerolino, ndi mkulu wachikristu. Iye ndi banja lake ndi achangu m’mipingo ku Zug, ku Switzerland.