Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 2/15 tsamba 30-31
  • Kodi Mumayanjana ndi Ena Kapena Mumangopezekapo?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Mumayanjana ndi Ena Kapena Mumangopezekapo?
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Abale Enieni
  • Mabwenzi Enieni
  • Anzanu
  • Kuthandizana
Nsanja ya Olonda—1999
w99 2/15 tsamba 30-31

Kodi Mumayanjana ndi Ena Kapena Mumangopezekapo?

MWINAMWAKE mumaganiza kuti palibe kusiyana kwenikweni pakati pa kupezeka pamisokhano ya Mboni za Yehova ndi kuyanjana ndi Mboni za Yehova. Komatu kusiyana kulipo. Si onse ofika pamisonkhano imeneyi amene amayanjana ndi ena.

Kuti mumvetse mmene munthu angapezekere pamisonkhano koma osayanjana ndi ena, talingalirani za nkhani ya m’Baibulo pa Yobu 1:6. Lembalo limasonyeza kuti si atumiki aumunthu okha a Mulungu amene amachita misonkhano, koma ngakhale ana auzimu a Mulungu ali ndi nthaŵi zoikika zokaonekera pamaso pa Yehova Mulungu. Nkhaniyo imati: “Ndipo panali tsiku lakuti ana a Mulungu anadza kudzionetsa kwa Yehova, nadzanso Satana pakati pawo.” Satana anapezekapo pamsonkhanowo, koma kodi anali kuyanjanadi ndi Yehova Mulungu ndi ana auzimu okhulupirika a Mulungu amene anasonkhana pamenepo? Iyayi.

Kupezekapo kumatanthauza “kukhalapo.” N’zimene Satana anachita panopa. Koma mawu akuti kuyanjana amatanthauza zambiri. Amatanthauza “kugwirizana ndi wina monga bwenzi, mnzako, wothandizana naye kapena wopanga naye mgwirizano,” kapena “kugwirizana kukhala gulu limodzi; kukhala munthu ndi mnzake; ndiponso, kuchitira zinthu pamodzi; kugwirizana pacholinga chimodzi.”

Ndithudi, mawuwa sakugwirizana ndi kupezekapo kwa Satana pamsonkhano uwu. Ndithudi sanagwirizane ndi Yehova Mulungu. Anasonyeza kuti sanali bwenzi la Yehova. Ndiponso Satana sanaone ana okhulupirika a Mulungu monga mabwenzi ake kapena anzake. Kwenikweni, iye anakayikira zolinga zawo potumikira Mulungu.

Choncho, tikuona kuti kuyanjanadi kwathu ndi ena sikudalira pa kungopezekapo kwathu, koma, m’malo mwake, pa zimene timaganizira kapena mmene timaonera awo opezekapo nafe.

Abale Enieni

Mboni za Yehova zimaitanana kuti “mbale” ndi “mlongo.” Zimenezi zimasonyeza unansi wathithithi umene uyenera kukhalapo pakati pa atumiki onse a Yehova Mulungu. Kwenikweni, mawu akuti “mbale” amatanthauza mwana wa makolo ako. Koma kodi timamvadi kuti tili paunansi weniweni woterowo ndi awo amene ali atumiki odzipatulira a Atate wathu, Yehova Mulungu? Kapena kodi timangogwiritsa ntchito mawu akuti “mbale” chifukwa chakuti tinangowapeza, chifukwa chakuti ndi mmene Mboni za Yehova zimaitanirana?

N’zochititsa chidwi kuona kuti paubale wawo wakuthupi Kaini ndi Abele ankati ndi olambira Yehova, zimene zikanawapangitsa kukhalanso paubale wauzimu. Penapake, Baibulo limati: “Yehova ndipo anati kwa Kaini, Ali kuti Abele mphwako [“mbale wako,” NW]? Ndipo anati, Sindidziwayi: kodi ndine woyang’anira mphwanga [“mbale wanga,” NW]?” (Genesis 4:9) Kaini anali atangopha kumene mbale wake, koma kodi mukuona kuti sanazengereze kugwiritsa ntchito mawu akuti “mbale”?

Zimenezi zikusonyeza kuti pamafunika zambiri zoposa kungotcha munthu wina kuti “mbale” kapena “mlongo.” M’malo mwake, tiyenera kukulitsa chikondi chenicheni chimene chimatisonyezadi kuti ndife mbale kapena mlongo kwa anzathu achikristu. N’kofunika kuti tisakonde “ndi mawu, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m’choonadi.” Lamulo lachikristu ndilo lakuti “iye amene akonda Mulungu akondenso mbale wake.”​—1 Yohane 3:18; 4:21.

Mabwenzi Enieni

Monga momwe taonera kale, limodzi mwa matanthauzo a mawu akuti kuyanjana ndilo “kugwirizana ndi wina monga bwenzi.” Nthaŵi zambiri, Mboni za Yehova zimagwiritsa ntchito mawu akuti “mabwenzi” ponena za abale ndi alongo awo achikristu. Koma kuti tikhale mabwenzi enieni pamafunika zambiri zoposa kungopezeka pamisonkhano ndi munthu wina, kapena ngakhale kungodziŵa dzina la munthu wina. Zimatanthauza kuti tayamba kum’konda munthuyo.

Kodi n’kukhaliranji paubwenzi weniweni ndi ena? Yesu anasonyeza chifukwa chake pamene anati: “Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu.” (Yohane 15:14) Zimenezi zimasonyeza kuti maubwenzi enieni achikristu amakhalapo chifukwa chakuti onse amafuna kuchita zimene Kristu akulamula. Mabwenzi a Yesu ndi awo amene amamumvera​—kwa iye msinkhu wa munthu, mtundu wake kapena fuko lake zilibe kanthu. Ndi mmenenso zilili pakati pa Akristu oona. Inde, kufuna kwawo kutumikira Mulungu kumawapangitsa kukondana kwambiri kuposanso chikondi cha m’banja.

Yesu Kristu anasonyeza kuti ndi mmene ziyenera kukhalira. Popeza panthaŵi inayake, atauzidwa kuti amayi ake ndi abale ake akuthupi akufuna kuonana naye, Yesu anati: “Amayi wanga ndi abale anga ndiwo amene akumva mawu a Mulungu, nawachita.”​—Luka 8:21.

Anzanu

Kuyanjana kumatanthauzanso ‘kugwirizana ndi wina monga mnzako.’ Ndipo kodi mnzako ndi ndani? Ndiye munthu amene amagwirizana ndi munthu wina, munthu amene amachita zinthu limodzi ndi wina. Mukabwera kumisonkhano ya Mboni za Yehova, kodi mumadzimvadi kuti ndinu mnzawo wa anthu amene alipo, kapena kodi simumamvabe kukhala womasuka?

Ngati mumamva kuipa, kapena kuti chilendo, kodi zingakhale kuti mwina simukuchita nawo mokwanira, kapena kugwirizana ndi, zimene anthu a Yehova amachita? Mboni za Yehova n’zodzipereka kotheratu ‘polalikira uthenga wabwino wa Ufumu padziko lonse lapansi chimaliziro chisanafike.’ (Mateyu 24:14) Chotero, poyanjana nawodi monga anzanu muyenera kugwira nawo ntchito yolalikirayi ndi mtima wonse. Muyenera kumatsatira kotheratu mapulinsipulo achikristu m’moyo wanu.

Kuthandizana

Tanthauzo lina la verebulo ndilo ‘kugwirizana ndi wina monga wothandizana naye.’ Wothandizana naye ndiye ‘wa kumbali yako,’ ‘wotengamo mbali mnzako.’ Kodi mumamvadi kuti ndinu wothandizana ndi awo amene ali pamisonkhano? Kodi mumamvadi kuti nonsenu muli kumbali imodzi? Wamasalmo wa m’Baibulo analemba kuti: “Ine ndine wakuyanjana nawo onse akukuopani [Yehova], ndi iwo akusamalira malangizo anu.” (Salmo 119:63) Ngati ndinu wotsimikiza mtima kuima nji kumbali ya Yehova Mulungu ndi Ufumu wake, muyenera kuona awo amene ali pamisonkhano kukhala othandizana nawo enieni.

Wamasalmo Davide anafotokoza malingaliro a anthu amene amayanjanadi ndi anthu a Mulungu pamene anati: “Ndinakondwera mmene ananena nane, Tiyeni ku nyumba ya Yehova.” (Salmo 122:1) Inde, Davide anakondwera kukhala ndi mwayi woyanjana ndi anthu a Mulungu. Ndipo taonani mawuwo akuti “tiyeni.” Iye sanali kungokondwera ndi kupezekapo kwake, koma anawakondadi onse amene anali kufuna kulambira Yehova. Inunso mukhale ndi malingaliro ofananawa pamene mutengamo mbali m’misonkhano ya Mboni za Yehova.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena