Musagonjetsedwe ndi Nkhaŵa
“MUSADERE nkhaŵa za maŵa; pakuti maŵa adzadzidera nkhaŵa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.” (Mateyu 6:34) Uphungu umenewu woperekedwa ndi Yesu Kristu n’ngwofunikadi kwa tonse amene tikukhala m’dziko lino losakhazikika ndi lopsinja maganizo.
Komabe, kodi ndi zoona kuti tingakhale osadera nkhaŵa za mavuto athu, zosankha zathu, zoyenera kuchita ndiponso udindo wathu? Anthu ambiri ndi atondovi, opsinjika maganizo, ndiponso othodwa. N’chifukwa chake mankhwala okhazika pansi maganizo akugulitsidwa mamiliyoni ochuluka a ndalama.
Pamene Tingalekezere
Tiyenera kukonzekera zomwe tiyenera kuchita, ntchito zathu, zosankha, ndi chochita pa mavuto—kaya zitakhala zofulumira kapena ayi. Baibulo limatilimbikitsa ‘kukhala pansi ndi kuŵerengera mtengo wake’, tisanachite chinthu chilichonse chachikulu. (Luka 14:28-30) Zimenezi zimaphatikizapo kupenda zinthu zimene mungasankhe kuchita, kupenda zotsatira zake, ndi kuona za nthaŵi, mphamvu, ndi ndalama zimene zingawonongeke.
Ngakhale kuti munthu ayenera kupenda mosamala zimene zingachitike, si zotheka kapenanso si zopindulitsa kufuna kudziŵa mathero alionse a zinthu. Mwachitsanzo, ndi cholinga chofuna kuteteza banja, mungafune kudziŵa chochita ngati patabuka moto panyumba panu. Mungagule zida zokuchenjezani ndi zozimitsira moto. Mungakonze njira zothaŵiramo m’mbali zosiyanasiyana za nyumbayo ndi kuyeserera kutero pasadakhale. Koma kodi kuganizira zam’tsogolo kwanzeru ndi kofunikira kumathera pati, ndipo kodi nkhaŵa yopambanitsa ndi yosafunikira imayambira pati? Nkhaŵa yodzipatsa dala imeneyi imayamba mukayamba kuvutika maganizo ndi zochitika zambirimbiri zongolota, zimene zochuluka zimangobwera chifukwa choganizira kwambiri. Maganizo osautsa angakuthetseni nzeru ndipo mungakhulupirire kuti munalekelera chinthu chinachake kapena kuti simunateteze banja lanu mokwanira. Nkhaŵa yodzipatsira dala imeneyi ingakusokonezeni maganizo kwambiri koti n’kulephera kupeza tulo.
Mose Pamaso pa Farao
Yehova Mulungu anapatsa mneneri wake Mose ntchito yovuta. Poyamba, Mose anayenera kukaonekera kwa Aisrayeli ndi kuwakhutiritsa kuti Yehova wamusankha kuti awatsogolere ndi kuwatulutsa mu Aigupto. Kenako, Mose anayenera kukaonekera pamaso pa Farao ndi kum’pempha kuti awalole Aisrayeli kuti azipita. Potsiriza, Mose anayenera kutsogoza chikhamu cha mamiliyoni a anthu kudzera m’chipululu kukaloŵa nacho m’dziko la anthu osafuna mtendere. (Eksodo 3:1-10) Zonsezi zikanam’chititsa mantha. Koma kodi Mose analola kuti udindo umenewu udzaze maganizo ake ndi nkhaŵa yosafunikira?
Mwachidziŵikire Mose anali odera nkhaŵa ndi nkhani zingapo. Iye anafunsa Yehova kuti: “Onani, pakufika ine kwa ana a Israyeli, ndi kunena nawo, Mulungu wa makolo anu wandituma kwa inu; ndipo akakanena ndi ine, Dzina lake ndani? ndikanena nawo chiyani?” Yehova ana’mpatsa yankho. (Eksodo 3:13, 14) Mose analinso ndi nkhaŵa ndi zimene zikanachitika ngati Farao akadakana kum’khulupirira. Pamenepanso Yehova anam’yankha mneneriyo. Vuto lomaliza—Mose sanabise kuti anali “wosoŵa ponena.” Kodi akanathana nalo bwanji? Yehova anatuma Aroni kuti azikamuyankhulira Mose.—Eksodo 4:1-5,10-16.
Pokhala atakonzekera mwakuyankhidwa mafunso ake komanso pokhala ndi chikhulupiriro mwa Mulungu, Mose anachita monga momwe Yehova anamulamulirira. M’malo modzizunza ndi maganizo a zimene zikanachitika panthaŵi imene ankaonana ndi Farao, Mose “anachita momwemo.” (Eksodo 7:6) Ngati akanalola kuti nkhaŵa zimugonjetse, zikanafooketsa chikhulupiriro chake ndi kulimba mtima zomwe zinali zofunikira kuti athe kuchita ntchito yake.
Njira yosamala imene Mose anachitira ntchito yake ndi chitsanzo cha chimene mtumwi Paulo anachitcha “chidziletso.” (2 Timoteo 1:7; Tito 2:2-6) Ngati Mose akanapanda kudziletsa, mosavuta akanalefulidwa poona kukula kwa ntchito yake mpaka mwina sakanailandira.
Kulamulira Maganizo Anu
Kodi mumatani pamene m’moyo wanu wa tsiku ndi tsiku mwapezana ndi ziyeso za chikhulupiriro chanu kapena mavuto? Kodi mumatekeseka ndi mantha n’kumangoganizira za zopinga ndi zovuta za m’tsogolo? Kapena kodi mumaziona modekha? Monga ena amati, ‘Musaoloke mlatho musadaufike.’ Ndiponsotu palibe chifukwa chouolokera mlatho wongoyerekezerawu! Ndiye kodi mulolelanji kuvutitsidwa ndi chinthu chimene sichingadzachitike n’komwe? Baibulo limati: “Nkhaŵa iweramitsa mtima wa munthu.” (Miyambo 12:25) Zotsatirapo zake zimakhala zakuti umayamba kuzengerezazengereza popanga chosankha, kumangoti ndizichitabe n’kumazindikira zinthu zitathina.
Choopsa kwambiri ndi chivulazo chauzimu chimene nkhaŵa yosafunikayi ingadzetse. Yesu Kristu anasonyeza kuti chiyamikiro cha “mawu a Ufumu” chingatsamwitsidwe kotheratu ndi mphamvu yonyenga ya chuma ndiponso ndi “nkhaŵa za dongosolo ili la zinthu.” (Mateyu 13:19, 22, NW) Monga momwe minga zingalepheretsere m’mera kukula ndi kudzabala zipatso, momwemonso nkhaŵa yosalamulirika ingatilepheretse kukula mwauzimu ndi kubala zipatso zom’tamanditsa Mulungu. Nsautso yodzipatsa dala, yovulaza imeneyi yawachititsa ena kulephera kudzipatulira kwa Yehova. Nkhaŵa yawo n’njakuti, ‘Nanga ndidzatani ndikalephera kusunga kudzipatulira kwanga?’
Mtumwi Paulo anatiuza kuti m’nkhondo yathu yauzimu, tikuyesayesa “kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Kristu.” (2 Akorinto 10:5) Mdani wathu wamkulu, Satana Mdyerekezi, angakhale wosangalala kwambiri kugwiritsa ntchito nkhaŵa zathu kuti atifooketse ndi kutilefula mwakuthupi, mwamalingaliro, ndi mwauzimu. Iye ndi katswiri wogwiritsa ntchito chikayikiro pokola iwo osakhala tcheru. Ichi ndi chifukwa chimene Paulo anachenjezera Akristu kuti ‘asam’patse malo Mdyerekezi.’ (Aefeso 4:27) Monga “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano” Satana wakhoza ‘kuchititsa khungu maganizo awo a osakhulupirira.’ (2 Akorinto 4:4) Tisam’lole kulamulira maganizo athu!
Chithandizo Chilipo
Pamene wapeza mavuto mwana amapita kwa tate wachikondi ndi kukalandira malangizo ndi chitonthozo. Mofananamo, tingapite kwa Atate wathu wakumwamba Yehova ndi mavuto athu. Ndiponsotu, Yehova amatipempha kum’senza nkhaŵa zathu. (Salmo 55:22) Monga mwana amene samadandaulanso ndi mavuto ake akalandira chilimbikitso kwa atate wake, tisamangom’senza chabe Yehova nkhaŵa zathu komanso tizizisiya kwa iye.—Yakobo 1:6.
Kodi Yehova timam’senzetsa motani nkhaŵa zathu? Afilipi 4:6, 7 akuyankha: “Musadere nkhaŵa konse; komatu m’zonse ndi pemphero, ndi pembedzero, pamodzi ndi chiyamiko, zopempha zanu zidziŵike kwa Mulungu. Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziŵitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Kristu Yesu.” Inde, poyankha mapemphero ndi mapembedzero athu akhama, Yehova angatipatse mtendere wapansi pa mtima umene umateteza maganizo athu ku nkhaŵa zosafunika.—Yeremiya 17:7, 8; Mateyu 6:25-34.
Komabe, kuti tichite mogwirizana ndi mapemphero athu, sitiyenera kudzipatula kaya mwakuthupi kapena mwamaganizo. (Miyambo 18:1) M’malo mwake, tingachite bwino kupenda mapulinsipulo ndi malangizo a Baibulo amene akukhudza vuto lathulo, choncho tidzakhala tikupewa kuchirikizika pa luntha lathu. (Miyambo 3:5, 6) Ana ndi akulu omwe angatembenukire ku Baibulo ndi zofalitsa za Watch Tower kuti apeze chidziŵitso chochuluka cha mmene angasankhire zochita ndi mmene angathetsere mavuto. Kuphatikizanso apo, mumpingo wachikristu, tadalitsidwa ndi akulu anzeru ndi odziŵa zinthu ndiponso Akristu ena okhwima maganizo amene nthaŵi zonse amakhala ofunitsitsa kuyankhula nafe. (Miyambo 11:14; 15:22) Anthu amene sakukhudzidwa mtima kwambiri ndi mavuto athuwo komanso okhala ndi malingaliro a Mulungu pankhani angamatithandize kumaona mavuto athu m’njira yosiyana. Ngakhale kuti sangatisankhire chochita, angatilimbikitse ndi kutichirikiza kwambiri.
‘Yembekezani Mulungu’
Palibe amene angatsutse kuti timapsinjika kwambiri tsiku lililonse ndi mavuto athu enieni ngakhale osaphatikizapo ena ongoyerekezera. Ngati nkhaŵa ya zimene zingachitike imatipatsa mantha ndi kutisoŵetsa mtendere pamenepo titembenukire kwa Yehova m’pemphero ndi mapembedzero. Tiyang’ane m’Mawu ake ndi ku gulu lake kaamba ka malangizo, nzeru, ndi maganizo abwino. Tidzaona kuti pachilichonse chimene chingabwere, tidzathandizidwa kuthana nacho.
Povutika maganizo, wamasalmo anaimba motere: “Udziŵeramiranji moyo wanga iwe? Ndi kuzingwa m’kati mwanga? Yembekeza Mulungu: pakuti ndidzam’lemekeza tsopanonso, ndiye chipulumutso cha nkhope yanga ndi Mulungu wanga.” (Salmo 42:11) Tidziganiza choncho.
Inde, konzekerani zinthu zokha zimene zili zofunikira kuziyembekezera, ndi kusiya zosadziŵikazo m’manja mwa Yehova. ‘Tayani pa Iye nkhaŵa yanu yonse, pakuti Iye asamalira inu.’—1 Petro 5:7.
[Chithunzi patsamba 23]
Monga Davide, kodi mumam’senza Yehova mavuto ndi nkhaŵa zanu?