Olengeza Ufumu Akusimba
Kulalikira ‘m’Nthaŵi Yabwino ndi m’Nthaŵi Yovuta’
PAMENE nkhondo inakuta dziko la Bosnia ndi Herzegovina, anthu zikwi zambiri anali pamavuto aakulu. Panthaŵi ya mayesero imeneyo, Mboni za Yehova zinayesetsa zolimba kulimbikitsa anthu ndi kuwapatsa chiyembekezo. Pansipa pali zigawo zina za kalata yolembedwa ndi Mboni ina imene panthaŵi ina inatumikira ku Sarajevo.
“Kuno moyo ndi wovuta, koma anthu amamvetsera kwambiri choonadi cha Baibulo. Mboni za kunoko zikupereka chitsanzo chabwino kwambiri cha kulimbikira. Izo n’zaumphaŵi mwakuthupi, koma zili ndi mzimu wabwino kwambiri. Pafupifupi achinyamata onse mumpingo ali mu utumiki wanthaŵi zonse. Ofalitsa atsopano amalimbikitsidwa ndi changu chimenechi, ndipo si zachilendo kwa iwo kuthera maola 60 kapena oposerapo mu utumiki mwezi uliwonse kungoyambira mwezi wawo woyamba kupita mu utumiki.
“Kuwonjezera pa kulalikira kunyumba ndi nyumba, tayesanso njira zina zosiyanasiyana zofikira anthu. Mwachitsanzo, pakhala zotsatirapo zabwino pogaŵira zofalitsa zofotokoza Baibulo m’manda ambiri a mumzindawu.
“Umboni waperekedwanso m’zipatala. Mu Dipatimenti ya Nthenda za Mtima ya m’chipatala china cha mu Sarajevo, dokotala wamkulu analandira Galamukani! ya December 8, 1996, imene ili ndi nkhani zonena za nthenda ya mtima. Anapempha makope owonjezeka kuti apatsenso madokotala ena. Ndiyeno Mboni zinaloledwa kuchezera odwala onse m’dipatimenti yake. Choncho, pa ola limodzi ndi mphindi zingapo, magazini oposa 100 anagaŵidwa pa bedi ndi bedi. Odwala ambiri ananena kuti kanali koyamba kuzondedwapo ndi munthu kuti awalimbikitse ndi kuwapatsa chiyembekezo.
“Nthaŵinso ina Mboni zinachezera Dipatimenti ya Matenda a Ana Aang’ono ndi nkhani za m’magazini zokhudza ana. Dokotala wamkulu nayenso analandira makope angapo a Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo oika m’chipinda choŵerengera. Tsopano amayi amaŵerengera ana awo nkhani za m’Baibulo masiku onse powazonda. Papangidwanso makonzedwe ochezera dokotala ameneyu kunyumba kwake.
“Mu Sarajevo muli asilikali zikwi zambiri a NATO [North Atlantic Treaty Organization] ochokera kumayiko osiyanasiyana. Amenewanso alalikidwa mosamalitsa. Nthaŵi zina timafikira galimoto lankhondo lililonse tikumasonyeza kabuku kakuti Good News for All Nations [Uthenga Wabwino ku Mitundu Yonse] pamodzi ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! a zinenero zosiyanasiyana. Magazini oposa 200 anagaŵidwa m’misasa ya asilikali a ku Italy. Chodabwitsa n’chakuti asilikali ambiri achitaliyana ankanena kuti sanayambe alankhulapo ndi Mboni za Yehova. Komatu tinalankhula nawo kuno ku Sarajevo.
“Tsiku lina galimoto lankhondo linaima m’mbali mwa msewu. Ndinagogoda pagalimotolo ndi ambulera yanga, ndipo msilikali anatuluka. Ndinamugaŵira Nsanja ya Olonda ya mutu wakuti ‘Amithenga a Mtendere—Kodi Iwo Ndani?’ Msilikaliyo anandiyang’ana ndi kundifunsa kuti, ‘Kodi ndinu wa Mboni za Yehova ngati?’ Atamva kuti ndinedi, anayankha nati, ‘N’zodabwitsa; kunonso muliko! Kodi padziko lapansi pali malo osakhala ndi Mboni?’”
Mtumwi Paulo anapereka chilimbikitso chakuti: “Lalikira mawu; chita nawo m’nthaŵi yabwino, m’nthaŵi yovuta.” (2 Timoteo 4:2, NW) Monga anzawo achikhulupiriro chofananacho padziko lonse lapansi, Mboni za Yehova ku Sarajevo zikuchita zomwezo, ngakhale kulalikira pabedi ndi bedi ndi kufikiranso galimoto lankhondo ndi galimoto lankhondo!