Akolejanti—Kuphunzira Baibulo Kunawasiyanitsa ndi Ena
Kodi munamvapo za Akolejanti?
Kagulu kachipembedzo kakang’ono kameneka ka ku Holland m’zaka za zana la 17 kanali kosiyana kwambiri ndi zipembedzo zikuluzikulu za m’nthaŵiyo. Motani, ndipo kodi tingaphunzireponji? kuti tidziŵe, tiyeni tibwerere m’mbuyo.
MU 1587, Jacobus Arminius (kapena, Jacob Harmensen) anafika mumzinda wa Amsterdam. Sanavutike kupeza ntchito chifukwa chakuti anali ndi maphunziro apamwamba. Ali ndi zaka 21, anamaliza maphunziro pa Yunivesite ya Leiden ku Holland. Kenako, anathera zaka zisanu ndi chimodzi ku Switzerland, akuphunzira zaumulungu kwa Théodore de Bèze, woloŵa m’malo John Calvin, Mpolotesitanti Wokonzanso Chipembedzo. Ndiye chifukwa chake Apolotesitanti a ku Amsterdam anali okondwa kusankha Arminius wa zaka zakubadwa 27 ameneyo kukhala mmodzi wa apasitala awo! Koma patangopita zaka zochepa, mamembala ambiri a tchalitchi anaona kuti sanasankhe bwino. Chifukwa chiyani?
Nkhani ya Kuikidwiratu
Arminius atangoyamba kulalikira, panabuka mkangano pakati pa Apolotesitanti a ku Amsterdam ponena za chiphunzitso cha kuikidwiratu. Chiphunzitsochi ndicho chinali chachikulu pa ziphunzitso za Calvin, koma mamembala ena a tchalitchi anayamba kuona kuti Mulungu amene anaikiratu chipulumutso kwa ena ndi chiwonongeko kwa ena anali waukali ndi wopanda chilungamo. Otsatira a Calvin anaganiza kuti Arminius, pokhala anaphunzitsidwa ndi Bèze, adzawongolera awo okhala ndi malingaliro osiyana. Koma m’malo mwake, Arminius anagwirizana nawo, zomwe zinadabwitsa otsatira a Calvin. Podzafika mu 1593 mkanganowo unali utakula kwambiri moti unagaŵanitsa Apolotesitanti mumzindawo kukhala magulu aŵiri—ochirikiza chiphunzitsocho ndi ochikana, amene anali ndi malingaliro achikatikati.
Pazaka zochepa chabe, mkangano wa pamalo amodzi umenewu unagaŵanitsa Apolotesitanti m’dziko lonselo. Pomalizira pake, mu November 1618 zinthu zinafika poti ayenera kuchitapo kanthu. Otsatira a Calvin, mochirikizidwa ndi asilikali ndi anthu ena onse, anaitanira okana chiphunzitsocho (panthaŵiyo otchedwa kuti Aremonisitirantia) ku bungwe lina loyang’anira zinthu m’dzikolo, la Protestant Synod ku Dordrecht. Pakutha pa msonkhanowo, atumiki onse a Aremonisitiranti anauzidwa kuti asankhepo chimodzi: Kusaina pangano lakuti sadzalalikiranso, kapena kuchoka m’dzikolo. Ambiri anasankha kuchoka m’dzikolo. Otsatira a Calvin okhwimitsa zinthu anayamba kulalikira m’matchalitchi osiyidwa ndi atumiki a Aremonisitiranti. Otsatira Calvin anapambana—mwina tinene kuti sinodiyo inkaona ngati zatero.
Chiyambi ndi Kukula kwa Akolejanti
Monga kwina kulikonse, mpingo wa Aremonisitiranti m’mudzi wa Warmond, pafupi ndi Leiden, unatsala wopanda pasitala. Koma mosiyana ndi kwina kulikonse, mpingowo sunavomereze pasitala woikidwapo ndi sinodi. Ndiponso, pamene mtumiki wina wa Aremonisitiranti anaika moyo wake pachiswe mwa kubwerera ku Warmond mu 1620 kuti akasamalire mpingowo, ena a mumpingowo anamukananso. Iwo anali atayamba kuchita misonkhano yawo mobisa mosatsogozedwa ndi mtsogoleri wachipembedzo aliyense. Kenako, misonkhano imeneyi inayamba kutchedwa kuti makoleji ndipo opezekapo ake anatchedwa Akolejanti.
Ngakhale kuti Akolejanti anakhalapo kwenikweni chifukwa cha mikhalidwe imene inalipo ndipo osati pofuna kutsatira malamulo, posapita nthaŵi zinthu zinasintha. Gijsbert van der Kodde, wa mumpingowo ananena kuti mwa kusonkhana popanda kuyang’aniridwa ndi atsogoleri, gululo linali kutsatira Baibulo ndi njira ya Akristu oyambirira mosamalitsa kuposa matchalitchi akuluakulu. Udindo wa atsogoleri achipembedzo, iye anatero, unapangidwa atumwi atamwalira kuti amuna osafuna kuphunzira ntchito ya manja apezerepo ntchito.
Mu 1621, Van der Kodde ndi anthu ena ofanana naye maganizo anayamba kusonkhanira pa mudzi woyandikana nawo wa Rijnsburg.b Patapita zaka zingapo, chizunzo chachipembedzo chitatha, mbiri ya misonkhano ya Akolejanti inafalikira m’dziko lonselo nikopa “mbalame zomwera maiŵe osiyanasiyana,” monga momwe wolemba mbiri Siegfried Zilverberg ananenera. Kunali Aremonisitiranti, a Mennonite, a Socinian, ndiponso ngakhale akatswiri a zaumulungu. Ena anali achikumbe. Ena anali andakatulo, osindikiza, madokotala, ndi azopangapanga. Wafilosofi Spinoza (Benedictus de Spinoza) ndi mphunzitsi Johann Amos Comenius (kapena, Jan Komenský), limodzi ndi wojambula zithunzi wotchukayo Rembrandt van Rijn, anali kulikonda gululo. Malingaliro osiyanasiyana amene anthu okonda kulambira ameneŵa anabwera nawo anasonkhezera kupita patsogolo kwa zikhulupiriro za Akolejanti.
Chaka cha 1640 chitapita gulu lachangu limeneli linakula kwambiri. Makoleji anawonjezeka mu Rotterdam, Amsterdam, Leeuwarden, ndi mizinda ina. Polofesa wa mbiri yakale Andrew C. Fix ananena kuti pakati pa chaka cha 1650 ndi 1700, “Akolejanti . . . anawonjezeka nakhala chimodzi mwa zipembedzo zotchuka kwambiri ndiponso zosonkhezera kwambiri mu Holland mu zaka za zana la 17.”
Zikhulupiriro za Akolejanti
Popeza kuti malingaliro otsatirika, kulolera ena, ufulu wa kuyankhula ndiyo inali mikhalidwe yaikulu ya gulu la Akolejanti, Mkolejanti aliyense anali waufulu kukhala ndi zikhulupiriro zakezake. Komabe, anamangiriridwa pamodzi ndi zikhulupiriro zina zimene onse anali nazo. Mwachitsanzo, Akolejanti onse anali kudziŵa kufunika kwa phunziro laumwini la Baibulo. Membala aliyense, analemba motero Mkolejanti wina, ayenera “kudzifufuzira yekha osati kufika podziŵa Mulungu mwa kuuzidwa ndi wina.” Iwo anaterodi. Malinga ndi kunena kwa wodziŵa mbiri yakale ya tchalitchi wa m’zaka za zana la 19 Jacobus C. van Slee, Akolejanti anali ndi chidziŵitso cha Baibulo chachikulu kuposa zipembedzo za panthaŵiyo. Ngakhale otsutsana nawo anayamikira Akolejanti chifukwa cha kugwiritsa ntchito kwawo Baibulo mwaluso.
Koma pamene Akolejanti anaphunzira Baibulo kwambiri, mpamenenso anakhala ndi zikhulupiriro zosiyana kwambiri ndi zimene matchalitchi akuluakulu anali nazo. Maumboni a m’zaka za mazana a 17 mpaka 20 akufotokoza zina mwa zikhulupiriro zawo:
Tchalitchi Choyambirira. Mkolejanti ndiponso katswiri wa zaumulungu Adam Boreel mu 1644 analemba kuti tchalitchi choyambirira chitaloŵa m’ndale panthaŵi ya Mfumu Constantine, chinaswa pangano lake ndi Kristu ndipo sichinakhalenso chothandizidwa ndi mzimu woyera. Iye anawonjezera kuti pachifukwa chimenecho, ziphunzitso zonyenga zinachuluka nizikhalapo kufikira m’tsiku lake.
Kukonzanso. Kukonzanso kwa m’zaka za zana la 16 kotsogozedwa ndi Luther, Calvin, ndi ena sikunasinthe tchalitchi mokwanira. M’malo mwake, malinga ndi Galenus Abrahamsz (1622-1706), Mkolejanti wotchuka amenenso anali dokotala, Kukonzanso kumeneku kunaipitsiratu mkhalidwe wa zachipembedzo mwa kuyambitsa mikangano ndi udani. Kukonzanso koona kuyenera kusintha mtima wa munthu, zimene Kukonzanso kunalephera kuchita.
Tchalitchi ndi Atsogoleri Achipembedzo. Matchalitchi aakulu n’ngosaona mtima, n’ngokondetsa zadziko, ndipo alibiretu ulamuliro wa Mulungu. Aliyense wokondadi chipembedzo sangachite bwino kusiyapo kuchoka m’tchalitchi chake kuti asakhalire kumbuyo machimo ake. Ntchito ya atsogoleri achipembedzo, anatero Akolejanti, ndi yosemphana ndi Malemba ndipo ndi “yowonongetsa ubwino wauzimu wa mpingo wachikristu.”
Ufumu ndi Paradaiso. Mmodzi mwa anthu oyambitsa koleji ya Amsterdam, Daniel de Breen (1594-1664), analemba kuti Ufumu wa Kristu si ufumu wauzimu wokhala mumtima mwa munthu. Mphunzitsi Jacob Ostens, Mkolejanti wa ku Rotterdam, ananena kuti “makolo amakedzana anali kuyembekezera malonjezo okhudza dziko lapansi.” Momwemonso, Akolejanti anali kuyembekezera nthaŵi pamene dziko lapansi lidzasandutsidwa kukhala paradaiso.
Utatu. Akolejanti ena odziŵika kwambiri, atasonkhezeredwa ndi zikhulupiriro za a Socinian, anakana Utatu.c Mwachitsanzo, Daniel Zwicker (1621-78) analemba kuti chiphunzitso chilichonse chosemphana ndi malingaliro otsatirika, monga Utatu, ndi “chosatheka ndi chonama.” Mu 1694 Baibulo lotembenuzidwa ndi Reijnier Rooleeuw, Mkolejanti, linafalitsidwa. Ilo linatembenuza mawu akumapeto a Yohane 1:1 motere: “Ndipo mawuwo anali mulungu” m’malo mwa matembenuzidwe akalewo akuti: “Ndipo Mawu ndiye Mulungu.”d
Misonkhano ya Mlungu ndi Mlungu
Ngakhale kuti Akolejanti sanali kugwirizana pazikhulupiriro zonse, makoleji awo m’mizinda yosiyanasiyana anali kuchita zinthu mofanana ndithu. Wolemba mbiri Van Slee anasimba kuti m’masiku oyambirira a gulu la Akolejanti, iwo sanali kukonzekereratu misonkhano. Akolejanti ankaganiza kuti malinga ndi mawu a Paulo onena za kufunika kwa ‘kunenera,’ mamembala onse achimuna anali ndi ufulu wokamba nkhani m’koleji. (1 Akorinto 14:1, 3, 26) Chotsatirapo chake chinali chakuti misonkhano inali kutha usiku kwambiri ndipo opezekapo ena anali kugona “tulo tofa nato.”
Pambuyo pake, anayamba kuilinganiza bwino misonkhano. Akolejanti sanali kusonkhana pa Sabata pokha komanso mkati mwa mlungu madzulo. Kuti wokamba nkhani pamodzi ndi mpingo wonse akonzekere misonkhano ya chaka chonsecho pasadakhale, pologalamu yosindikizidwa inandandalika mavesi onse a Baibulo oyenera kuphunziridwa limodzi ndi zilembo zoyambirira za dzina la wokamba nkhani. Msonkhano utatsegulidwa ndi nyimbo ndi pemphero, wokamba nkhani ankafotokoza mavesi a Baibulo. Atamaliza, ankapempha amuna kukambapo zimene akuganiza ponena za nkhani imene yangofotokozedwa kumene. Kenako wokamba nkhani wachiŵiri anali kusonyeza mmene iwo angagwiritsire ntchito mavesi omwewo. Ndiye anali kumaliza msonkhanowo ndi pemphero ndi nyimbo.
Akolejanti m’tauni ya Harlingen, m’chigawo cha Friesland, anali ndi njira yachilendo yochitira kuti misonkhano yawo iziyendera nthaŵi. Wokamba nkhani amene anapitirira nthaŵi imene anapatsidwa ankalipira faindi yaing’ono.
Misonkhano Yaikulu
Akolejanti anaonanso kufunika kochita misonkhano yaikulu. Choncho, kuyambira mu 1640, Akolejanti m’dziko lonselo anali kupita ku Rijnsburg kaŵiri pachaka (m’ngululu ndi m’chilimwe). Misonkhano imeneyi, analemba motero wodziŵa mbiri yakale Fix, inawathandiza “kudziŵa malingaliro, kaonedwe, zikhulupiriro, ndi zochita za abale awo ochokera mtalimtali.”
Akolejanti ena ochokera kwina anali kubwereka zipinda kwa eni mudziwo pamene ena anali kukhala mu Groote Huis, kapena kuti Nyumba Yaikulu, nyumba yaikuludi ya zipinda 30 ya Akolejanti. Chakudya chinali kukonzedwa kumeneko ndipo anthu 60 mpaka 70 anali kudyera pamodzi. Atadya chakudya chamadzulo, alendowo anali kuwongola miyendo m’munda wa maluŵa waukulu bwino wa nyumbayo kuti asangalale ndi ‘ntchito za Mulungu, kucheza mofatsa, kapena kuti asinkhesinkhe.’
Ngakhale kuti si Akolejanti onse amene ankaganiza kuti ubatizo ndi wofunika, ambiri ankaganiza motero. Choncho, ubatizo unakhala chochitika cha pamisonkhano yaikuluyi. Wodziŵa mbiri yakale Van Slee ananena kuti mwambowo nthaŵi zambiri unali kuchitika Loŵeruka mmaŵa. Pambuyo pa nyimbo ndi pemphero panali kukhala nkhani yofotokoza kufunika kwa kumizidwa. Kenako wokamba nkhaniyo ankapempha anthu aakulu ofuna kubatizidwa amenewo kuti apereke umboni wa chikhulupiriro chawo, monga mwa kunena kuti, “Ndikhulupirira kuti Yesu Kristu ndi Mwana wa Mulungu wamoyo.” Atamaliza nkhaniyo ndi pemphero, onse opezekapo ankapita kudziŵe la ubatizo nakaona amuna ndi akazi atagwada m’dziŵemo, madzi atawafika m’mapeŵa. Kenako wobatiza anali kukankhira mutu wa wokhulupirira watsopanoyo kutsogolo ndi kuumiza m’madzi. Mwambowo utatha, onse anali kubwerera kumipando yawo kuti amvetserenso nkhani ina.
Loŵeruka madzulo panthaŵi ya 5:00 p.m., msonkhano weniweniwo unali kuyamba ndi kuŵerenga kachigawo ka m’Baibulo, nyimbo, ndi pemphero. Kuti aonetsetse kuti nthaŵi zonse wokamba nkhani analipo, makoleji a ku Rotterdam, Leiden, Amsterdam, ndi North Holland anali kusinthana kupereka okamba nkhani pamsonkhano uliwonse. Lamlungu mmaŵa anali kuchita phwando la Chakudya Chamadzulo cha Ambuye. Pambuyo pa nkhani, pemphero, ndi nyimbo, amuna kenako akazi anali kudyako mkate ndi kumwako vinyo. Nkhani zowonjezereka zinatsatira Lamlungu madzulo, ndipo Lolemba mmaŵa onse ankakumananso kuti amvetsere nkhani yotsekera. Nkhani zambiri zoperekedwa pamisonkhano yaikulu imeneyi, anatero Van Slee, zinali zothandiza, zogogomezera mmene angagwiritsire ntchito mfundozo ndipo osati kungozifotokoza chabe.
A pamudzi wa Rijnsburg ankasangalala kuti misonkhanoyo izichitikira pamudzi pawo. Wina wake amene anaona zochitikazo m’zaka za zana la 18 analemba kuti khamu la alendo, amene ankagula chakudya pamudzipo, anathandiza a pamudzipo kupeza ndalama. Ndiponso, msonkhano uliwonse utatha Akolejanti anali kupereka kangachepe kwa anthu osauka a pamudzi wa Rijnsburg. Mosakayikira, a pamudziwo anachita chisoni misonkhanoyo italekeka mu 1787. Kenako gulu la Akolejanti linatha. Chifukwa chiyani?
Chifukwa Chimene Linathera
Kumapeto kwa zaka za zana la 17, panabuka mkangano wokhudza kufunika kwa malingaliro otsatirika m’chipembedzo. Akolejanti ena ankalingalira kuti maganizo a munthu ayenera kukhala patsogolo pa vumbulutso la Mulungu, koma ena anatsutsa. M’kupita kwa nthaŵi, mkanganowo unagaŵa gulu lonse la Akolejanti. Atamwalira otsogolera magulu aŵiriwo mpamene Akolejanti anagwirizananso. Komabe, pambuyo pa kupatukana kumeneku gululo “silinakhalenso monga kale,” anatero wodziŵa mbiri yakale Fix.
Kulolera kowonjezereka kwa matchalitchi achipolotesitanti a m’zaka za zana la 18 nakonso kunapangitsa kuti gulu la Akolejanti lithe. Pamene mapulinsipulo a Akolejanti a malingaliro otsatirika ndi kulolera anayamba kukhala olandirika kwa anthu onse, “nyali ya Akolejanti yomwe inkaoneka ili yokha inazimiririka ndi kuwala kwa mbandakucha kwa m’Nyengo ya Kutseguka Maso.” Pomadzafika kumapeto kwa zaka za zana la 18, Akolejanti ambiri anali atagwirizana ndi a Mennonite ndi magulu ena achipembedzo.
Popeza kuti Akolejanti m’gulu lawo analibe cholinga chokhala ndi malingaliro amodzimodzi, pafupifupi Mkolejanti aliyense anali ndi malingaliro ake ake. Iwo ankadziŵa zimenezi ndipo sananene kuti ali ‘omangika . . . m’chiweruziro chomwecho,’ monga momwe mtumwi Paulo analimbikitsira Akristu. (1 Akorinto 1:10) Komabe, panthaŵi imodzimodziyo Akolejanti ankayembekezera nthaŵi pamene zikhulupiriro zazikulu zachikristu, monga umodzi wa malingaliro, zidzakhalapodi.
Polingalira kuti chidziŵitso cholondola chinali chisanachulukebe m’nthaŵi ya Akolejanti, iwo anapereka chitsanzo chimene zipembedzo zambiri lerolino zingatengerepo phunziro. (Yerekezani ndi Danieli 12:4.) Kugogomezera kwawo kufunika kwa phunziro la Baibulo kunali kogwirizana ndi uphungu wa mtumwi Paulo wakuti: “Tsimikizirani zinthu zonse.” (1 Atesalonika 5:21, NW) Phunziro laumwini la Baibulo linaphunzitsa Jacobus Arminius ndi ena kuti zikhulupiriro zina zomwe zinalipo kuyambira kale ndi miyambo ina sizinachokere m’Baibulo mpang’ono pomwe. Atazindikira zimenezi, iwo analimba mtima nachita zosiyana ndi zipembedzo zazikulu. Kodi inuyo mukadatero?
[Mawu a M’munsi]
a Mu 1610 okana chiphunzitsocho anatumiza kalata (remonstrance) kwa olamulira a Holland yofotokoza zifukwa zimene akuchikanira. Atatero, anatchedwa kuti Aremonisitiranti.
b Chifukwa cha malo ameneŵa, Akolejanti anali kutchedwanso kuti a Rijnsburger.
c Onani Galamukani! yachingelezi ya November 22, 1988, tsamba 19, “The Socinians—Why Did They Reject the Trinity?”
d Het Nieuwe Testament van onze Heer Jezus Christus, uit het Grieksch vertaald door Reijnier Rooleeuw, M.D. (Chipangano Chatsopano cha Ambuye Wathu Yesu Kristu, lotembenuzidwa kuchokera m’Chigiriki ndi Reijnier Rooleeuw, M.D.)
[Chithunzi patsamba 24]
Rembrandt van Rijn
[Zithunzi patsamba 26]
Mudzi wa Warmond kumene kunayambira Akolejanti, ndi Mtsinje wa De Vliet kumene maubatizo ankachitikira
[Mawu a Chithunzi patsamba 23]
Chithunzi: Courtesy of the American Bible Society Library, New York