“Kuloŵa m’Nyanja Yanamondwe”
KODI simungaone kuchita zimenezo panthaŵiyo kukhala kolakwika, kupusa, ndiponso koopsa kwambiri? Komabe, ena amadziloŵetsa mumkhalidwe woterowo m’njira ina. Motani? Wolemba nkhani wachingelezi wa m’zaka za zana la 17 Thomas Fuller anati: “Osachita kanthu utakwiya. Ndi kuloŵa m’nyanja yanamondwe.”
Kuchitapo kanthu utakwiya kwadzaoneni kungakhale ndi zotsatirapo zochititsa mantha. Chochitika china cholembedwa m’Baibulo chikusonyeza zimenezi. Simeoni ndi Levi, ana a Yakobo, kholo lamakedzana, anabwezera mwaukali mlongo wawo Dina ataipitsidwa. Chotsatirapo chake chinali chakuti anapha anthu ambiri ndi kufunkha katundu wochuluka. Ndiye chifukwa chake Yakobo anatsutsa chochita chawo choipacho, nati: “Mwandisautsa ndi kundinunkhitsa ine mwa anthu okhala m’dzikomu.”—Genesis 34:25-30.
Mwanzeru, Mawu a Mulungu, Baibulo, amayamikira njira ina. Amati: “Leka kupsa mtima, nutaye mkwiyo: usavutike mtima ungachite choipa.” (Salmo 37:8) Kutsatira uphungu umenewo kungatitetezere ku kuchita machimo aakulu.—Mlaliki 10:4; onaninso Miyambo 22:24, 25.