Mtendere wa Dziko Lonse—Kuchokera ku Gwero Liti?
KODI kugwirizanitsa maphunziro ndi zipembedzo padziko lonse kudzadzetsa mtendere? N’zimene akulakalaka zitachitika Dr. Robert Muller, amene kale anali wachiŵiri wa mlembi wamkulu wa United Nations amenenso anapatsidwa Mphotho ya UNESCO ya Maphunziro a Mtendere mu 1989. Monga momwe nyuzipepala ya The Vancouver Sun inanenera, Dr. Muller ali “wotsimikiza mtima kuti ophunzira onse padziko lapansi ayenera kuphunzitsidwa mfundo zazikulu zofanana ponena za pulaneti, kuganizira anthu ena ndi kusachita chiwawa.” Akulakalaka kuona tsiku pamene kuzungulira dziko lonse lapansi masukulu onse adzaphunzitsa ana za UN monga chiyembekezo chabwino koposa cha mtendere. Amakhulupiriranso kuti “zipembedzo zonse padziko lapansi ziyenera kukhala mamembala a bungwe latsopano longa UN lotchedwa kuti United Religions [Zipembedzo Zogwirizana],” inatero Sun. Pamenepo “ziphunzitso zonse zachipembedzo zidzachirikiza kusachita chiwawa.”
Kodi mtendere wa padziko lonse udzakhalapodi? Mosakayikira! Koma sudzadzetsedwa ndi bungwe lililonse la anthu. Zaka zoposa 2,700 zapitazo, wolemba wina wouziridwa anatchula gwero lapamwamba la maphunziro a mtendere pamene analosera kuti anthu owongoka mtima “adzaphunzitsidwa ndi Yehova,” ndipo mtendere wawo udzakhala “waukulu.”—Yesaya 54:13.
Mulungu ndiye “wopereka mtendere,” limatero Baibulo. (Aroma 16:20, NW) Ngakhale tsopano pologalamu yochititsa chidwi yamaphunziro ikuchitika padziko lonse pamene Yehova akulangiza anthu ake ‘kufunafuna mtendere ndi kuulondola,’ ‘kusula malupanga awo kukhala zolimira,’ ndi ‘kusaphunziranso nkhondo.’—1 Petro 3:11; Yesaya 2:2-4.
Mulungu amavomereza ndi kudalitsa kulambira kozikidwa pa choonadi, kopanda chinyengo ndi ukathyali. (Mateyu 15:7-9; Yohane 4:23, 24) Ndi kulambira koona kokha, kogwirizana kotheratu ndi Mawu a Mulungu, kumene kungapangitse anthu kukhala mumtendere ndi umodzi ndi kukhalanso ndi chikondi chenicheni pa wina ndi mnzake.—Yohane 13:35.
Kuti muphunzire zambiri ponena za zimene Mawu a Mulungu amanena ponena za mtendere wa padziko lonse, tikukupemphani kuti muyankhule ndi ofalitsa magazini ino.