Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 5/1 tsamba 26-27
  • Dziko la Avenda Lobala Zipatso Zambiri

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Dziko la Avenda Lobala Zipatso Zambiri
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Chinenero Chovuta
  • Zipatso Zauzimu
Nsanja ya Olonda—1999
w99 5/1 tsamba 26-27

Dziko la Avenda Lobala Zipatso Zambiri

KWA zaka khumi zapitazo, ine ndi mkazi wanga takhala tili alaliki a nthaŵi zonse, ndipo tagwira ntchitoyi kwawo kwa Avenda. Avenda amakhala kummwera kwa Mtsinje wa Limpopo womwe uli kumpoto kwa South Africa, ndipo mtundu wawo n’ngwa anthu a mitundu ingapo amene anawoloka Limpopo kalekale. Avenda ena amati makolo awo anayamba kukhala kumeneko zaka zoposa 1,000 zapitazo.

Zoonadi, chigawo chimenechi poyamba chinali cha anthu akalekale a Ufumu wa Mapungubwe. Ufumu wa Mapungubwe unali tauni yaikulu yoyamba ku South Africa, ndipo unali kulamulira dera lonse la chigwa chachikulu cha Mtsinje wa Limpopo, kuchokera ku Botswana cha kumadzulo mpaka ku Mozambique cha kummaŵa. Cha m’ma 900 C.E. mpaka 1100 C.E., amalonda achiluya ankagula minyanga ya njobvu, nyanga za chipembere, zikopa za nyama, mkuwa, ngakhalenso golidi ku ufumu wa Mapungubwe. Zinthu zosemedwa mwaluso n’kukutidwa ndi golidi zinafukulidwa pa kaphiri kotchedwa Mapungubwe, pomwenso panali manda a banja lachifumu. Buku lina la insaikulopediya linanena kuti zinthu zimenezo ndizo “umboni wina wosonyeza kuti kummwera kwa Africa ankakumbako golidi.”

Koma masiku ano kumeneko sakumbakonso golidi. Lero, dziko la Avenda n’lotchuka chifukwa cha kubala zipatso zambiri. Kummwera kwa Mapiri a Soutpansberg kuli chigwa china chachonde kwambiri kumene kuli mitengo yambiri ya zipatso monga mapeyala, nthochi, mango, ndi magwafa. Kusiyapo mtedza wina wa pecan ndi wa macadamia umene umapezeka kumeneko, kulinso ndiwo zamasamba zambiri. Zimenezi zimaphatikizapo ndiwo zamasamba zomera zokha zotchedwa moroho, ndipo m’kamwamu zimakhala ngati spinach ndipo anthu a kumeneko amazikonda zedi.

Avenda ndi anthu amtendere ndipo okonda kuchereza alendo. Si kaŵirikaŵiri kuti bambo wapamudzi alephere kuuza mkazi wake kuphikira mlendo nkhuku, ngakhale ngati mlendoyo wangofika mwadzidzidzi. Nkhukuyo amaidyera pamodzi ndi vhuswa, chakudya cha masiku onse, chophika ndi ufa wachimanga. Mlendoyo atatsazika, bambo wapamudzipo amam’perekeza mlendo wakeyo n’kukam’siya chapatali. Umenewo ndiwo mwambo wawo wochitira ulemu alendo. Ana amawaphunzitsa kupatsa alendo moni mwaulemu mwa kuŵerama n’kupereka manja onse aŵiri. Akazi aŵiri mukuona patsamba lino ndi Avenda, akupatsana moni wa mwambo womwewu tikunena pano.

Chinenero Chovuta

Chivenda n’chovuta kwambiri kwa anthu a ku Ulaya kuchiphunzira. Chovuta china n’chakuti mawu ambiri amawalemba mofanana koma amawatchula mosiyana. Tsiku lina ndinkakamba nkhani ya Baibulo pampingo wachivenda wa Mboni za Yehova, ndiye ndinkayesa kulimbikitsa omvetsera kulankhula ndi munthu aliyense. Munthu wina mwa omvetserawo anangofa n’kuseka chifukwa ndinati “chala chilichonse” m’malo moti nditi “munthu aliyense.”

Pamene ndinkayesa kulankhula Chivenda kwa nthaŵi yoyamba pantchito yochitira umboni poyera, mayi wina wachivenda anayankha kuti: “Sindilankhula Chingelezi.” Ndinkayesa kuti ndalankhula Chivenda chomveka, koma mkaziyo anamva ngati kuti chinali Chingelezi! Tsiku lina ndinafika panyumba ina, ndiye ndinapempha kamwana kuti kakandiitanire bambo wa m’banjalo. Avenda akamatchula mutu wa m’banja amati thoʹho. Ndinalakwa ndi kunena kuti thohoʹ, kumene kunali kupempha kulankhula ndi nyani wa m’nyumbamo! Zimenezo zinkandifooketsa kwambiri, koma tinalimbikirabe, moti ine ndi mkazi wanga tsopano tikulankhula bwino Chivenda.

Zipatso Zauzimu

Tsopano dziko la Avenda layamba kubala zipatso mwauzimu. Cha m’ma 1950, anthu ena ochokera m’mayiko apafupi anabwera kudzagwira ntchito pamgodi wa mkuwa m’tauni ina ya Messina, ndiye kumenekoko kunakhazikitsidwa mpingo wa Mboni za Yehova. Ankalalikira mwachangu moti Avenda ambiri anamva choonadi cha Baibulo. Patapita zaka khumi, gulu lina la Mboni zachivenda linali kusonkhana m’nyumba ya munthu wina m’tauni ya Sibasa.

Nthambi ya Watch Tower Society ku South Africa inatumiza alaliki anthaŵi zonse kumunda wachonde umenewo kuti ntchito igwirike msanga. Posakhalitsa gulu la ku Sibasa limenelo linakhala mpingo waukulu. Panthaŵi imeneyo tinkachitira misonkhano yachikristu m’kalasi. Komabe, cha kummwera, pamtunda wa makilomita 160, kuli tauni ya Pietersburg, ndiye Mboni za kumeneko zinatithandiza kumanga Nyumba ya Ufumu ku Thohoyandou, tauni yoyandikana ndi kumeneko.

Anthu olankhula Chivenda kumpoto kwa South Africa amaposa 500,000. Pamene ntchito yolalikira Ufumu inayambika kumeneko m’ma 1950, kunalibe Mboni zachivenda. Tsopano kuli oposa 150. Komabe kukadali madera ena amene sikunafikebe alaliki ndipo padakali ntchito yoti igwiridwe. Mu 1989 tinayamba kuchezera mudzi wina wa Avenda wotchedwa Hamutsha. Panthaŵi imeneyo kunali Mboni imodzi basi. Tsopano m’mudzi umenewo muli olengeza Ufumu oposa 40. Tili kalikiliki kufuna kumaliza Nyumba yathu ya Ufumu, mothandizidwanso ndi Mboni za m’mipingo ya ku Pietersburg ndi ndalama zimene amapereka abale a m’mayiko olemera.

Timakhala mu caravan (ngolo yaing’ono) pafamu. Chifukwa chakuti timakhala moyo wosalira zambiri, timakwanitsa kuyendera anthu ambiri kukawauza uthenga wabwino. (Marko 13:10) Choncho, Yehova Mulungu watidalitsa kwambiri ndi mwayi wakuthandiza anthu ochuluka kudzipatulira kwa iye. Mwachitsanzo, pali munthu wina wotchedwa Michael, iyeyu anaona, ali m’nyumba ya mnzake wina, buku lakuti Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi.a Anayamba kuliŵerenga ndipo nthaŵi yomweyo anazindikira kuti chinali choonadi. Ndiyeno analembera ku Watch Tower Society napempha mabuku enanso ofotokoza za Baibulo. Michael anafotokoza m’kalata yakeyo kuti anali atangobatizidwa kumene monga wa tchalitchi cha Apostolic. Ndiye anapitiriza kuti: “Ndaona kuti ndasochera, njira yopita ku Ufumu wa Mulungu si imeneyi iyayi. Ndaganiza kuti ndikhale wa inuyo, koma sindikudziŵa kuti nditani.” Kenaka anawauza adiresi yake n’kuwapempha kuti am’tumizire wina wa Mboni za Yehova akam’thandize. Ndinam’peza Michael ameneyo n’kuyamba naye phunziro la Baibulo lapanyumba. Lero, ndi Mboni yobatizidwa ndipo akutumikira Yehova mokhulupirika.

Mu December 1997, tinakhala nawo pa Msonkhano Wachigawo wa Mboni za Yehova, wakuti “Kukhulupirira Mawu a Mulungu,” mu bwalo lamaseŵero ku Thohoyandou. Panali anthu okwana 634, ndipo atsopano okwana 12 anabatizidwa. Ndinali ndi mwayi wokambapo nkhani ziŵiri m’Chivenda. Chimenecho chinali chosaiŵalika m’moyo wathu wachimwemwe pazaka khumi zimene tatumikira m’dziko lobala zipatso zambiri limeneli!​—Yoperekedwa.

[Mawu a M’munsi]

a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena