Mpingo Wachikristu—Gwero la Chitonthozo
POPI, mkazi wazaka za m’ma 20, anali wokhumudwa kwambiri chifukwa cha vuto losautsa m’banja. Vutolo linali kusalankhulana momasuka ndi makolo ake.a Atafotokozera mkulu wina wachikristu ndi mkazi wake zonse zimene anali nazo kukhosi, analemba kuti: “Zikomo kwambiri pokhala ndi nthaŵi yolankhula ndi ine. Simungadziŵe mmene ndikuyamikirira kukoma mtima kwanu. Ndikuthokoza Yehova pondipatsa anthu amene ndingakhulupirire komanso amene ndingalankhule nawo.”
Toula, mkazi amene ali ndi ana achinyamata aŵiri komanso amene anafedwa mwamuna wake posachedwapa, anali ndi zothetsa nzeru zazikulu zopsinja mtima komanso vuto la ndalama. Iyeyo ndi ana ake ankachezeredwa nthaŵi zonse ndi banja lina lachikristu mumpingo wawo. Atagonjetsa mavuto akewo, anatumizira khadi ku banjalo, nati: “Nthaŵi zonse ndimakukumbukirani m’mapemphero anga. Ndimakumbukira nthaŵi zambiri zimene munandithandiza ndi kundichirikiza.”
Kodi inuyo nthaŵi zina mumadzimva ‘wothodwa’ chifukwa cha zipsinjo zambiri za dzikoli? (Mateyu 11:28) Kodi “nthaŵi ndi zochitika zosadziŵika” zasokoneza moyo wanu ndi masoka? (Mlaliki 9:11, NW) Ndiye simuli nokha. Koma mofanana ndi zimene anthu opsinjika mtima zikwizikwi apeza, inunso mungapeze thandizo lofunika kwambiri mumpingo wachikristu wa Mboni za Yehova. M’zaka za zana loyamba C.E., mtumwi Paulo anaona kuti ena mwa okhulupirira anzake analidi ‘otonthoza mtima’ kwa iye. (Akolose 4:10, 11) Inunso zimenezi zingakuchitikireni.
Chichirikizo ndi Thandizo
M’Malemba Achigiriki Achikristu, liwu lotembenuzidwa kuti “mpingo” ndi liwu lachigiriki lakuti ek·kle·siʹa, limene limatanthauza gulu la anthu osonkhanitsidwa. Liwu limenelo lingaliro lake lenileni ndi la umodzi ndi kuchirikizana.
Mpingo wachikristu umachirikiza choonadi cha Mawu a Mulungu ndipo umalalikira uthenga wabwino wa Ufumu wake. (1 Timoteo 3:15; 1 Petro 2:9) Komanso, mpingo umapereka chichirikizo chauzimu ndi thandizo kwa anthu ake. Mumpingomo, munthu angapeze mabwenzi achikondi, odera nkhaŵa, ndi okoma mtima, amene ali okonzeka ndi ofunitsitsa kuthandiza ndi kutonthoza ena panthaŵi ya nsautso.—2 Akorinto 7:5-7.
Nthaŵi zonse olambira Yehova apeza chitetezo ndi chisungiko mumpingo wake. Wamasalmo anasonyeza kuti anapeza chimwemwe ndi chisungiko pakati pa anthu osonkhana a Mulungu. (Salmo 27:4, 5; 55:14; 122:1) Lerolinonso, mpingo wachikristu ndi gulu la anthu achikhulupiriro chimodzi amene amamangirirana ndi kulimbikitsana.—Miyambo 13:20; Aroma 1:11, 12.
Anthu mumpingo amaphunzitsidwa ‘kuchitira onse chokoma, koma makamaka iwo apabanja [lawo] la chikhulupiriro.’ (Agalatiya 6:10) Maphunziro ozikidwa pa Baibulo amene amalandira amawasonkhezera kuonetsa chikondi cha pa abale ndi kukondana wina ndi mnzake. (Aroma 12:10; 1 Petro 3:8) Abale achikristu ndi alongo amasonkhezereka kukhala okoma mtima, amtendere, komanso achifundo. (Aefeso 4:3) M’malo mongokhala olambira mwamwambo, iwo amasonyeza nkhaŵa yachikondi kwa ena.—Yakobo 1:27.
Ndiye chifukwa chake opsinjika amapeza mzimu wogwirizana mumpingo wonga uja umene umapezeka m’banja lenileni. (Marko 10:29, 30) Kudzimva kwawo kuti ali m’gulu logwirizana kwambiri komanso limene anthu ake amakondana kumawalimbikitsa. (Salmo 133:1-3) Kupyolera mu mpingo, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amapereka ‘chakudya chauzimu panthaŵi yake’ chopatsa thanzi.—Mateyu 24:45.
Kulandira Thandizo kwa Oyang’anira Achikondi
Anthu a mumpingo wachikristu angayembekezere kupezamo abusa achikondi, omvetsa, ndi okhoza bwino amene amapereka chichirikizo chauzimu ndi chilimbikitso. Abusa amene ali ndi mikhalidwe imeneyi ali ngati “pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo.” (Yesaya 32:1, 2) Akulu oikidwa ndi mzimu, kapena kuti oyang’anira, amasamala anthu a Mulungu onga nkhosa, kulimbikitsa odwala ndi opsinjika, ndi kuyesetsa kubweza amene alakwa.—Salmo 100:3; 1 Petro 5:2, 3.
Zoona, bungwe la akulu pampingo silili gulu la madokotala kapena asing’anga ochiritsa matenda m’thupi kapena m’maganizo amene okhulupirira anzawo amadwala ayi. M’dongosolo ili la zinthu, odwala ‘afunabe sing’anga.’ (Luka 5:31) Ngakhale ndi choncho, abusa amenewo angathandize aja amene akusoŵa mwauzimu. (Yakobo 5:14, 15) Pamene kuli kotheka, akulu amakonzanso zopereka thandizo lina.—Yakobo 2:15, 16.
Kodi amene amachirikiza makonzedwe achikondi amenewa ndani? Yehova Mulungu mwiniyo! Mneneri Ezekieli akufotokoza Yehova kukhala akunena kuti: “Nidzapwaira nkhosa zanga ndi kuzifunafuna. . . . Ndidzawalanditsa m’malo monse anabalalikamo . . . Ine ndekha ndidzadyetsa nkhosa zanga, ndi kuzigonetsa.” Mulungu amasamalanso za nkhosa zolefuka ndi zofooka.—Ezekieli 34:11, 12, 15, 16.
Thandizo Lenileni pa Nthaŵi Yake
Kodi thandizo lenileni lilimodi mumpingo wachikristu? Inde, ndipo zitsanzo zotsatira zikusonyeza mikhalidwe yosiyanasiyana pamene mpingo ungathandize.
◆ Kufedwa wokondedwa wathu. Mwamuna wa Anna anamwalira pambuyo podwala nthaŵi yaitali. “Kuyambira nthaŵi imeneyo, ndasonyezedwa chikondi ndi abale anga achikristu,” iye akutero. “Mawu olimbikitsa amene okhulupirira anzanga sasiya kundiuza, kuphatikizapo kundikumbatira kwawo ndi mtima wonse, zandithandiza kukhalabe wachimwemwe m’malo mokhala wopsinjika kotheratu, ndipo ndikuthokoza Yehova. Chikondi chawo chandichititsa kuona kuti ndikuchirikizidwa kwambiri, kulimbikitsidwa, komanso kusamalidwa kwabasi.” Mwina inunso munafedwapo wokondedwa wanu. Nthaŵi ngati imeneyo, mpingo ungapereke chitonthozo chofunika koposacho komanso kukulimbitsani mtima.
◆ Matenda. Arthur, woyang’anira woyendayenda wa ku Poland, ankachezera mipingo ku Central Asia mokhazikika kuilimbikitsa mwauzimu. Paulendo wake wina, anadwala kwambiri ndipo kuchira kwake kunavuta zedi. “Ndikufuna kukuuzani mmene abale ndi alongo [mumzinda wina ku Kazakhstan] anandisamalira,” anatero Arthur poyamikira. “Abale ndi alongo, ambiri amene sindikuwadziŵa—ndi okondwerera omwe—anandibweretsera ndalama, chakudya, ndi mankhwala. . . . Komanso anatero ndi chimwemwe chachikulu.
“Taganizirani mmene ndinamvera nditalandira envulopu yokhala ndi ndalama limodzi ndi kalata yakuti: ‘Mbale Wokondedwa, landirani moni wanga wamafuta. Amayi anandipatsa ndalama ya ayezikirimu, koma ndaganiza zokupatsani kuti mukagulire mankhwala. Ndikufunirani kuchira kwamsanga. Yehova akutifuna kwanthaŵi yaitali. Ndikuti mafuno abwino. Ndipo tatiuzaninso nkhani zina zabwino komanso zophunzitsa zija. Vova.’” Inde, malinga ndi chitsanzochi, achichepere ndi achikulire mumpingo amapereka chitonthozo pamene tikudwala.—Afilipi 2:25-29.
◆ Kupsinjika maganizo. Teri ankasangalala kwambiri kukhala mpainiya, kapena kuti mlaliki wa Ufumu wanthaŵi zonse. Koma chifukwa cha zovuta zina, anasiya upainiya. “Ndinadzimva wamlandu kwambiri poyesa kutumikira paudindo umenewu kwinaku n’kulephera kukwanitsa chaka chathunthu,” iye anatero. Teri ankaganiza molakwa kuti chiyanjo cha Yehova chinadalira kuchuluka kwa zimene angachite pom’tumikira. (Siyanitsani ndi Marko 12:41-44.) Chifukwa chopsinjika maganizo kwambiri, anadzipatula kwa ena onse. Komano thandizo lotsitsimula linachokera ku mpingo.
Nazi zimene Teri akukumbukira: “Mlongo wina wachikulire mpainiya sanazengereze kundithandiza ndipo anamvetsera pamene ndinkamuuza zonse zakukhosi. Pochoka panyumba pake, ndinamva ngati kuti winawake wanditula chikatundu cholemera. Kuyambira tsiku lomwelo, mlongo ameneyu mpainiya ndi mwamuna wake, amenenso ndi mkulu mumpingo, anandithandiza kwambiri. Ankandiimbira foni tsiku ndi tsiku kundifunsa mmene ndinalili. . . . Nthaŵi zina amandilola kukhala nawo paphunziro lawo la banja, limene landithandiza kuona kufunika koti mabanja azikhala ogwirizana kwambiri.”
Ambiri—ngakhale Akristu odzipatulira—amapsinjika mtima, kukhumudwa, ndi kusungulumwa. Tikuthokoza kwambiri pokhala ndi thandizo lachikondi ndi lopanda dyera mumpingo wa Mulungu!—1 Atesalonika 5:14.
◆ Masoka ndi ngozi. Taganizani kuti muli m’banja la anthu anayi limene linataya katundu wawo yense pamene nyumba yawo inapsa. Posakhalitsa anaona zimene anatcha “chochitika cholimbikitsa chimene sitidzaiŵala komanso chimene chinatitsimikizira za chikondi chenicheni chimene anthu a Yehova ali nacho.” Akufotokoza kuti: “Zimenezo zitangochitika, tinalandira mauthenga ambiri a pafoni ochokera pansi pa mtima kuchokera kwa abale athu auzimu ndi alongo otilimbikitsa ndi otiuza za chisoni chawo. Foni inkangoimba osasiya. Nkhaŵa ya aliyense komanso chikondi chawo zinali zenizeni komanso zinatikhudza mtima kwambiri moti tinagwetsa misozi chifukwa choyamikira.”
Posapita nthaŵi, akulu analinganiza gulu la abale mumpingo, ndipo m’masiku oŵerengeka, banja limeneli analimangira nyumba yatsopano. Munthu wina woyandikana naye anati: “Kaoneni zimene zikuchitika! Kuli anthu osiyanasiyana amene akugwira ntchito—amuna, akazi, akuda, ndi a Hispanic!” Umenewu unali umboni woonekeratu wa chikondi cha pa abale.—Yohane 13:35.
Akristu anzawo anapatsa banjali zovala, chakudya, ndi ndalama. Atate awo anati: “Nthaŵi imeneyi inali ya Khirisimasi pamene ambiri amakhala akupereka mphatso, koma tikunena mochokera pansi pa mtima kuti palibe wina aliyense amene anaona kuolowa manja kwenikweni komanso kopambana ngati kumene tinaona.” Ndipo anawonjezera kuti: “Tikuiŵala pang’onopang’ono za motowo. M’malo mwake, tikukumbukira kwambiri kukoma mtimako ndi mabwenzi abwino amenewo. Tikuthokoza Yehova, Atate wathu wakumwamba komanso wachikondi pokhala ndi banja lodabwitsa komanso logwirizana ndi abale padziko lapansi, ndipo tikuyamikira kukhala m’banjalo!”
Inde, sikuti nthaŵi iliyonse imene pachitika tsoka ndiye kuti zonsezi zingatheke kapenanso tingaziyembekezere. Koma chochitikachi chikusonyeza mmene mpingo ungaperekere chichirikizo.
Nzeru Yochokera Kumwamba
Ambiri apeza gwero lina la chithandizo ndi nyonga mumpingo wachikristu. Lotani? Zofalitsa zokonzedwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” Zodziŵika kwambiri mwa zimenezi ndi magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! Kuti zipereke uphungu wanzeru ndi malangizo othandiza, zofalitsa zimenezi zimadalira kwambiri nzeru yaumulungu yopezeka m’Baibulo. (Salmo 119:105) Pa chidziŵitso cha m’Malemba chimenechi pamawonjezedwa kufufuza kosamala komanso kodalirika pankhani zonga kuchita tondovi, kuiŵala nkhanza zimene munthu anachitidwa, mavuto osiyanasiyana a kakhalidwe ndi zachuma, zothetsa nzeru zimene achinyamata amakumana nazo, ndi mavuto a m’mayiko amene akutukuka. Makamaka, zofalitsa zimenezi zimachirikiza njira ya Mulungu kuti ndiyo njira yokha ya moyo yoposa.—Yesaya 30:20, 21.
Chaka chilichonse Watch Tower Society imalandira makalata zikwizikwi oyamikira. Mwachitsanzo, ponena za nkhani ya mu Galamukani! yonena za kudzipha, mnyamata wina ku Russia analemba kuti: “Chifukwa chochita tondovi nthaŵi zambiri, . . . nthaŵi zingapo ndinaganiza zodzipha. Nkhani imeneyi inalimbitsa chikhulupiriro changa chakuti Mulungu andithandiza kulimbana ndi mavuto anga. Iye akufuna kuti ineyo ndikhale ndi moyo. Ndikumuthokoza pondichirikiza kupyolera m’nkhani imeneyi.”
Ngati mwaona kuti mukulephera kudutsa mavuto osalekeza a m’dzikoli onga chimkuntho, dziŵani kuti malo achisungiko ali mumpingo wachikristu. Inde, ngati dongosolo ili lopanda chikondi longa chipululu chouma likulefulani, mungapeze chitsime chotsitsimula m’gulu la Yehova. Mutaona chichirikizo chimenecho, inunso munganene zimene ananena mkazi wina wachikristu amene anakhoza kupirira matenda oopsa a mwamuna wake nalemba kuti: “Chifukwa cha chikondi ndi chisamaliro chimene anationetsa, ndimaona ngati kuti Yehova anatinyamula m’dzanja lake kudutsa vuto limeneli. Ndikuthokoza kwambiri pokhala m’gulu la Yehova labwino chotere!”
[Mawu a M’munsi]
a Maina asinthidwa.
[Zithunzi patsamba 26]
Tingapereke chitonthozo kwa odwala, ofedwa, ndi enanso