Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 6/1 tsamba 8
  • “Zinthu Zonse Zitheka ndi Mulungu”

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • “Zinthu Zonse Zitheka ndi Mulungu”
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Nkhani Yofanana
  • Kuyamikira Chichilikizo CHosalekeza cha Yehova
    Nsanja ya Olonda—1993
  • Kuchokera ku Tondovi Kumka ku Chimwemwe
    Nsanja ya Olonda​—1990
  • “Yehova, Mwandipeza!”
    Galamukani!—2004
Nsanja ya Olonda—1999
w99 6/1 tsamba 8

Olengeza Ufumu Akusimba

“Zinthu Zonse Zitheka ndi Mulungu”

MAWUWA, opezeka pa Mateyu 19:26, anakhala oona kwa mkazi wina ku Venezuela. Ataphunzira kudalira Yehova kotheratu, anakhoza kugonjetsa vuto lalikulu. Iye akuti:

“Agogo anga aakazi anali okoma mtima komanso achifundo kwambiri. Tsoka lake n’lakuti anamwalira pamene ndinali ndi zaka 16. Imfa yawo inandikhudza kwambiri. Ndinasweka mtima, ndipo sindinafune ngakhale kutuluka kunja kwa nyumba. Zotsatira zake zinali zoti ndinatsala pang’ono kuzoloŵera moyo wokhala ndekhandekha nthaŵi zonse.

“Sindinapite kusukulu, ndipo sindinkagwira ntchito. Ndinkangokhala m’chipinda mwanga. Pokhala wosungulumwa ndi wopanda mabwenzi, ndinachita tondovi kwambiri. Ndinadzimva kukhala wopanda pake ndipo ndinafuna kudzipha kuti zonse zithe. Ndinkadzifunsa kuti, ‘Ndikukhaliranji ndi moyo?’

“Amayi ankalandira magazini a Nsanja ya Olonda ndi Galamukani! kwa Mboni yachichepere dzina lake Gisela. Tsiku lina amayi anaona Gisela akudutsa pafupi ndi nyumba yathu ndipo anam’pempha kudzandithandiza. Gisela anavomera kuti ayese, koma ine ndinakana kuti sindifuna kumuonanso. Zimenezi sizinam’lefule Gisela. Anandilembera kalata kundiuza kuti akufuna kuti ndikhale mnzake ndi kuti munthu wina wofunika kwambiri kuposa iye akufunanso kuti akhale mnzanganso. Iye anati munthu ameneyo ndi Yehova Mulungu.

“Zimenezi zinandikhudza kwambiri ndipo ndinayankha kalata yake. Tinalemberana makalata miyezi itatu. Pomaliza pake ndinalimba mtima kukumana ndi Gisela pambuyo pakuti iyeyo wayesetsa kundiumiriza ndi kundilimbikitsa. Titakumana ulendo woyamba, Gisela anaphunzira nane Baibulo, kugwiritsa ntchito buku la Mungathe Kukhala ndi Moyo Kosatha m’Paradaiso pa Dziko Lapansi. Pambuyo pa phunziro anandipempha kupita kumsonkhano ku Nyumba ya Ufumu yakwathu. Ndinadabwa. Sindinkatuluka m’nyumba zaka zinayi, ndipo ndinachita mantha n’tanganiza zokayenda mumsewu.

“Gisela ankaleza nane mtima kwambiri. Anandiuza kuti palibe choopera komanso kuti adzatsagana nane kumisonkhanoko. Pomaliza ndinavomera. Titafika ku Nyumba ya Ufumu, ndinayamba kunjenjemera ndi kutuluka thukuta. Ndinalephera kupereka moni kwa aliyense. Komabe, ndinavomera kuti ndizipitabe kumisonkhano, ndipo Gisela sankalephera kudzanditenga mlungu uliwonse.

“Pofuna kundithandiza kuthetsa mantha angawo, Gisela ankapita nane kumisonkhano mofulumirirapo. Tinkaima pakhomo ndi kupereka moni kwa aliyense wofika. Mwanjira imeneyo ndinalankhula ndi munthu mmodzi kapena aŵiri, m’malo mwa gulu lonse nthaŵi imodzi. Nditamva kuti sindipiriranso zimenezo, Gisela ankagwira mawu Mateyu 19:26 kuti: ‘Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.’

“Ngakhale kuti zinali zovuta, m’kupita kwa nthaŵi ndinakhoza kufika ngakhale pakhamu lalikulu la anthu pamsonkhano wadera. Pamenepo ndinakhoza kwambiri! M’September 1995, ndinalimba mtima ndipo ndinauza akulu kuti ndikufuna kumachita nawo utumiki wakunyumba ndi nyumba. Patapita miyezi isanu ndi umodzi, mu April 1996, ndinasonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova mwa kubatizidwa m’madzi.

“Pamene wina anandifunsa posachedwapa kuti zinatheka bwanji kuti ndilimbe mtima ndi kuchita zimenezi, ndinam’yankha kuti: ‘Chikhumbo changa chokondweretsa Yehova chimaposa mantha anga.’ Ngakhale kuti nthaŵi zina ndimachitabe tondovi, kutumikira kwanga monga mpainiya wokhazikika kumawonjezera chimwemwe changa. Ndikayang’ana m’mbuyomu, ndimavomerezana ndi Gisela. Tsopano ndili ndi Bwenzi limene limandikonda komanso ‘limandipatsa mphamvu.’”​—Afilipi 4:13.

[Zithunzi patsamba 8]

“Chikhumbo changa chokondweretsa Yehova chimaposa mantha anga”

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena