Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 6/1 tsamba 20-23
  • Kusunga Lonjezo Langa Lotumikira Mulungu

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kusunga Lonjezo Langa Lotumikira Mulungu
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Kukula Kwanga ku Lithuania
  • Kusunga Lonjezo Langa
  • Ziyeso Zoyambirira pa Chikhulupiriro Changa
  • Chiletso ndi Kumangidwanso
  • Kusunga Chikhulupiriro m’Ndende
  • Kuyambiranso Utumiki Wanthaŵi Zonse
  • Zosoŵa Zosinthitsa Zinthu
  • Ndinalimbikitsidwa ndi Kukhulupirika kwa Banja Lathu kwa Mulungu
    Galamukani!—1998
  • Kudikirabe Yehova Moleza Mtima Kuyambira Ubwana Wanga
    Nsanja ya Olonda—1997
  • Tinayesetsa Kuti Tikhale Olimba Mwauzimu
    Nsanja ya Olonda—2006
  • Mulungu Ndiye Pothaŵira Panga ndi Mphamvu Yanga
    Nsanja ya Olonda—1997
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 6/1 tsamba 20-23

Kusunga Lonjezo Langa Lotumikira Mulungu

YOSIMBIDWA NDI FRANZ GUDLIKIES

Asilikali anayi okha mwa gulu lathu la oposa zana limodzi ndiwo anatsala amoyo. Poyang’anizana ndi imfa, ndinagwada ndi kulonjeza Mulungu kuti, ‘Ndikapulumuka nkhondoyi, ndidzakutumikirani nthaŵi zonse.’

LONJEZO limenelo ndinalipanga zaka 54 zapitazo, mu April 1945, pamene ndinali msilikali m’gulu la nkhondo la Germany. Panthaŵiyo, Nkhondo Yadziko II inali itatsala pang’ono kutha, ndipo gulu la nkhondo la Soviet Union linali kuyesetsa ndithu kufika ku Berlin. Ifeyo tinali pafupi ndi tauni ya Seelow ku Mtsinje wa Oder, makilomita osakwanira 65 kuchokera ku Berlin. Kumeneko tinaomberedwa mwamphamvu usiku ndi usana, ndipo gulu lathu linasakazidwa kwambiri.

Nthaŵi imeneyo koyamba m’moyo mpamene ndinalira ndi kupemphera kwa Mulungu misozi ilikugwa. Ndinakumbukira mawu a m’Baibulo amene amayi anga oopa Mulungu ankawatchula nthaŵi zambiri akuti: “Undiitane tsiku la chisautso: ndidzakulanditsa, ndipo iwe udzandilemekeza.” (Salmo 50:15) Ndili kumeneko m’maenje kwinaku mantha akuti ndikufa atandigwira, ndinalonjeza Mulungu mawu amene ndatchulawo. Kodi zinatheka bwanji kuti ndisunge lonjezolo? Ndipo zinachitika bwanji kuti ndiloŵe m’gulu la nkhondo la Germany?

Kukula Kwanga ku Lithuania

Mu 1918, m’kati mwa Nkhondo Yadziko I, dziko la Lithuania linalengeza kuti lapata ufulu wake wodzilamulira ndipo linakhazikitsa boma la demokalase. Ndinabadwa mu 1925 m’chigawo cha Memel (Klaipėda) pafupi ndi nyanja ya Baltic Sea. Chigawo chimenecho chinali chitakhala mbali ya Lithuania patapita chaka chimodzi ine ndisanabadwe.

Ubwana wathu ineyo ndi achemwali anga asanu unali wosangalatsa. Atate anali ngati mnzathu wapamtima, nthaŵi zonse ankachita zinthu limodzi ndi anafe. Makolo athu anali mamembala a Tchalitchi cha Evangelical, koma sankapita kumapemphero chifukwa amayi anakhumudwa ndi chinyengo cha wansembe. Koma ankakonda Mulungu ndi Mawu ake, Baibulo, limene ankaŵerenga mwakhama.

Mu 1939, Germany analanda mbali ya Lithuania kumene tinkakhala. Kenako, kumayambiriro a 1943, anandiitana kukaloŵa usilikali m’gulu la nkhondo la Germany. Nthaŵi ina pomenya nkhondo ndinavulala, koma zilonda zitapola, ndinabwereranso kunkhondo ku Malire a Kummaŵa. Panthaŵiyi n’kuti zinthu zitasintha pankhondoyo ndipo Ajeremani anali kuthaŵa asilikali a Soviet Union. Apa m’pamene ndinatsala pang’ono kuphedwa, zimene ndasimba m’mawu oyamba.

Kusunga Lonjezo Langa

M’kati mwa nkhondoyo, makolo anga anasamukira ku Oschatz, ku Germany, kumwera chakum’maŵa kwa Leipzig. Nkhondo itatha, zinali zovuta kuwapeza. Koma tinasangalala kwabasi pamene tinakumananso! Posakhalitsa, mu April 1947, ndinatsagana ndi amayi kukamvetsera nkhani yapoyera ya Max Schuber, wa Mboni za Yehova. Amayi anakhulupirira kuti apeza chipembedzo choona, ndipo titapita nawo ku misonkhano ingapo, inenso ndinakhulupirira zimenezo.

Posapita nthaŵi, amayi anagwa pamakwerero, ndipo anavulala, kenako anamwalira patapita miyezi ingapo. Ali m’chipatala asanamwalire, anandilimbikitsa kwambiri kuti: “Ndakhala ndikupemphera nthaŵi zambiri kuti wina mwa ana anga apeze njira ya Mulungu. Panopo ndaona kuti mapemphero anga ayankhidwa, ndipo ndifa ndi mtendere.” Mmene ndimalakalakira nthaŵi pamene amayi adzauka kwa akufa ndi kudziŵa kuti mapemphero awo anakwaniritsidwa!​—Yohane 5:28.

Pa August 8, 1947, patangopita miyezi inayi kuchokera pamene Mbale Schuber anakamba nkhani yake, ndinabatizidwa pamsonkhano ku Leipzig kusonyeza kudzipatulira kwanga kwa Yehova Mulungu. Tsopano ndinali kutsatira masitepe okwaniritsira lonjezo langa kwa Mulungu. Posakhalitsa ndinakhala mpainiya, mmene Mboni za Yehova zimatchera atumiki anthaŵi zonse. Nthaŵiyo panali apainiya pafupifupi 400 omwe ankakhala m’dera limene linadzatchedwa German Democratic Republic, kapena kuti East Germany.

Ziyeso Zoyambirira pa Chikhulupiriro Changa

Munthu wina wachinansi ku Oschatz anayesa kundikopa ndi chiphunzitso cha Marx, akumandiuza kuti Boma likandilipirira maphunziro akuyunivesite ndikaloŵa m’chipani cha Socialist Unity Party of Germany (SED). Ndinakana, monga momwenso Yesu anakanira kwa Satana.​—Mateyu 4:8-10.

Tsiku lina mu April 1949, apolisi aŵiri anafika kuntchito kwathu nandilamula kuwatsatira. Anandipereka ku ofesi ya bungwe la Soviet Union lofufuza za adani kumene anandiimba mlandu wogwirizana ndi ochirikiza chikapitolizimu a Kumadzulo. Anandiuza kuti ngati ndikufuna kuwatsimikiza kuti ndilibe mlandu, ndizichitabe ntchito yanga ya kunyumba ndi nyumba komano ndiziwauza za aliyense amene anenera zoipa Soviet Union kapenanso chipani cha SED kapena za aliyense wofika pamisonkhano ya Mboni za Yehova. Nditakana, ananditsekera m’selo yapapolisi. Pambuyo pake anandipereka pamaso pa limene linali ngati khothi la asilikali. Chilango chimene anandilamula: zaka 15 zogwira ntchito yachibalo ku Siberia!

Ndinangokhala phe osatekeseka, ndipo zimenezo zinachititsa chidwi asilikaliwo. Kenako anandiuza kuti chilango changacho chikhala momwemo koma kuti ndizingopita kwa iwo kukaonekera kamodzi pamlungu kufikira n’takonzeka kugwirizana nawo. Pofuna kupempha nzeru kwa Mboni zofikapo, ndinapita ku Magdeburg, kumene nthaŵiyo kunali ofesi ya nthambi ya Watch Tower Society. Ulendowo sunali wapafupi, pakuti ankandiyang’anira. Ernst Wauer, amene anali ku Dipatimenti ya Zamalamulo, anandiuza kuti: “Ukalimbikira nkhondoyi, udzapambana. Ukagonja, ndiye kuti walephera. N’zimene tinaphunzira kumsasa wachibalo.”a Langizo limenelo linandithandiza kusunga lonjezo langa lotumikira Mulungu.

Chiletso ndi Kumangidwanso

Mu July 1950, ndinaikidwa kutumikira monga woyang’anira woyendayenda. Komabe, pa August 30, apolisi analanda malo athu ku Magdeburg, ndipo ntchito yathu yolalikira inaletsedwa. Ndiye ntchito yanga inasintha. Ineyo ndi Paul Herschberger tinapatsidwa ntchito yogwira ndi mipingo pafupifupi 50, tikumakhala masiku aŵiri kapena atatu pampingo uliwonse ndi kuthandiza abale kutsatira dongosolo labwino pochita utumiki wawo chiletso chili m’kati. Miyezi isanu ndi umodzi yotsatira, ndinazemba apolisi kasanu ndi kamodzi kuti asandigwire!

Mpingo wina unaloŵeredwa ndi wina wake amene anakatineneza kwa a Stasi, Bungwe la Chitetezo cha Boma. Chotero, mu July 1951, amuna asanu ndi mfuti m’manja anandigwira ineyo ndi Paul mumsewu. Pokumbukira za m’mbuyo, tinaona kuti sitinalidalire kwambiri gulu la Yehova. Abale achikulire anali atatiuza kuti tisamayendere limodzi. Kudzidalira mopambanitsa kunatitayitsa ufulu wathu! Komanso, sitinakambirane pasadakhale zonena ngati atatigwira.

Ndili ndekhandekha m’selo muja, ndinachonderera Yehova ndikulira kuti andithandize kusapereka abale anga kapena kulola chikhulupiriro changa kugonja. Nditagona tulo, ndinadzuka mwadzidzidzi chifukwa cha kumva mawu a mnzanga Paul. Pamwamba pa chipinda changa panali chipinda chimene a Stasi anali kum’funsiramo. Popeza kuti kunali kotentha usikuwo, khomo la pakhonde linali lotsegula, ndipo ndinkamva pang’ono zonse. Kenako pondifunsa, ndinapereka mayankho omwe iye anapereka, zimene zinadabwitsa apolisiwo. Ndinakumbukirabe lemba lija ankakonda amayi lakuti, “Undiitane tsiku la chisautso: ndidzakulanditsa,” ndipo zinandilimbikitsa kwambiri.​—Salmo 50:15.

Atamaliza kutifunsa, ineyo ndi Paul tinakhala miyezi isanu m’ndende ya a Stasi ku Halle kenako ku Magdeburg kuyembekezera kuti mlandu wathu uzengedwe. Ndili ku Magdeburg, nthaŵi zina ndinkaona nyumba yathu ya nthambi yotsekedwa ija. Ndinalakalaka kwambiri kuti bwenzi ndikugwira ntchito kumeneko m’malo mokhala m’ndende! Mu February 1952, tinauzidwa chilango chathu: “zaka 10 m’ndende komanso zaka 20 zopanda ufulu woyenera nzika.”

Kusunga Chikhulupiriro m’Ndende

Mboni za Yehova zimene zinalamulidwa kukhala zaka zosachepera khumi nthaŵi zina zinkavala chizindikiro chapadera chozidziŵikitsa m’ndendemo. Kansalu kofiira kanasokeredwa kumwendo umodzi wa talauza komanso kudzanja limodzi la jakete. Ndiponso, kachidutswa kofiira ka khadibolodi komanso kozungulira kanamatidwa kunja kwa chitseko cha selo kuchenjeza alonda kuti tinali apandu oopsa.

Kwenikweni, akuluakulu a boma ankatiyesa apandu oipitsitsa. Sankatilola kukhala ndi Baibulo chifukwa, malinga ndi kufotokoza kwa mlonda wina: “Ngati wina wa Mboni za Yehova wagwira Baibulo, amakhala ngati mpandu amene wanyamula mfuti.” Pofuna kukhala ndi tizidutswa ta Baibulo, tinkaŵerenga mabuku a wolemba nkhani wa ku Russia, Leo Tolstoy, amene nthaŵi zambiri ankagwira malemba m’Baibulo polemba mabuku ake. Tinaloŵeza malemba a m’Baibulo amenewa pamtima.

Asanandigwire mu 1951, ndinapalana chibwenzi ndi Elsa Riemer. Ankandichezera nthaŵi zambiri ndili m’ndende ndipo ankanditumizira phukusi la chakudya kamodzi pamwezi. Komanso m’mapukusiwo ankabisamo chakudya chauzimu. Nthaŵi ina, anaika nkhani za mu Nsanja ya Olonda m’masoseji ena. Kaŵirikaŵiri alonda anali kucheka masoseji kuwatsegula kuti aone ngati anabisamo zinthu m’kati, koma tsikulo phukusilo linafika kutatsala nthaŵi yochepa kuti aweruke, choncho sanafufuze.

Nthaŵiyo n’kuti ineyo ndi Karl Heinz Kleber tikukhalira limodzi m’kachipinda kakang’ono ndi akaidi ena atatu osakhala Mboni. Kodi tikanatani kuti tiŵerenge Nsanja ya Olonda imeneyo popanda kuonedwa? Tinachita ngati tikuŵerenga buku koma m’kati mwakemo titabisamo nkhani za mu Nsanja ya Olonda. Tinapatsiranso Mboni zinzathu m’ndendemo chakudya chauzimu chofunika kwambiri chimenecho.

Tili m’ndendemo, tinapezeraponso mpata wouza ena za Ufumu wa Mulungu. Ndinasangalala kuona mmodzi wa akaidi anzanga atakhala wokhulupirira chifukwa cha zimenezo.​—Mateyu 24:14.

Kuyambiranso Utumiki Wanthaŵi Zonse

Pa April 1, 1957, nditakhala pafupifupi zaka zisanu ndi chimodzi m’ndende, anandimasula. Pasanapite milungu iŵiri, ndinakwatira Elsa. A Stasi atamva za kumasulidwa kwanga, anayesa kupeza chifukwa choti andibwezere kundende. Kuti ndipeŵe zimenezo, ine ndi Elsa tinadutsa malire kupita kukakhala ku West Berlin.

Titafika ku West Berlin, Sosaite inafuna kudziŵa zolinga zathu. Tinafotokoza kuti mmodzi wa ife azichita upainiya pamene wina azigwira ntchito yakuthupi.

“Kodi simungakonde kukhala apainiya aŵirinu?” anatifunsa.

“Ngati zimenezo zili zotheka,” tinayankha, “titha kuyamba nthaŵi yomwe ino.”

Choncho tinkapatsidwa tindalama pang’ono mwezi uliwonse togulira zofunikira, ndipo tinayamba kutumikira monga apainiya apadera mu 1958. Tinasangalala kwabasi kuona anthu amene tinaphunzira nawo Baibulo akusintha miyoyo yawo kukhala atumiki a Yehova! Zaka khumi zotsatira zimene tinali mu utumiki wa upainiya wapadera zinatiphunzitsa kugwira ntchito limodzi mogwirizana monga mwamuna ndi mkazi wake. Elsa nthaŵi zonse ankandithandiza, ngakhale pamene ndinkakonza galimoto. Tinkaŵerenga, kuphunzira, ndi kupempherera pamodzi.

Mu 1969, tinapatsidwa ntchito yoyendayenda, kuchezera mpingo wosiyana mlungu uliwonse kutumikira abale pa zosoŵa zawo. Josef Barth, amene anali wozoloŵera kwambiri ntchito yoyendayenda, anandilangiza kuti: “Ngati ukufuna kuti ntchito yako iyende bwino, ungokhala monga mbale kwa abale.” Ndinayesa kutsatira nzeru imeneyo. Choncho, unansi wathu ndi Mboni zinzathu unali wabwino kwambiri komanso wogwirizana, zimene zinandipeputsira zinthu popereka uphungu utafunikira.

Mu 1972, Elsa anam’peza ndi kansa ndipo anam’panga opaleshoni. Pambuyo pake, anadwalanso nyamakazi. Ngakhale kuti anali kumva kupweteka, anali kutsagana nanebe mlungu uliwonse potumikira mipingo, ndipo amayesetsa kugwira ntchito ndi alongo mu utumiki.

Zosoŵa Zosinthitsa Zinthu

Mu 1984 apongozi anga anafunikira chisamaliro chanthaŵi zonse, choncho tinasiya ntchito yoyendayenda kuti tikathandize kuwasamalira kufikira atamwalira patapita zaka zinayi. (1 Timoteo 5:8) Kenako, mu 1989, Elsa anadwala kwakayakaya. Bwino lake n’lakuti wachirirapo, koma ndiyenera kuchita ntchito zake zonse za panyumba. Ndidakaphunzira kukhala ndi munthu amene amamvabe kupweteka nthaŵi zonse. Koma mosasamala kanthu za kupsinjika maganizo, sitinataye chikondi chathu cha zinthu zauzimu.

Lero ndikuthokoza kuti tidakali pampambo wa apainiya. Komabe, tafika pozindikira kuti chofunika kwambiri si udindo umene tili nawo kapenanso kuchuluka kwa ntchito zathu, koma kukhalabe okhulupirika. Tikufuna kutumikira Yehova, Mulungu wathu, osati zaka zochepa chabe, koma mpaka kalekale. Zimene zachitika pamoyo wathu zatiphunzitsa zambiri kaamba ka m’tsogolo. Ndipo Yehova watipatsa mphamvu yoti tim’tumikire nayo ngakhale pamene zinthu zafika povutitsitsa.​—Afilipi 4:13.

[Mawu a M’munsi]

a Nkhani ya Ernst Wauer inali mu Nsanja ya Olonda ya August 1, 1991, masamba 25 mpaka 29.

[Chithunzi patsamba 23]

Ndinali m’ndende kunoko ku Magdeburg

[Mawu a Chithunzi]

Gedenkstätte Moritzplatz Magdeburg für die Opfer politischer Gewalt; Foto: Fredi Fröschki, Magdeburg

[Chithunzi patsamba 23]

Pamene tinakwatirana mu 1957

[Chithunzi patsamba 23]

Limodzi ndi Elsa lero

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena