Kukonda a “pa Banja la Chikhulupiriro”
AKRISTU enieni ndi omangidwa pamodzi monga banja. Zoonadi, kuyambira m’zaka za zana loyamba C.E., akhala akuitanana kuti “mbale” ndi “mlongo.” (Marko 3:31-35; Filemoni 1, 2) Aŵa si mawu wamba; amalongosola mmene olambira a Mulungu amaonerana. (Yerekezerani ndi 1 Yohane 4:7, 8.) Yesu anati: “Mwa ichi adzazindikira onse kuti muli akuphunzira anga, ngati muli nacho chikondano wina ndi mnzake.”—Yohane 13:35.
Chikondi choterocho chinaoneka ku Chile mu July 1997 pamene pambuyo pakuti kunali chilala kwa nthaŵi yaitali, kunagwa mvula yambiri ndipo madzi anasefukira. Mwadzidzidzi, anthu ambiri analibe chakudya, zovala, ndi zinthu zina. Kukagwa tsoka, Mboni za Yehova zimayesetsa kutsatira zimene Paulo analangiza Agalatiya kuti: “Chifukwa chake, monga tili nayo nyengo, tichitire onse chokoma, koma makamaka iwo a pa banja la chikhulupiriro.”—Agalatiya 6:10.
Motero, mwamsangamsanga Mboni za Yehova zinakonzeka kuti zichitepo kanthu. Chakudya, zovala ndi zinthu zina zotero zinasonkhanitsidwa, kusankhidwa, kulongedzedwa, ndiyeno ndi kutumizidwa kudera komwe kunagwa tsokako. Ana anapereka ngakhale zidole! Mlongo wina anadabwa ataona Nyumba ya Ufumu itadzaza ndi zinthu zachithandizo. “Ndinazizwa, sindinadziŵe kuti kaya ndiseke kapena ndilire,” iye anatero. “Zinalidi zimene tinkazifuna.”
Ndiyeno, mwadzidzidzi mbali ina ya dera lomwe munasefukira madzilo munachita chivomezi. Nyumba zambiri zinawonongeka. Kuti athe kukonza zimenezi, anapanga makomiti achithandizo enanso. Makomiti Omanga Achigawo, amene makamaka amamanga nyumba zosonkhaniramo za Mboni za Yehova, analoŵapo ndi kuthandiza. Zotsatira zake? Nyumba zabwino—zojambulidwa ndi kumangidwa ndi abale—zinaperekedwa kwa anthu amene nyumba zawo zinawonongedwa. Ngakhale kuti nyumbazi sizinali zazikulu kwambiri, zinali kusiyana kwambiri ndi zimene mabungwe ena opereka chithandizo anali kumanga pangongole, zimene zinali zopanda simenti ndi mawindo komanso zinali zosapenta.
Abale ena odzathandiza anachokera madera akutali. Tcheyamani wa Komiti Yomanga Yachigawo inayake anayendayenda kwambiri m’deralo kwa masiku aŵiri otsatizana—mosasamala kanthu kuti amayenda panjinga ya anthu olemala. Mbale wina wosaona anagwira ntchito zolimba. Anali kunyamula matabwa ndi kukapatsira akalipentala amene anali kuwadula m’masaizi ofunikira. Mbale wina wogontha anali kutenga matabwawo ndi kukapereka kumene anali kuwagwiritsa ntchito.
Ambiri amene anali kuonerera zimene zinali kuchitikazo anachita chidwi ndi chithandizo chimene abale anapereka. M’tauni ina apolisi anaimika galimoto yawo pafupi ndi nyumba ya mlongo wina imene inali kukonzedwa. Apolisiwo ankafunitsitsa kudziŵa chomwe chinali kuchitika. Mmodzi wa iwo anafunsa mbale wina kuti: “Kodi anthu amene akugwira ntchito mosangalala kwambiriŵa ndani, ndipo amalipidwa zingati?” Mbaleyo anafotokoza kuti onsewo anali kugwira ntchito modzifunira. Mmodzi wa maofesalawo anati iye anali kupereka chakhumi mwezi uliwonse ku tchalitchi kwawo, koma apasitala awo sanadzamuonepo chichitikire chivomezicho! Mmaŵa wake mlongoyo analandira telefoni kuchokera kwa mkulu wa apolisi. Iyenso anawaona anthu amene anali kugwira ntchitowo. Anati anachita chidwi kwambiri ndi mzimu wofunitsitsa wa anthu amene anali kugwira ntchitowo kwakuti anaganiza zogwira nawo!
Ndithudi, ntchito yachithandizoyo ku Chile inali chochitika chosangalatsa kwa antchito odzifunirawo ndiponso umboni wabwino kwambiri kwa anthu amene anaona izi zikuchitika.