Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 6/15 tsamba 4-7
  • Kuwononga Zinthu Kungathetsedwe

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kuwononga Zinthu Kungathetsedwe
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Zochititsa Zina Zikuluzikulu za Kuwononga Zinthu
  • Chitsogozo Chanzeru kwa Achinyamata
  • Chinthu China Chabwino Kusiyana ndi Kutsutsa
  • Dziko Latsopano Lopanda Kuwononga Zinthu Ndi Lotheka
  • Kuwononga Zinthu—Chifukwa Chiyani?
    Nsanja ya Olonda—1999
  • Anthu Akuvutika Ndi Chidani Padziko Lonse
    Nsanja ya Olonda Yolengeza Ufumu wa Yehova (Yogawira)—2022
  • Kuthandiza Achinyamata Kusiya Kupulupudza
    Galamukani!—2000
  • Mtsogolo Mosungika Mmene Mungamupezere
    M’tsogolo Mosungika—M’mene Mungamupezere
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—1999
w99 6/15 tsamba 4-7

Kuwononga Zinthu Kungathetsedwe

“NTHAŴI zonse achinyamata akamawononga kapena kuipitsa zinthu zimatengedwa kuti sakupereka ulemu ndiponso sakugwirizana ndi anthu akuluakulu ndi miyezo yawo,” analongosola motero olemba buku Jane Norman ndi Myron W. Harris. Pamene kuli kwakuti achinyamata ambiri amakhulupirira kuti palibe chimene chingachitidwe kuti mkhalidwewu usinthe, “m’modzi mwa achinyamata atatu amaganiza kuti achinyamata angachepetse kuwononga zinthu ngati makolo atamasamalira ana awo kwambiri, ndiponso ngati achinyamata angamakhale osanyong’onyeka kwambiri,” anatero alembiwo. Pamene kuli kwakuti kupatsa achinyamata zochita ndiponso kuyang’aniridwa bwino ndi makolo kungachepetse kuwononga zinthu, kodi zimenezi mwa izo zokha zingathetse zoyambitsa zake zenizeni?

Achinyamata ambiri savuta pamene ali okha, koma atakhala pagulu kapena pamene alipo aŵiri, amafuna kuti anthu adziŵe kuti alipo, amachita zinthu zauchitsiru ndi zonyansa. Ndi zimene Nelson anali kuchita. Kaŵirikaŵiri atamwa mankhwala osokoneza bongo kapena moŵa anali kuwononga zinthu kuti asonyeze kuti wakwiya kapena kuti sakukhutira ndi zinthu zina. José, atasonkhezeredwa ndi maulaliki m’Tchalitchi cha Katolika onena za kugaŵanso malo ndi ufulu wa antchito, anaona kuti anafunika kunyanyala nawo ntchito ndi kuwononga nawo zinthu ngati njira yotsutsira. Komabe, onse aŵiri Nelson ndi José anapeza chinthu china chabwino kwambiri kupambana zipolowe ndi kuwononga zinthu.

Zochititsa Zina Zikuluzikulu za Kuwononga Zinthu

Tatiyeni tione bwinobwino zifukwa zimene zimachititsa achinyamata ena kuwononga zinthu. Achinyamata ambiri amasokonezeka maganizo ndipo “amati dzikoli ndi losokonezeka, malo oyaluka, odzala ndi anthu oyaluka.” Komabe, ndipo mosiyana ndi zimene ena amaganiza, lipoti lina linati: “Achinyamata amadera nkhaŵa za tsogolo lawo. Amadera nkhaŵa kwambiri kusiyana ndi mmene akuluakulu amaganizira.” Mosadziŵa kaya modziŵa, wachinyamata amene wawononga chinthu angatero posonyeza kuti ali wokhumudwa kwambiri, ali ndi mavuto osathetsedwa, kapena kuti zofuna zake sizinakwaniritsidwe. Malinga ndi kafukufuku amene watchulidwa pachiyambi pa nkhani ino, “palibe ndi mmodzi yemwe mwa ofunsidwawo amene anachirikiza kapena kunena kuti kuwononga zinthu ndi kwabwino, ngakhale amene anazichitapo sanazichirikize.”

Mwina ndi mwakamodzikamodzi kuti wachinyamata amve ena akumuyamikira kapena kumulimbikitsa. Popeza kuti mowonjezerekawonjezereka maphunziro akukhala ofunika kwambiri ndipo ntchito zambiri zimafunika kuzidziŵa bwino kwambiri kapenanso zimafuna umisiri weniweni, iye angamve kuti akunyazitsidwa. Ndiponso, makolo, aphunzitsi, ngakhale mabwenzi angakhale osuliza kwambiri ndi ofuna zambiri, akumagogomezera zimene wachinyamatayo amachita osati mmene iye alili monga munthu. Ambiri amapanduka kapena amawononga zinthu chabe chifukwa chakuti akhumudwa ndi mmene alili. Kodi chikondi ndi chisamaliro cha makolo sichingachepetse kwambiri kuvutika koteroko?

Mwina munaonapo kuti pamene kuli kwakuti akuluakulu aboma ena amaoneka kuti anasiya kuyesa kuletsa kulembalemba mawu pazipupa ndiponso zochita zina zosonyeza kupulupudza, kaŵirikaŵiri anthu okhudzidwa amayembekezera kuti aphunzitsi ndi oyang’anira sukulu aziletsa kuwonongedwa kwa zinthu. Ponena za kukhwimitsa malamulo, The World Book Encyclopedia imati: “Munthu amalipira faindi kapena kupita kundende chifukwa chowononga zinthu. M’mayiko ena, madera ena ali ndi malamulo amene amaimba mlandu makolo ana awo akawononga zinthu. Koma anthu ambiri salangidwa chifukwa chowononga zinthu. M’zochitika zoterozo ndi kovuta kukhwimitsa malamulo, ndipo zinthu zambiri zimene zimawonongedwa mtengo wa chinthu chimodzi si waukulu kwambiri kuti nkhaniyo ingafunike kupita kukhothi.” Lipoti lina linasonyeza kuti 3 peresenti chabe ya olakwa ndi amene anagwidwapo.

Mwinamwake inu mungavomereze kuti njira yabwino kwambiri yothanirana ndi choyambitsa kupulupudza ndi yakuti makolo azisamalira ana awo mokwanira. Koma pamene moyo wa banja uloŵa pansi, anthu amavutika. Polofesa Ana Luisa Vieira de Mattos, wa pa Yunivesite ya São Paulo, ku Brazil, ananena kuti zifukwa zina zimene pamakhalira mavuto ndi achinyamata ndi “makolo osayang’anira kwenikweni ana awo, kusoŵeka kwa malamulo, kusalankhulana, kulekerera, kusiyana maganizo kapena kukondera.”

M’masiku athu ano ife taonadi kukwaniritsidwa kwa mawu a Yesu akuti: “Chifukwa cha kuchuluka kwa kusayeruzika, chikondano cha anthu aunyinji chidzazirala.” (Mateyu 24:12) Ndipo ndani angakane kuti mawu olembedwa pa 2 Timoteo 3:1-4 ndi oona? Mtumwi Paulo analemba kuti: “Zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthaŵi zoŵaŵitsa. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudyerekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.” Zoonadi ndi zakuti, kungokhala ndi anthu a makhalidwe ameneŵa kumawonjezera kupulupudza. Komabe sitiyenera kusiya. Mokulira anthu alephera kuthetsa kuwononga zinthu, koma tingathe kupeza anthu amene akhala okhoza kusintha moyo wawo, tsopano salinso ndi makhalidwe oipa ndiponso si osimbwa. Kwa iwowo kuwononga zinthu kunatha.

Chitsogozo Chanzeru kwa Achinyamata

Kodi ndi chiyani chimene chathandiza anthu amene ankawononga zinthu pamodzinso ndi anthu ena kusintha umunthu wawo? Ngakhale kuti kwa aphunzitsi ndi makolo ena zingakhale zovuta kukhulupirira, Baibulo lili ndi chitsogozo chapamwamba kwambiri ndiponso chamakono. Mwa kuchitsatira, amene kale anali anthu owononga zinthu asonkhezeredwa kumvera lamulo la Mulungu losapita m’mbali ili: “Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa.” (Eksodo 23:2) Ena akopeka ndi choonadi cha Mawu a Mulungu pa zikhulupiriro ndi ziphunzitso zimene n’kale lonse sanali kuzimvetsa, ndipo zimene aphunzira zawathandiza kuwongolera. Lingalirani za José, mnyamata wa ku São Paulo. Iye analeredwa akukhulupirira kugwiritsa ntchito mafano polambira. Pamene anaphunzira kuti Mulungu ali ndi dzina, Yehova, ndi kuti savomereza kulambira mafano, José anasintha kuti azichita zimene zimasangalatsa Mulungu.​—Eksodo 20:4, 5; Salmo 83:18; 1 Yohane 5:21; Chivumbulutso 4:11.

M’malo mokhumudwa ndi chochitika chilichonse m’gulu lochita zachiwawa ndi kumanyanyala ntchito, Nelson anapeza chiyembekezo chenicheni cha m’tsogolo, ndipo izi zamupumuza kwambiri. Iye anati: “M’malo monyanyalidwa ndi makolo anga chifukwa chogwirizana ndi anthu amakhalidwe oipa ndiponso moyo wanga wokonda mankhwala osokoneza bongo, tsopano ine ndine amene amandilemekeza kwambiri panyumba. Nthaŵi zambiri bambo anga amandipempha kuti ndilangize azikulu anga. Kuchokera pamene ndinayamba kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, ndili wachimwemwe chifukwa tsopano moyo wanga uli ndi chifuno.” Ndipo kwa wachinyamata wam’tauni monga Marco​—wozoloŵera kukhala m’malo achiwawa​—kudziŵa kuti Ufumu wa Mulungu udzapanga dziko lapansili kukhala paradaiso kwakhaladi kotonthoza kwambiri.​—Chivumbulutso 21:3, 4.

Talingaliraninso za amene kale anali m’gulu laupandu, wandewu, ndi wowononga zinthu. Valter, yemwe anali mwana wamasiye wovutika kwambiri, anachita chidwi atadziŵa kuti Mulungu ali ndi anthu ake pakati pa dongosolo losalungama ndi loipali. Iwo amayesetsa kugwiritsa ntchito malamulo a Baibulo m’miyoyo yawo, ali achifundo, amalingalira ena, ndipo ndi okoma mtima. Valter anati: “Mogwirizanadi ndi lonjezo la Yesu, ine tsopano ndili m’banja lalikulu, ndili ndi ‘abale ndi alongo ndi amayi ndi atate.’ Ponena za m’tsogolo, ndikuyembekezera nthaŵi imene anthu adzakhala osangalala ndi ogwirizana m’boma lolungama la Mulungu.”​—Marko 10:29, 30; Salmo 37:10, 11, 29.

Chinthu China Chabwino Kusiyana ndi Kutsutsa

Kuwonjezera pa kulingalira ndi kukonda anzawo, anthu aŵa amene kale anali owononga zinthu aphunzira ‘kudana nacho choipa.’ (Salmo 97:10; Mateyu 7:12) Nanga inuyo bwanji? Ngakhale ngati ndinu chabe munthu amene amavutika ndi zochita zowononga zinthu zomwe ndi zofala kwambiri, kuphunzira Mawu a Mulungu kudzakuthandizani kuona Yehova kuti ali weniweni, Atate wakumwamba wachikondi amene amafuna kukusamalirani. (1 Petro 5:6, 7) Mulungu angakuthandizeni kukula mwauzimu, mosasamala kanthu za kufooka kwanu kapena umphaŵi. Zimenezi zokha ndi zosangalatsa kwambiri!

Ndithudi, Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu, akufuna kuti anthu a mitundu yonse akhale ndi mwayi wophunzira choonadi cha Baibulo. Mawu a Mulungu angathandize anthu kwambiri tsopano lino kuposa chabe kuwasiyitsa kukhala anthu owononga zinthu. Angawachititse kupitirizabe kugwiritsa ntchito malamulo a Mulungu. Zotsatira zake ndi zakuti iwo amakhala amodzi a gulu la ubale wa padziko lonse limene limadziŵika ndi ukhondo ndi makhalidwe abwino, mpingo wa padziko lonse wa Mboni za Yehova. Mogwirizana ndi Aefeso 4:24, Akristu oona mtima ameneŵa ‘avala munthu watsopano, amene analengedwa monga mwa Mulungu, m’chilungamo, ndi m’chiyero cha choonadi.’ Posachedwa anthu otereŵa ndiwo adzakhale padziko lapansi chifukwa ndi okhaŵa amene adzapulumuke ndi kukhala ndi moyo kosatha.​—Yerekezerani ndi Luka 23:43.

Dziko Latsopano Lopanda Kuwononga Zinthu Ndi Lotheka

Kodi mumakhulupirira kuti kuwononga zinthu kukhozadi kuthetsedwa? Ngati ndi tero, kodi kusintha kofunika kumeneku kudzachitika bwanji? Ufumu wa Mulungu posachedwapa udzachotsa dongosolo loipali. Awo okhala m’dzikolo azidzafunsidwa ngati aswa mwadala malamulo olungama a Mulungu. (Yerekezerani ndi Yesaya 24:5, 6.) Pamene kuli kwakuti “olakwa adzawonongeka pamodzi,” aja amene amakonda chilungamo adzalanditsidwa. ‘Yehova adzawathandiza, nadzawalanditsa: adzawalanditsa kwa oipa nadzawapulumutsa, chifukwa kuti anamukhulupirira Iye.’​—Salmo 37:38-40.

Ndithudi, zifukwa zimene zimapangitsa anthu kuwononga zinthu zidzachotsedweratu. Zidzakhalanso choncho ndi upandu, kuponderezana, kuvutika, ndi kuipa konse. M’malo mwake, moyo m’dziko latsopano udzakhala wamtendere, wachilungamo chenicheni, wabata, ndi wosungika. Yesaya 32:18 amalongosola zimene moonadi zidzachitika: “Anthu anga adzakhala m’malo a mtendere, ndi mokhala mokhulupirika ndi mopuma mwa phe.” Inde, m’paradaiso wa padziko lonse wokongola mudzakhala anthu amene amakonda ndiponso amene amalingalira ena.

Pamodzi ndi anthu ena mamiliyoni, anthu amene kale anali okonda kuwononga zinthu akusangalala ndi unansi wathithithi ndi Yehova Mulungu. Iwo tsopano sawononganso zinthu. Kodi inunso mudzalola kuti Mawu a Mulungu akutsogolereni ku moyo m’dziko lake latsopano? Bwanji osatsanzira wamasalmo wakale amene analemba chilengezo cha Yehova chakuti: “Ine ndidzakulangiza ndi kuphunzitsa iwe za njira ukayendayo; ndidzakupangira ndi diso langa lakuyang’ana iwe.”​—Salmo 32:8.

[Chithunzi patsamba 7]

Chikondi ndi chisamaliro cha makolo zimateteza achinyamata

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena