Kuwononga Zinthu—Chifukwa Chiyani?
“NDILIBE mawu.” Mawu ameneŵa analembedwa m’zilembo zikuluzikulu pa khoma lina limene linali litangopakidwa penti kumene m’dera lina lokongola ku São Paulo. Mungaganize kuti ndi kuwononga malo kosavuta. Ndipotu kulemba mawu pazipupa ndi mtundu umodzi chabe wa kuwononga zinthu.
Talingalirani kuti anthu okonda kuwononga zinthu mwadala aswa galimoto yanu yatsopano. Kapena mwina mungaone kuti nyumba ya boma—imene imathandiza anthu ambiri—yaipitsidwa kapena kuwonongedwa ndi anthu owononga zinthu. N’chifukwa chiyani? Indedi, n’chifukwa chiyani? Kodi munaganizapo kuti ndi chifukwa chiyani anthu ochuluka amawononga zinthu? M’malo ambiri, anthu okonda kuwononga zinthu amaoneka kuti amasangalala ndi kuipitsa kapena kuwononga malo oimbiramo telefoni. Kaŵirikaŵiri amawononga zoyendera za anthu onse, monga sitima kapena mabasi. Zikuoneka kuti anthu owononga zinthu sasamala chilichonse. Koma kodi ndi chiyani chimene chimachititsa anthu ambiri kuwononga zinthu kumene timaona kapena kuvutika nako?
Marco,a mnyamata wa ku Rio de Janeiro, anakhumudwa timu yake itagonjetsedwa pa maseŵera a mpira—anakhumudwa kwambiri kwakuti anayamba kugenda miyala basi imene munakwera anthu ochemerera timu imene inapambanayo. Kapenanso ganizirani za Claus. Pamene sanakhoze bwino kusukulu, anakwiya kwambiri kwakuti anaswa mawindo ndi miyala. Koma “chisangalalocho” chinatha pamene bambo ake anauzidwa kuti alipire zimene anawonongazo. Mnyamata wina, Erwin, anali kuphunzira kusukulu uku akugwira ntchito. Iyeyo pamodzi ndi mabwenzi ake anali kuonedwa kuti anali anyamata abwino. Komatu, iwo panthaŵi yawo yocheza anali kuwononga zinthu za m’dera limene anali kukhala. Makolo ake a Erwin sanali kuzidziŵa zimenezi. Valter anali mwana wa masiye amene sakanachitira mwina koma kumakhala m’misewu ya ku São Paulo. Anzake amene anali kukondana nawo kwambiri anali kagulu ka anthu owononga zinthu, ndipo iye anali kuchita nawo zimene iwo anali kuchita ndiponso anaphunzira maluso omenyera. Zitsanzo zimenezi zikusonyeza kuti pali anthu amene amawononga ndi kuipitsa zinthu, ndiponso kuti zimene zimawachititsa, kapena malingaliro awo, ndi zosiyanasiyana.
“Kuwononga zinthu kungakhale kubwezera zinazake kapena ingakhale njira yosonyezera malingaliro ako andale. Nthaŵi zina achinyamata ndi akuluakulu omwe amachita zimenezi pofuna chabe ‘kusangalala,’” imatero The World Book Encyclopedia. Komabe, m’malo mongokhala zosangalatsa achinyamata, kuwononga zinthu kungakhale kowononga kwabasi, mwinanso kwakupha. Kagulu kena ka achinyamata kanali kufuna “kusangalala,” ndipo pamene anaona mwamuna wina akugona, anamuthira mafuta ogwira moto msanga ndi kumuyatsa. Mwamunayo, Mmwenye, anakafera kuchipatala. Lipoti lina linati, “anyamatawo anati anali kuganiza kuti palibe amene zikanamukhudza chifukwa anthu opemphapempha ambirimbiri anali atawotchedwa mumsewu, ndipo palibe chimene chinachitika.” Kaya kuwononga zinthu kukuoneka kukhala kosavulaza kapena ayi, mtengo wake, ndalama kapena mwa malingaliro, ndi waukulu kwambiri. Motero, kodi ndi chiyani chimene chingachepetse kapena kuletsa kuwononga zinthu?
Ndani Angaletse Kuwononga Zinthu?
Kodi apolisi ndi masukulu angateteze zinthu kuti zisamawonongedwe? Vuto ndi lakuti akuluakulu aboma amatanganidwa kwambiri ndi milandu ikuluikulu, monga ngati kuzembetsa mankhwala osokoneza bongo kapena nkhani za kuphana, m’malo mwa milandu yopanda “munthu wovulazidwa.” Mkulu wa apolisi wina anati, pamene mwana apezeka m’mavuto, kaŵirikaŵiri makolo ake “amaimba mlandu ana amene amaseŵera nawo, kapena sukulu, kapena apolisi chifukwa chomugwira.” Maphunziro ndi kukhwimitsa malamulo zingachepetse kuwononga zinthu; koma bwanji ngati makolo sangasinthe maganizo awo? Mkulu wina wa khoti lozenga milandu achinyamata anati: “Ndi chifukwa cha kunyong’onyeka ndiponso kukhala ndi mpata. [Ana amakhala ali] kunja usiku kwambiri, ndipo amakhala alibe chochita. Ndipo mwinamwake sayang’aniridwa—apo ayi sakanakhala ali kunja.”
Ngakhale kuti kuwononga zinthu ndi vuto lalikulu m’madera ambiri, talingalirani mmene zinthu zingasinthire. Achinyamata okonda kuwononga zinthu amene atchulidwa poyambirirawo anasintha; iwo tsopano amapeŵeratu khalidwe lililonse lomwe anthu sasangalala nalo. Kodi ndi chiyani chimene chinachititsa ana omwe kale anali opulupudza ameneŵa kusintha moyo wawo? Komanso, kodi mungadabwe ngati kuwononga zinthu kutathetsedwa osati chabe kuchepetsedwa? Chonde ŵerengani nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Tasintha mayina.