Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w99 7/15 tsamba 26-28
  • Ku Namibia Kuli Miyala Yamtengo Wapatali Yamoyo!

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Ku Namibia Kuli Miyala Yamtengo Wapatali Yamoyo!
  • Nsanja ya Olonda—1999
  • Timitu
  • Chiyambi chokumba Migodi Yauzimu
  • Antchito Anthaŵi Zonse Afika
  • Kusalalitsa Miyala Yamtengo Wapatali
  • Antchito Akufunika pa Migodi Yauzimu
Nsanja ya Olonda—1999
w99 7/15 tsamba 26-28

Ku Namibia Kuli Miyala Yamtengo Wapatali Yamoyo!

NAMIBIA ali ndi utali wa makilomita pafupifupi 1,500 m’mphepete mwa gombe la kumwera chakumadzulo kwa Afirika. M’gombe lonse la dzikoli muli miyulu yaikulu ya mchenga, mapiri amiyala, ndi zidikha zazikulu za mchenga. Ina mwa miyala yopezeka m’gombe la m’Namibia, ndi miyala yamtengo wapatali, yamitundu yosiyanasiyana. Ngakhalenso diamondi nthaŵi zina amapezeka kumeneko. Komabe dzikolo lili ndi chinthu china chamtengo wapatali zedi kuposa miyala imeneyi. Dziko la Namibia lili ndi miyala yamtengo wapatali koma yamoyo​—anthu amitundu yonse ya m’dzikolo.

Mbadwa zoyambirira za dziko la Namibia zinali kulankhula zinenero zosiyanasiyana zomwe zimapanga chilankhulo chotchedwa Chikhoisani. Chilankhulo chawo chimadziŵika ndi mmene zimamvekera akamatchula mawu. Ena mwa omwe amalankhula Chikhoisani lerolino, ndi anthu akhungu lakuda otchedwa Adamara, akhungu loyererapo, anthu afupiafupi otchedwa Anama, komanso alenje otchuka Abushimani. Mafuko ambiri a anthu akuda abwera kudzakhala mu Namibia m’zaka mazana apitawa. Ameneŵa akuphatikizidwa m’magulu amitundu ikuluikulu itatu: Aovambo (Mtundu waukulu mu Namibia), Aherero, ndi Akavango. Azungu anayamba kudzakhala mu Namibia cha m’zaka za zana la 19. Ambiri analoŵa m’dzikomo pambuyo potulukira miyala ya diamondi m’chipululu chamchenga.

Nzika za m’Namibia ndi zamtengo wapatali zedi chifukwa chakuti ali mbali ya mtundu wa anthu adziko lapansi umene Mulungu anaperekera Mwana wake, kuti atsegule njira ya ku moyo wosatha. (Yohane 3:16) Mazanamazana a anthu a m’Namibia, amafuko osiyanasiyana alandira kale uthenga wa chipulumutso. Ameneŵa angayerekezedwe ndi miyala yamtengo wapatali yamoyo chifukwa ali mbali ya “zofunika za amitundu onse” omwe tsopano akusonkhanitsidwira ku nyumba ya Yehova yolambirira.​—Hagai 2:7.

Chiyambi chokumba Migodi Yauzimu

Munali m’chaka cha 1928 pamene kukumba miyala yauzimu kunayamba m’Namibia. M’chaka chimenecho, nthambi ya South Africa ya Watch Tower Society inatumiza mabuku othandiza pophunzira Baibulo okwana 50,000 kwa anthu m’dziko lonselo. Chaka chotsatira, Mkristu wodzozedwa wamkazi wochokera ku South Africa wotchedwa Lenie Theron, anakayendera amene anasonyeza chidwi. M’miyezi inayi yokha, iye anazungulira dziko lonselo, ndipo anagaŵira mabuku oposa 6,000 m’Chiafilikana, m’Chingerezi, ndi m’Chijeremani. Ntchito yonseyi mwachionekere sanaigwire mwachabe.

Mwachitsanzo, talingalirani za Bernhard Baade, Mjeremani wogwira ntchito m’migodi. Mu 1929 analandira mazira kuchokera kwa mlimi wina yemwe anakulunga dzira lililonse m’pepala lochokera m’zofalitsa za Watch Tower. Bernhard anaŵerenga mwakhama tsamba lililonse, ngakhale kuti sanadziŵe yemwe analemba bukulo. Ndipo potsirizira pake anafika patsamba lakumapeto, pamene panalembedwa keyala ya ku Germany ya Watch Tower Society. Bernahard analembera Sosaite kuti amutumizire mabuku ena, ndipo anali munthu woyamba mu Namibia kulandira choonadi.

Antchito Anthaŵi Zonse Afika

Mu 1950, amishonale anayi ophunzitsidwa pa Sukulu ya Baibulo ya Gileadi ya Watchtower, anafika mu Namibia. Chiŵerengero cha amishonale chinakwera kufika pa asanu ndi atatu pomafika 1953. Ena mwa iwo anali Dick Waldron ndi mkazi wake Coralie ochokera ku Australia, omwe akutumikirabe kuno mokhulupirika. Olengeza Ufumu anthaŵi zonse ena ambiri ochokera ku South Africa ndi kumayiko akunja atenga nawonso mbali m’kukumba miyala yamtengo wapatali yauzimu mu Namibia. Amishonale ena, limodzinso ndi omaliza maphunziro a Sukulu Yophunzitsa Utumiki, atumizidwa ku Namibia.

Chinthu china chimene chathandizira kukula kwauzimu mu Namibia ndi kumasulira ndi kufalitsa mabuku othandiza pophunzira Baibulo m’zinenero zikuluzikulu, monga Chiherero, Chikwangali, Chikwanyama, Chinama/​Chidamara, ndi Chindonga. Chiyambire 1990, ofesi yomasulira ndi nyumba ya antchito odzifunira anthaŵi zonse zakhala zikugwira ntchito m’likulu la dzikolo, Windhoek. Karen Deppisch, yemwe watumikira limodzi ndi mwamuna wake monga alaliki anthaŵi zonse m’madera osiyanasiyana mu Namibia, anati: “Ambiri amadabwa pamene tiŵapatsa mabuku m’zinenero zawo, makamaka poona kuti ndi mabuku ochepa kwambiri amtundu wina uliwonse amene alembedwa m’chinenero chimenecho.”

Kusalalitsa Miyala Yamtengo Wapatali

Ina mwa miyala yeniyeni ya mu Namibia yasalalitsidwa ndi kayendedwe ka mafunde a madzi ndi mchenga kwa zaka zikwi zambiri zapitazo. Komabe, kusalalitsa kwachilengedwe koteroko sikumatulutsa miyala yamtengo wapatali yamoyo. Pamafunikira kulimbikira kwenikweni kuti anthu opanda ungwiro ‘avule, . . . umunthu wakale’ ndi kuvala umunthu watsopano wonga wa Kristu. (Aefeso 4:20-24) Mwachitsanzo, kulambira makolo amene anamwalira kalekale ndi mwambo wa chikhalidwe cha mafuko ambiri m’Namibia. Omwe samachita nawo mwambo wolambira makolo akale, nthaŵi zambiri amazunzidwa ndi am’banja lawo ndi mabwenzi awo. Pamene wina aphunzira kuchokera m’Baibulo kuti akufa “sadziwa kanthu bi,” zimawavuta kumvetsa. (Mlaliki 9:5) Motani?

Mboni Yachiherero ikulongosola: “Chinali chinthu chovuta kwambiri kuti ndikhale wokhulupirika pa choonadi. Ndinavomera kuphunzira Baibulo ndi Mboni za Yehova, koma zinanditengera nthaŵi kuti ndizichita zomwe ndinkaphunzirazo. Poyamba ndinayesa kuti ndione ngati sipakakhala vuto lina lililonse pamene ndileka kutsatira zikhulupiriro za miyambo yakale. Mwachitsanzo, ndinayamba kudutsa malo ena mu Namibia osaima kuti ndiike mwala pamanda kapena kuvula chipeŵa popereka ulemu kwa akufa. Pang’ono ndi pang’ono, ndinatsimikiza kuti palibe chomwe chingandichitikire ngati ndisiya kulambira makolo akale akufawo. Ndili wosangalala kwambiri, kuti Yehova wadalitsa kuyesetsa kwanga kuti ndithandize am’banja langa ndi okondwerera ena kuphunzira choonadi!”

Antchito Akufunika pa Migodi Yauzimu

Asanafike amishonale mu 1950, munali wofalitsa uthenga wabwino mmodzi yekha mu Namibia. Chiŵerengerocho chakula pang’ono ndi pang’ono kufika pa 995. Komabe, padakali ntchito yambiri. Kunena zoona, madera ena sanafoledwe m’pang’ono pomwe. Kodi inu muli wokonzeka kukatumikira kumene kuli kusoŵa kwakukulu kwa olengeza Ufumu akhama? Ndiyeno, chonde, wolokerani ku Namibia ndipo tithandizeni kupeza ndi kusalalitsa miyala yambiri yamtengo wapatali yauzimu.​—Yerekezani ndi Machitidwe 16:9.

[Mapu/​Zithunzi patsamba 26]

(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)

AFRICA

NAMIBIA

[Zithunzi]

Namibia ndi dziko la miyala yamtengo wapatali

[Mawu a Chithunzi]

Mapu: Mountain High Maps® Copyright © 1997 Digital Wisdom, Inc.; Diamonds: Courtesy Namdek Diamond Corporation

[Zithunzi patsamba 26]

Uthenga wabwino ukulalikidwa mu Namibia kwa anthu amitundu yonse

[Chithunzi patsamba 28]

Kodi mungakatumikire kumene kuli kusoŵa kwakukulu kwa olengeza Ufumu?

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena