Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • w10 3/1 tsamba 3-4
  • Kodi Baibulo Ndi Mawu a Mulungudi?

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Kodi Baibulo Ndi Mawu a Mulungudi?
  • Nsanja ya Olonda—2010
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • Ena Ayamba Kukayikira Baibulo
  • Baibulo Ndi Mawu Ouziridwadi ndi Mulungu
    Nsanja ya Olonda—2010
  • Kodi Baibulo ‘Linauziridwadi Ndi Mulungu’?
    Galamukani!—2017
  • Kuŵerengeranji Baibulo?
    Baibulo—Kodi Ndilo Mawu a Mulungu Kapena a Munthu?
  • Magwero Apadera a Nzeru Yapamwamba
    Kodi Moyo Uli ndi Chifuno?
Onani Zambiri
Nsanja ya Olonda—2010
w10 3/1 tsamba 3-4

Kodi Baibulo Ndi Mawu a Mulungudi?

“Malemba onse anawauzira ndi Mulungu, ndipo ndi opindulitsa pa kuphunzitsa, kudzudzula, kuwongola zinthu, kulangiza m’chilungamo, kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera mokwanira, wokonzeka bwino lomwe kuchita ntchito iliyonse yabwino.”​—2 TIMOTEYO 3:16, 17.

MAWU a mtumwi Paulo amenewa ndi okhudza mtima kwambiri ndipo akusonyeza kuti Baibulo ndi buku lothandiza kwabasi. Kwenikweni, Paulo ankanena za mbali ya Baibulo imene inalipo pa nthawiyo, yomwe nthawi zina anthu amangoitcha kuti Chipangano Chakale. Komabe mawu a Paulowa akugwiranso ntchito pa mabuku onse 66 amene ali m’Baibulo, kuphatikizapo mabuku amene analembedwa ndi ophunzira a Yesu okhulupirika m’nthawi ya atumwi.

Kodi inunso mumaona kuti Baibulo ndi lofunika kwambiri ngati mmene Paulo ankalionera? Kodi mumakhulupirira kuti amene analemba Baibulo anauziridwadi ndi Mulungu? Akhristu am’nthawi ya atumwi ankakhulupirira zimenezi monganso mmene amachitira Akhristu masiku ano. Mwachitsanzo, m’zaka za m’ma 1300, mtsogoleri wina wa chipembedzo wa ku England, dzina lake John Wycliffe, ankaona kuti Baibulo ndi “buku la choonadi chokhachokha.” Buku lina lomasulira mawu a m’Baibulo linathirira ndemanga pa mawu a Paulo ali pamwambawo. Bukuli linanena kuti mfundo yoti Mulungu “anauzira Baibulo ikutsimikizira kuti zonse zimene Baibulo limanena ndi zoona.”​—The New Bible Dictionary.

Ena Ayamba Kukayikira Baibulo

Komabe m’zaka zaposachedwapa, anthu ambiri asiya kukhulupirira kuti Baibulo ndi lothandizadi. Buku lina lofotokoza za zipembedzo zapadziko lonse linanena kuti, “Akhristu onse amavomerezabe ndi mawu chabe kuti Baibulo ndi buku lothandiza posankha zochita ndiponso pa nkhani ya chikhulupiriro.” Komabe zochita za Akhristuwa, sizigwirizana ndi mawu amenewa. Masiku ano, anthu ambiri amaona kuti Baibulo “ndi losathandiza chifukwa amaganiza kuti limangofotokoza maganizo a anthu.” Anthu amenewa amavomereza kuti amene analemba Baibulo anali anthu a chikhulupiriro chachikulu. Komabe amaonanso kuti olemba Baibulowo anali anthu basi, moti analemba zinthu zina zolakwika ndipo zinkawavuta kufotokoza mfundo zozama za choonadi chifukwa sankadziwa zinthu zambiri zimene tikudziwa masiku ano.

Kunena zoona, ndi anthu ochepa chabe masiku ano amene amayesetsa kuti maganizo awo ndiponso zochita zawo zikhale zogwirizana ndi mfundo za m’Baibulo. Mwachitsanzo, kodi simunamvepo anthu akunena kuti zimene Baibulo limanena pa nkhani ya makhalidwe abwino ndi zachikale ndipo n’zosathandiza? Abusa ambiri amangophunzitsa anthu mfundo ndiponso malamulo a m’Baibulo amene akuona kuti anthuwo angawakonde kapenanso amangopeweratu kutchula mfundo zimenezi poopa kuwakhumudwitsa. Ena amene amati ndi Akhristu satsatira ngakhale pang’ono zimene Baibulo limanena pa nkhani ya dama, chigololo, kusaona mtima, ndiponso uchidakwa.​—1 Akorinto 6:9, 10.

N’chifukwa chiyani amatero? Kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, Sir Charles Marston, yemwe ndi katswiri wa mbiri ya zinthu zakale zokumbidwa pansi, anapereka chifukwa chimodzi m’buku lake. Iye anati anthu ankafulumira “kukhulupirira mfundo zongopenekera za olemba mabuku a masiku amenewo” amene ankakayikira zoti Baibulo limanena zoona. (The Bible Is True) Kodi zimenezi n’zimenenso zikuchitika masiku ano? Kodi muyenera kukhulupirira maganizo ndiponso mfundo za akatswiri amene amakayikira Baibulo? Werengani zimene nkhani yotsatirayi ikunena..

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena