Zamkatimu
April 15, 2010
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA MILUNGU YA:
May 31, 2010–June 6, 2010
Achinyamata, Khalani ndi Mtima Wokonda Kwambiri Kutumikira Yehova
TSAMBA 3
NYIMBO ZOIMBA: 11, 41
June 7-13, 2010
Ntchito ya Mzimu Woyera Pokwaniritsa Cholinga cha Yehova
TSAMBA 7
NYIMBO ZOIMBA: 43, 19
June 14-20, 2010
TSAMBA 20
NYIMBO ZOIMBA: 29, 52
June 21-27, 2010
Kodi Mukutsatira Khristu ndi Mtima Wonse?
TSAMBA 24
NYIMBO ZOIMBA: 54, 17
Cholinga cha Nkhani Zophunzira
NKHANI YOPHUNZIRA 1 MASAMBA 3-7
Yehova akuuza achinyamata kuti azimvera, kuphunzira ndi kutsatira malangizo ake. Nkhaniyi ikufotokoza mmene kuwerenga Baibulo, kupemphera ndiponso khalidwe labwino zingathandizire achinyamata kulambira Yehova ndi mtima wonse.
NKHANI YOPHUNZIRA 2 MASAMBA 7-11
Tikudziwa kuti cholinga cha Yehova chidzakwaniritsidwa ndipo palibe chimene chingalepheretse. Nkhaniyi ikufotokoza ntchito ya mzimu woyera pokwaniritsa cholinga cha Yehova m’nthawi yakale, masiku ano komanso m’tsogolo.
NKHANI YOPHUNZIRA 3 MASAMBA 20-24
Pamene dziko la Satanali likuyandikira mapeto ake, timaona ndiponso kumva zinthu zimene zingasokoneze ubwenzi wathu ndi Mulungu. M’nkhani ino tikambirana zina mwa zinthu zimenezi, chifukwa chake Satana amazigwiritsa ntchito komanso zimene tingachite kuti tidziteteze.
NKHANI YOPHUNZIRA 4 MASAMBA 24-28
Kodi n’chiyani chingatithandize kukhalabe achangu potumikira Mulungu? Ngati tikufuna kupitirizabe kutsatira Khristu, kodi tiyenera kupewa chizolowezi chiti? Nkhaniyi ikufotokoza mayankho a mafunso ofunika amenewa.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI:
Kodi Mumalola Yehova Kukufunsani Mafunso? 13
Mavuto Amene Takumana Nawo Atithandiza Kudalira Yehova 16
Yehova Amafuna Kuti Mukhale Otetezeka 29