Zamkatimu
March 15, 2011
Magazini Yophunzira
NKHANI ZOPHUNZIRA MILUNGU YA:
May 2-8, 2011
Landirani Mzimu wa Mulungu Osati wa Dziko
TSAMBA 8
May 9-15, 2011
Muzidalira Yehova Pamene Mapeto Akuyandikira
TSAMBA 12
May 16-22, 2011
TSAMBA 24
May 23-29, 2011
Khalanibe Tcheru Ngati Yeremiya
TSAMBA 28
Cholinga cha Nkhani Zophunzira
NKHANI YOPHUNZIRA 1 TSAMBA 8-12
Anthu ambiri amasonyeza mzimu wa dziko ndiye kodi n’zotheka kukhala osiyana nawo? Nkhaniyi itithandiza kuona mmene mzimu wa dziko ungayambire kutitsogolera. Tikambirananso zimene tikuphunzira kwa Yesu pa nkhani yolandira mzimu wa Mulungu.
NKHANI YOPHUNZIRA 2 TSAMBA 12-16
Kodi kudalira Yehova kumatanthauza chiyani? Nkhaniyi itithandiza kuona kuti kudalira Yehova sikumangotanthauza kukhulupirira malonjezo ake onena za dziko latsopano. Kumatanthauzanso kuvomereza ndi mtima wonse njira zake ndiponso mfundo zake, n’kumakana njira ndi mfundo za dzikoli.
NKHANI ZOPHUNZIRA 3, 4 TSAMBA 24-32
M’nkhanizi tidziwa zimene zinathandiza Nowa ndi banja lake, Mose ndiponso Yeremiya kukhalabe tcheru kuti akwaniritse ntchito zimene anapatsidwa. Onsewa adzaona kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Mulungu. Onani zimene mungaphunzire kwa anthu amenewa komanso mtima umene anali nawo.
M’MAGAZINI INO MULINSO NKHANI IZI:
3 Musamadzinyenge ndi Maganizo Onama
6 Mafunso Ochokera kwa Owerenga
17 Zinthu Zimene Mungakondwere Nazo
20 Musasiye Okhulupirira Anzanu